1 Samueli
18 Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula ndi Sauli, Yonatani+ anagwirizana kwambiri+ ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.+ 2 Tsiku limenelo Sauli anatenga Davide, ndipo sanamulole kubwerera kunyumba ya bambo ake.+ 3 Yonatani ndi Davide anachita pangano,+ chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.+ 4 Pamenepo Yonatani anavula malaya ake akunja odula manja ndi kupatsa Davide. Anam’patsanso zovala zina ngakhalenso lupanga, uta ndi lamba wake. 5 Choncho Davide anayamba kupita kunkhondo. Kulikonse kumene Sauli wamutumiza anali kuchita zinthu mwanzeru,+ moti Sauli anamuika kukhala woyang’anira asilikali.+ Zimenezi zinasangalatsa anthu onse komanso atumiki a Sauli.
6 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene asilikali anali kubwerera, Davide atakantha Mfilisiti uja, akazi anayamba kutuluka m’mizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ ndi kuvina. Iwo anali kupita kukachingamira mfumu Sauli mosangalala,+ akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu. 7 Akazi amene anali kusangalalawo anali kuimba molandizana mawu kuti:
“Sauli wakantha adani ake masauzande,
Ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi.”+
8 Sauli atamva zimenezi anakwiya kwambiri+ ndipo mawu amenewa anamuipira, moti anayamba kuganiza kuti: “Davide amupatsa masauzande makumimakumi, koma ine angondipatsa masauzande okha. Ndiye kuti kwangotsala kum’patsa ufumuwu basi!”+ 9 Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyang’ana Davide ndi diso loipa.+
10 Tsiku lotsatira,+ mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa Sauli,+ moti anayamba kuchita zinthu ngati mneneri+ m’nyumba mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kuimba nyimbo+ ngati kale ndipo Sauli anali ndi mkondo m’manja mwake.+ 11 Ndiyeno Sauli anaponya mkondo uja+ ndi kunena kuti: “Ndilasa Davide ndi kumukhomerera kukhoma* ndi mkondowu!”+ Koma Davide anamuthawa, ndipo zimenezi zinachitika kawiri konse.+ 12 Zitatero, Sauli anachita mantha+ ndi Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo,+ koma Sauliyo anali atam’chokera.+ 13 Chotero Sauli anachotsa Davide kuti asamakhale naye pafupi,+ ndipo anamuika kukhala mtsogoleri wa gulu la asilikali 1,000, moti Davide anali kutsogolera asilikali amenewo.+ 14 Davide anali kuchita zinthu mwanzeru+ nthawi zonse m’njira zake zonse, ndipo Yehova anali naye.+ 15 Sauli nayenso anali kuona kuti Davide akuchita zinthu mwanzeru,+ moti anali kuchita naye mantha. 16 Anthu onse a mu Isiraeli ndi Yuda anali kum’konda Davide, chifukwa iye anali kuwatsogolera.
17 Ndiyeno Sauli anauza Davide kuti: “Mwana wanga wamkazi wamkulu Merabu+ alipo. Ndidzakupatsa ameneyu kuti akhale mkazi wako.+ Koma iwe undisonyeze kulimba mtima kwako ndi kumenya nkhondo za Yehova.”+ Mumtima mwake Sauli anati: “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisiti.”+ 18 Koma Davide anayankha Sauli kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?”+ 19 Ndiyeno itafika nthawi yopereka Merabu mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, anali atam’pereka kale kwa Adiriyeli+ Mmeholati+ kuti akhale mkazi wake.
20 Tsopano Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anali kukonda Davide, ndipo anthu anauza Sauli zimenezi. Sauli atamva nkhani imeneyi anasangalala. 21 Chotero Sauli anati: “Ndidzam’patsa Mikala kuti akhale msampha kwa iye,+ ndi kuti Afilisiti amuphe.” Zitatero Sauli anauza Davide kuti: “Lero uchite nane mgwirizano wa ukwati mwa kutenga mmodzi mwa akazi awiriwa.” 22 Kuwonjezera pamenepo, Sauli analamula atumiki ake kuti: “Mukalankhule ndi Davide mwachinsinsi kuti, ‘Mfumutu ikusangalala nawe, ndipo atumiki ake onse akukonda kwambiri. Ndiye chita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu.’” 23 Atumiki a Sauli anapita kukauza Davide mawu amenewa, koma Davide anawayankha kuti: “Kodi mukuona ngati ndi nkhani yaing’ono kuchita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu, pamene ine ndine munthu wosauka+ ndi wonyozeka?”+ 24 Ndiyeno atumikiwo anauza Sauli kuti: “Izi n’zimene Davide anatiyankha.”
25 Pamenepo Sauli anati: “Amuna inu, mukauze Davide kuti, ‘Sikuti mfumu ikufuna ndalama za ukwati,+ koma ikufuna makungu 100 akunsonga + a Afilisiti, kuti ibwezere+ adani ake.’” Koma Sauli anali atakonza chiwembu kuti Davide aphedwe ndi Afilisiti. 26 Choncho atumiki a Sauliwo anauza Davide uthengawo, ndipo Davide anavomera kuchita mgwirizano wa ukwati+ ndi mfumu. Masiku oti apereke makunguwo kwa mfumuyo asanathe, 27 Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+ 28 Sauli anaona ndi kudziwa kuti Yehova ali ndi Davide.+ Ndipo Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, anam’konda kwambiri Davide.+ 29 Apanso Sauli anachita mantha kwambiri ndi Davide, moti anali kudana ndi Davide nthawi zonse.+
30 Ndiyeno akalonga+ a Afilisiti akatuluka kudzamenya nkhondo, Davide anali kuchita zinthu mwanzeru kwambiri+ mwa atumiki onse a Sauli, moti dzina la Davide linatchuka kwambiri.+