Miyambo
6 Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+ ngati wagwirana chanza ndi mlendo pochita mgwirizano,+ 2 ngati wakodwa ndi mawu a m’kamwa mwako,+ ngati wagwidwa ndi mawu a m’kamwa mwako, 3 uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse, pakuti wagwa m’manja mwa mnzako:+ Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+ 4 Maso ako asapeze tulo, ndipo maso ako owala asagone.+ 5 Dzipulumutse ngati insa m’manja mwa wosaka, ndiponso ngati mbalame m’manja mwa wosaka mbalame.+
6 Pita kwa nyerere+ waulesi iwe,+ ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru. 7 Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira, 8 imakonza chakudya chake m’chilimwe.+ Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola. 9 Kodi ugonabe mpaka liti, waulesiwe?+ Udzuka nthawi yanji kutulo tako?+ 10 Ukapitiriza kugona pang’ono, ukapitiriza katulo pang’ono, ukapitiriza kupinda manja pang’ono pogona,+ 11 umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,+ ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+
12 Munthu wopanda pake,+ wochita zopweteka anzake, amayenda ndi mawu opotoka.+ 13 Amatsinzinira ena ndi diso lake,+ amapanga zizindikiro ndi phazi lake, ndiponso amapanga zizindikiro ndi zala zake.+ 14 Mumtima mwake muli zopotoka.+ Nthawi zonse amakhala akukonza zoipa.+ Amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15 N’chifukwa chake tsoka lake lidzabwere mwadzidzidzi.+ Adzathyoledwa modzidzimutsa, ndipo sadzachira.+
16 Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.+ Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo:+ 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+ 18 mtima wokonzera ena ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa,+ 19 mboni yachinyengo yonena mabodza,+ ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.+
20 Mwana wanga, sunga lamulo la bambo ako,+ ndipo usasiye malangizo a mayi ako.+ 21 Ulimange pamtima pako nthawi zonse+ ndipo ulimange m’khosi mwako.+ 22 Lidzakutsogolera ukamayenda,+ lidzakulondera ukamagona,+ ndipo ukadzuka, lidzakusamalira. 23 Pakuti lamulolo ndilo nyale,+ ndipo malangizo ndiwo kuwala,+ komanso kudzudzula* kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo,+ 24 kuti kukuteteze kwa mkazi woipa,+ komanso ku lilime losalala la mkazi wachilendo.+ 25 Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+ Asakukope ndi maso ake owala,+ 26 pakuti munthu amafika potsala ndi mkate wozungulira umodzi wokha chifukwa cha hule,+ koma mkazi wamwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.+ 27 Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28 Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29 N’chimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.+ Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+ 30 Anthu sanyoza munthu wakuba, akaba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31 Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7. Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake.+ 32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru mumtima mwake.+ Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.+ 33 Adzapeza tsoka ndi manyazi,+ ndipo kunyozeka kwake sikudzafufutika.+ 34 Pakuti nsanje ya mwamuna imautsa mkwiyo wake,+ ndipo sadzamva chisoni pa tsiku lobwezera.+ 35 Iye sadzavomera dipo* lamtundu uliwonse, ndipo sadzalola ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.