Masalimo
BUKU LACHITATU
(Masalimo 73 – 89)
Nyimbo ya Asafu.+
73 Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+
2 Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka,+
Mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.+
5 Iwo sakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo,+
Ndipo sakumana ndi masoka mofanana ndi anthu ena onse.+
9 Kudzikweza kwawo kwafika kumwamba,+
Akuyendayenda padziko lapansi ndipo lilime lawo likunena zilizonse zimene akufuna.+
10 Choncho woipa amatengera anthu a Mulungu kumalo omwewo,
Ndipo amamwa madzi m’kapu yodzaza bwino.
12 Onani! Awa ndi anthu oipa, amene akukhala mosatekeseka mpaka kalekale.+
Iwo achulukitsa chuma chawo.+
13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,+
Ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.+
15 Ngati ndikananena kuti: “Ndidzalankhula za zinthu zimenezi,”
Pamenepo ndikanachitira chinyengo
M’badwo wa ana anu aamuna.+
16 Ndipo ndinali kuganizira nkhani imeneyi kuti ndiimvetse.+
Zinali zopweteka kwa ine,
17 Kufikira pamene ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.+
Ndinafuna kudziwa za tsogolo lawo.+
19 Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+
Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa!
20 Inu Yehova, anthu amenewa ali ngati maloto amene aiwalika podzuka.+
Choncho pamene mukuimirira mudzawakana mochititsa manyazi.+
21 Pakuti mtima unandipweteka+
Ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.+
22 Ndinakhala wopanda nzeru ndipo sindinadziwe kanthu.+
Ndinakhala ngati nyama yakuthengo pamaso panu.+
25 Winanso ndani kumwambako amene ali kumbali yanga?+
Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.+
26 Thupi langa ndi mtima wanga zalefuka.+
Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+