Hoseya
5 “Imvani inu ansembe+ ndipo mvetserani inu a m’nyumba ya Isiraeli. Inunso a m’nyumba ya mfumu+ mvetserani, pakuti chiweruzochi chikukhudza inuyo, chifukwa mwakhala msampha+ ku Mizipa ndipo mwakhala ngati ukonde paphiri la Tabori.+ 2 Pakuti anthu amene andipandukira apha anthu ambiri,+ ngakhale kuti ine ndakhala ndikuwachenjeza onsewo.+ 3 Inetu ndimamudziwa bwino Efuraimu+ ndipo Isiraeli si wobisika kwa ine.+ Iwe Efuraimu ukuchita zachiwerewere ndi akazi+ ndipo Isiraeli wadziipitsa.+ 4 Zochita zawo zikuwalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo+ chifukwa iwo ali ndi mtima wadama+ ndipo akana kudziwa Yehova.+ 5 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+ ndipo Isiraeli ndi Efuraimu apunthwa ndi zochita zawo.+ Nayenso Yuda wapunthwa pamodzi nawo.+ 6 Iwo anapita kukafunafuna Yehova ali ndi nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, koma sanamupeze+ chifukwa anali atawachokera. 7 Achitira Yehova zinthu zachinyengo,+ chifukwa abereka ana achilendo.+ Tsopano pomatha mwezi, iwo adzakhala atadyedwa limodzi ndi zinthu zawo.+
8 “Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa+ ku Gibeya!+ Lizani lipenga ku Rama! Fuulani mfuu ya nkhondo ku Beti-aveni!+ Tili pambuyo pako, iwe Benjamini!+ 9 Iwe Efuraimu, udzakhala chinthu chodabwitsa pa tsiku lako lolangidwa.+ Inetu ndauza mafuko a Isiraeli zinthu zoona zimene zidzawachitikira.+ 10 Akalonga a Yuda akhala ngati anthu osuntha malire.+ Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi. 11 Efuraimu waponderezedwa. Akusautsidwa moyenereradi,+ chifukwa anatsatira dala mdani wake.+ 12 Ine ndinali ngati njenjete*+ kwa Efuraimu, ndiponso ndinachititsa kuti nyumba ya Yuda iwole.
13 “Efuraimu anaona kudwala kwake ndipo Yuda anaona chilonda chake.+ Pamenepo Efuraimu anapita ku Asuri+ ndipo anatumiza amithenga kwa mfumu yaikulu.+ Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani anthu inu,+ ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.+ 14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu+ ndiponso ngati mkango wamphongo kwa nyumba ya Yuda. Ineyo ndidzawakhadzulakhadzula ndekha ndi kuwataya ndipo sipadzakhala wowalanditsa.+ 15 Kenako ndidzabwerera kumalo anga kufikira iwo atalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo+ ndipo adzayamba kufunafuna nkhope yanga.+ Zinthu zikadzawavuta,+ adzandifuna.”+