2 Akorinto
2 Ndasankha mumtima mwanga kuti pobweranso kwa inu ndisadzakhalenso wachisoni.+ 2 Pakuti ngati ndingakuchititseni kumva chisoni,+ adzandisangalatsa ndani kupatulapo amene ndawachititsa kumva chisoniwo? 3 N’chifukwa chake ndinalemba zimenezi, kuti ndikadzabwera kumeneko, ndisadzakhale wachisoni+ chifukwa cha anthu amene ndiyenera kusangalala nawo.+ Pakuti ndili ndi chikhulupiriro+ mwa nonsenu kuti chimwemwe chimene ndili nacho ndi chimenenso nonsenu muli nacho. 4 Inetu ndinakulemberani kalata ija ndikusautsika ndi kuzunzika kwambiri mumtima, pamodzi ndi misozi yambiri,+ osati kuti muchite chisoni,+ koma kuti mudziwe chikondi chimene ndili nacho makamaka pa inu.
5 Ngati wina wachita kanthu kochititsa chisoni,+ sanachititse chisoni ineyo, koma mwanjira ina wachititsa chisoni nonsenu. Komabe sindikufuna kutsindika mfundo imeneyi mwamphamvu kwambiri. 6 Kudzudzulidwa+ ndi anthu ambiri chonchi n’kokwanira kwa munthu ameneyu. 7 Chotero tsopano mukhululukireni ndi mtima wonse+ ndi kumutonthoza, kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire.+ 8 Choncho ndikukudandaulirani kuti mumutsimikizire kuti mumamukonda.+ 9 Pakuti ndikulemba zimenezi pofuna kudziwa ngati mulidi omvera m’zinthu zonse.+ 10 Chilichonse chimene mwakhululukira munthu ndi mtima wonse, inenso ndimukhululukira chimodzimodzi.+ Ndipo chilichonse chimene ineyo ndakhululukira munthu ndi mtima wonse, ngati chilipo chimene ndakhululuka ndi mtima wonse, ndachita zimenezo chifukwa cha inuyo, pamaso pa Khristu, 11 kuti Satana asatichenjerere,+ pakuti tikudziwa bwino ziwembu zake.+
12 Nditafika ku Torowa+ kukalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, ndipo mwayi wina utanditsegukira mu ntchito ya Ambuye,+ 13 mtima wanga sunakhazikike chifukwa Tito+ m’bale wanga sindinamupeze. Ndiye ndinatsanzikana ndi abale kumeneko, n’kupita ku Makedoniya.+
14 Koma tiyamike Mulungu amene nthawi zonse amatitsogolera+ pamodzi ndi Khristu ngati kuti tikuguba pa chionetsero chonyadirira kupambana.+ Kudziwa Mulungu kuli ngati fungo lonunkhira bwino ndipo kudzera mu ntchito yathu fungoli likufalikira paliponse.+ 15 Pakuti pamaso pa Mulungu ndife fungo lonunkhira bwino+ lonena za uthenga wa Khristu, limene likumvedwa ndi anthu amene akupita kukapulumuka komanso ndi amene akupita kukawonongedwa.+ 16 Kwa amene akupita kukawonongedwawo ndife fungo lochokera ku imfa kupita ku imfa,+ koma kwa amene akupita kukapulumukawo ndife fungo lochokera ku moyo kupita ku moyo. Ndipo ndani ali woyenerera kugwira ntchito imeneyi?+ 17 Ifeyo ndife oyenerera. Pakuti mawu a Mulungu sitichita nawo malonda+ ngati mmene ambiri akuchitira,+ koma timalankhula moona mtima monga otsatira Khristu, okhala pamaso pa Mulungu, komanso ngati anthu amene atumidwa ndi Mulungu.+