27 Tsopano Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo+ kuti:
2 “Pali Mulungu wamoyo+ amene wandimana chilungamo,+
Ndiponso pali Wamphamvuyonse wamoyo amene wachititsa moyo wanga kupweteka,+
3 Pamene mpweya wanga udakali wonse mwa ine,
Ndiponso pamene mzimu wa Mulungu udakali m’mphuno mwanga,+
4 Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,
Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.
5 Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama.+
Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.+
6 Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya.+
Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.+
7 Mdani wanga akhale munthu woipa m’zonse,+
Ndipo wondiukira akhaledi wochita zoipa.
8 Kodi chiyembekezo cha wampatuko n’chiyani Mulungu akachotsa moyo wake,+
Akamulanda moyo wake?+
9 Kodi Mulungu angamumvere kulira kwake
Zowawa zikamugwera?+
10 Kodi iye angasangalale ndi Wamphamvuyonse?
Kodi angapemphere kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Ndikuphunzitsani ndi thandizo la Mulungu amuna inu.
Sindibisa maganizo a Wamphamvuyonse.+
12 Nonsenutu mwaona masomphenya.
Nanga n’chifukwa chiyani mukuoneka kuti ndinu opanda nzeru?+
13 Gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+
Zomwe adzalandire kwa Wamphamvuyonse monga cholowa cha ozunza anzawo, ndi izi:
14 Ana ake akachuluka, amachulukira lupanga.+
Mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira.
15 Opulumuka ake adzaikidwa m’manda pa nthawi ya mliri wakupha,
Ndipo akazi awo amasiye sadzalira.+
16 Iye akaunjika siliva ngati fumbi,
Ndipo akakonza zovala zake ngati dothi,
17 Ngakhale akonze zovalazo, wolungama ndi amene adzazivale.+
Ndipo silivayo, wosalakwa ndi amene adzam’tenge.
18 Iye wamanga nyumba yake ngati kadziwotche,
Ndiponso ngati chisimba+ chimene mlonda wamanga.
19 Adzagona ali wolemera, koma palibe chimene chidzasonkhanitsidwe.
Adzatsegula maso ake, koma sipadzakhala kalikonse.+
20 Zoopsa zadzidzidzi zidzam’tenga ngati madzi.+
Usiku chimphepo chamkuntho chidzamuba ndithu.
21 Mphepo ya kum’mawa idzamunyamula n’kumusowetsa,+
Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+
22 Idzamukuntha, ndipo sidzamumvera chisoni.+
Adzayesera kuthawa mphamvu ya mphepoyo koma sadzatha.+
23 Anthu adzamuwombera m’manja monyoza.+
Ndipo adzamuimbira mluzu+ ali pamalo pake.