Agalatiya
4 Tsopano ndikuuzeni kuti, wolandira cholowa akakhala kamwana, iye sasiyana konse ndi kapolo,+ ngakhale ali mwini zinthu zonse. 2 Amakhalabe pansi pa amuna oyang’anira ana+ ndiponso anthu oyang’anira zinthu za mbuye wawo, kufikira tsiku limene bambo ake anaikiratu. 3 N’chimodzimodzinso ifeyo. Pamene tinali tiana, tinali akapolo a mfundo zachibwanabwana+ zimene anthu a m’dzikoli amayendera. 4 Koma nthawi itakwana,+ Mulungu anatumiza Mwana wake,+ amene anadzabadwa kwa mkazi+ ndipo anadzakhala pansi pa chilamulo.+ 5 Zinatero kuti amasule anthu okhala pansi pa chilamulo mwa kuwagula,+ kutinso Mulungu atitenge ife kukhala ana ake.+
6 Tsopano pakuti ndinu ana ake, Mulunguyo watitumizira mzimu+ wa Mwana wake m’mitima yathu ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+ 7 Chotero si iwenso kapolo, koma mwana ndipo ngati uli mwana, ndiwenso wolandira cholowa kudzera mwa Mulungu.+
8 Ngakhale zili choncho, pamene munali osadziwa Mulungu,+ munali akapolo a zinthu zimene mwachilengedwe si milungu.+ 9 Koma tsopano pamene mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziwidwa ndi Mulungu,+ mukubwereranso bwanji ku mfundo zachibwanabwana,+ zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake,+ n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?+ 10 Mukusunga mwakhama masiku,+ miyezi,+ nyengo ndi zaka. 11 Ndikuda nkhawa, kuti mwina ntchito imene ndaigwira pa inu ipita pachabe.+
12 Ndikukupemphani abale anga, khalani monga ine+ chifukwa inenso ndinali ngati inuyo kale.+ Simunandilakwire ayi.+ 13 Koma mukudziwa kuti nthawi yoyamba imene ndinalengeza uthenga wabwino kwa inu chifukwa chakuti ndinali kudwala,+ 14 inuyo simunanyansidwe ndi matenda anga, amene anali mayesero kwa inu, ndipo simunalavule malovu ponyansidwa nawo, koma munandilandira ngati mngelo+ wa Mulungu, ngati Khristu Yesu.+ 15 Chili kuti nanga chimwemwe chimene munali nacho poyamba chija?+ Pakuti ndikunenetsa kuti, zikanakhala zotheka, mukanakolowola maso anu n’kundipatsa.+ 16 Kodi ndakhala mdani+ wanu tsopano chifukwa ndakuuzani zoona?+ 17 Anthu ena akuyesetsa kwambiri kuti akukopereni kwa iwowo,+ osati ndi zolinga zabwino, koma kuti akutsekerezeni kuti musabwere kwa ine, kuti inuyo muyesetse kuwatsatira.+ 18 Ngati munthu akukufunani kwambiri pa chifukwa chabwino, n’zabwino kwa inu.+ Zimenezi zikachitika osati pa nthawi imene ine ndili nanu limodzi yokha,+ komanso nthawi zonse, 19 ndiye kuti n’zabwino kwa inu ana anga.+ Ine ndayambanso kumva zopweteka zimene ndinamva pokuberekani, mpaka Khristu adzakhazikike mwa inu.+ 20 Panopa ndikanakonda kukhala pakati panu+ kuti ndilankhule mosiyanako, chifukwa mwandithetsa nzeru.+
21 Tandiuzani, inu amene mukufuna kutsatira chilamulo,+ Kodi simukumva zimene Chilamulocho chikunena?+ 22 Mwachitsanzo, Malemba amati Abulahamu anabereka ana aamuna awiri, wina kwa mdzakazi*+ ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu.+ 23 Koma mwana amene anabadwa kwa mdzakazi uja anabadwa monga mmene ana onse amabadwira,+ pamene mwana winayo amene anabadwa kwa mkazi amene anali mfulu anabadwa mwa lonjezo.+ 24 Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira,+ pakuti azimayi amenewa akuimira mapangano awiri.+ Loyamba ndi pangano la paphiri la Sinai,+ limene limabereka ana oti akhale akapolo. Pangano limenelo ndiye Hagara uja. 25 Tsopano, Hagara ameneyu akutanthauza Sinai,+ phiri la ku Arabiya, ndipo masiku ano akufanana ndi Yerusalemu, pakuti ali mu ukapolo+ pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu+ wam’mwamba ndi mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.+
27 Pakuti Malemba amati: “Kondwera, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Kuwa ndipo fuula mokondwa, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+ 28 Tsopano ifeyo abale, ndife ana a lonjezo monga mmene analili Isaki.+ 29 Koma monga mmene zinalili pa nthawiyo, kuti wobadwa monga mmene ana onse amabadwira anayamba kuzunza+ wobadwa mwa mzimu, ndi mmenenso zilili masiku ano.+ 30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, pakuti sizingatheke mwana wa mdzakazi kudzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi waufulu.”+ 31 Chotero abale, ife ndife ana a mkazi waufulu,+ osati a mdzakazi.+