-
Mateyu 21:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Kenako Yesu analowa mʼkachisi nʼkuthamangitsa anthu onse amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 13 Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”+
-
-
Maliko 11:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Tsopano iwo anafika ku Yerusalemu. Kumeneko analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuthamangitsa anthu amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 16 Iye sanalole aliyense kuti adutse mʼkachisimo atanyamula katundu. 17 Iye ankaphunzitsa ndipo ankauza anthuwo kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonseʼ?+ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+
-
-
Yohane 2:13-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tsopano Pasika+ wa Ayuda anali atayandikira, choncho Yesu ananyamuka nʼkupita ku Yerusalemu. 14 Kumeneko anapeza ogulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda+ komanso osintha ndalama ali mʼkachisi atakhala mʼmipando yawo. 15 Choncho anapanga chikwapu chazingwe nʼkuthamangitsa onse amene anali ndi nkhosa komanso ngʼombe mʼkachisimo. Anakhuthula makobidi a anthu osintha ndalama nʼkugubuduza matebulo awo.+ 16 Ndiyeno anauza ogulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno! Musiyiretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”*+ 17 Ophunzira ake anakumbukira zimene Malemba amanena kuti: “Kudzipereka kwanga panyumba yanu kudzakhala ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga.”+
-