Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 51:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+

      Fufutani zolakwa zanga mogwirizana ndi chifundo chanu chachikulu.+

  • Salimo 103:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa,

      Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.+

  • Yesaya 1:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova wanena kuti: “Bwerani tsopano, tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+

      Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri,

      Adzayera kwambiri.+

      Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi,

      Adzayera ngati thonje.

  • Yesaya 43:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ineyo ndi amene ndikufafaniza zolakwa zako*+ chifukwa cha dzina langa,+

      Ndipo machimo ako sindidzawakumbukira.+

  • Yeremiya 33:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndidzawayeretsa ku zolakwa zonse zimene anandichimwira+ ndipo ndidzawakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nʼkuphwanya nazo malamulo anga.+

  • Machitidwe 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Choncho lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.*

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena