Kalata Yoyamba kwa Timoteyo
1 Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu molamulidwa ndi Mulungu+ Mpulumutsi wathu,+ ndi Khristu Yesu yemwe ali chiyembekezo chathu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo,+ mwana wanga weniweni+ m’chikhulupiriro:
Kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu, zikhale nawe.+
3 Paja nditatsala pang’ono kupita ku Makedoniya, ndinakulimbikitsa kuti ukhalebe ku Efeso.+ Ndikukulimbikitsanso kuti ukhalebe komweko, uletse+ anthu ena ake kuti asaphunzitse chiphunzitso chosiyana ndi chathu,+ 4 ndiponso kuti asamamvere nkhani zonama+ ndi kukumbana mibadwo ya makolo. Zimenezi n’zosapindulitsa,+ koma zimangoyambitsa mafunso ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro. 5 Ndithu, cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi+ chochokera mumtima woyera,+ m’chikumbumtima chabwino,+ ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.+ 6 Anthu ena akana kutsatira zimenezi ndipo asocheretsedwa+ n’kuyamba kutsatira nkhani zopanda pake.+ 7 Amenewa amafuna kukhala aphunzitsi+ a chilamulo+ koma sazindikira zimene akunena kapena mfundo zimene akuzilimbikira.
8 Tikudziwa kuti Chilamulo n’chabwino+ ngati munthu akuchigwiritsa ntchito moyenera.+ 9 Zili choncho podziwa mfundo iyi yakuti, lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ osalamulirika,+ osaopa Mulungu, ochimwa, osakoma mtima,*+ onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu, 10 adama,+ amuna ogonana ndi amuna anzawo, oba anthu, onama, olumbira monama,+ ndiponso ochita china chilichonse chosagwirizana+ ndi chiphunzitso cholondola.+ 11 Chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero umene anauika m’manja mwanga,+ wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.+
12 Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika,+ ndipo anandipatsa utumiki.+ 13 Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake+ ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo+ chifukwa ndinali wosadziwa+ ndi wopanda chikhulupiriro. 14 Koma ndinalandira kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu. Ndinalandiranso chikhulupiriro ndi chikondi chodzera mwa Khristu Yesu.+ 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse.+ Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+ 16 Komabe, anandichitira chifundo+ kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa kwambiri, kuti chikhale chitsanzo kwa amene adzamukhulupirire+ n’cholinga chakuti adzapeze moyo wosatha.+
17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukulamulira+ kuchita izi malinga ndi maulosi+ amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+ 19 Ukhale ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino+ chimene ena achikankhira kumbali,+ moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.+ 20 Ena mwa amenewa ndi Hemenayo+ ndi Alekizanda,+ ndipo ndawapereka kwa Satana+ kuti akalangidwa,* aphunzire kuti sayenera kulankhula zonyoza Mulungu.+
2 Choncho, poyamba ndikuchonderera nonse kuti muzipereka mapembedzero kwa Mulungu, muzipereka mapemphero,+ muzipemphererana, ndipo muzipereka mapemphero oyamika Mulungu m’malo mwa anthu onse, kaya akhale a mtundu wotani.+ 2 Muchite zimenezi m’malo mwa mafumu+ ndi m’malo mwa anthu onse apamwamba,+ kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso tikhale oganiza bwino.+ 3 Zimenezi ndi zabwino ndiponso ndi zovomerezeka+ kwa Mpulumutsi wathu Mulungu,+ 4 amene chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani,+ apulumuke+ ndi kukhala odziwa choonadi+ molondola.+ 5 Pakuti pali Mulungu mmodzi+ ndi mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu+ ndi anthu.+ Ameneyo ndiye munthuyo Khristu Yesu.+ 6 Iye anadzipereka kuti akhale dipo* lokwanira ndendende m’malo mwa onse.+ Zimenezi ndi zimene adzazichitire umboni pa nthawi zake. 7 Chifukwa cha umboni umenewu,+ ine ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki ndi mtumwi.+ Ndikunenatu zoona,+ sindikunama ayi. Ndinasankhidwa kuti ndikhale mphunzitsi wophunzitsa anthu a mitundu ina+ za chikhulupiriro+ ndi choonadi.
8 Choncho, ndikufuna kuti kulikonse amuna apitirize kupemphera, kukweza m’mwamba manja awo oyera+ popanda kukwiyirana+ ndi kutsutsana.+ 9 Mofanana ndi zimenezi, ndikufunanso kuti akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu+ ndi mwanzeru, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.+ 10 Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.+ Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino.+
11 Pophunzira, mkazi azikhala chete ndipo azikhala wogonjera ndi mtima wonse.+ 12 Sindikuvomereza kuti mkazi aziphunzitsa+ kapena kukhala ndi ulamuliro pa mwamuna,+ koma azikhala chete. 13 Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.+ 14 Komanso, Adamu sananyengedwe,+ koma mkaziyo ndiye amene ananyengedwa+ ndipo anachimwa.+ 15 Komabe, mkazi adzatetezeka mwa kubereka ana,+ malinga ngati akupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro, chikondi, ndi kukhala woyera ndiponso woganiza bwino.+
Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira,+ akufuna ntchito yabwino. 2 Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire,+ woganiza bwino,+ wadongosolo,+ wochereza alendo,+ ndiponso wotha kuphunzitsa.+ 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,*+ kapena wandewu,+ koma wololera.+ Asakhale waukali,+ kapena wokonda ndalama.+ 4 Akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake+ ndiponso akhale woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+ 5 (Ndithudi, ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) 6 Asakhale wotembenuka kumene,+ kuopera kuti angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada,+ n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira.+ 7 Komanso, akhale woti ngakhale anthu akunja* akumuchitira umboni wabwino,+ kuti asatonzedwe ndi kukodwa mumsampha+ wa Mdyerekezi.
8 Nawonso atumiki othandiza+ akhale opanda chibwana, osanena pawiri, osakonda kumwa vinyo wambiri, ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 9 Akhale ogwira chikhulupiriro mwamphamvu, chimene ndi chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, ali ndi chikumbumtima choyera.+
10 Ndiponso, amenewa ayesedwe+ kaye ngati ali oyenerera, ndiyeno atumikire monga atumiki, popeza ndi opanda chifukwa chowanenezera.+
11 Nawonso amayi akhale opanda chibwana, osati amiseche.+ Akhale ochita zinthu mosapitirira malire,+ ndi okhulupirika m’zinthu zonse.+
12 Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi,+ oyang’anira bwino ana awo ndi mabanja awo.+ 13 Pakuti amuna otumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino+ ndi ufulu waukulu wa kulankhula+ za chikhulupiriro, mwa Khristu Yesu.
14 Ndikukulembera zimenezi, ngakhale kuti ndikuyembekezera kuti ndibwera kwa iwe posachedwapa.+ 15 Koma ngati ndingachedwe, ndalemba izi kuti udziwe mmene uyenera kuchitira m’nyumba ya Mulungu,+ imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi umene umalimbikitsa ndi kuteteza+ choonadi. 16 Ndithudi, chinsinsi chopatulikachi+ chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu n’chachikulu ndithu: ‘Iye anaonekera ngati munthu,+ anaonedwa kuti ndi wolungama pamene anali mzimu,+ anaonekera kwa angelo,+ analalikidwa kwa mitundu ya anthu,+ anthu padziko lapansi anamukhulupirira,+ ndiponso analandiridwa kumwamba mu ulemerero.’+
4 Komabe, mawu ouziridwa amanenadi kuti m’nthawi zam’tsogolo,+ ena adzagwa+ pa chikhulupiriro, chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso ziphunzitso za ziwanda.+ 2 Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera+ chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto. 3 Anthu amenewo adzaletsa anthu kukwatira,+ ndipo adzalamula anthu kusala zakudya zina+ zimene Mulungu anazilenga+ kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro ndiponso odziwa choonadi molondola azidya moyamikira.+ 4 Ndikutero chifukwa chakuti chilichonse cholengedwa ndi Mulungu n’chabwino,+ ndipo palibe chimene chiyenera kukanidwa+ ngati chalandiridwa moyamikira,+ 5 pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndiponso pemphero.
6 Chifukwa chopereka malangizo awa kwa abale, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu. Ndipo udzakula bwino ndi mawu a chikhulupiriro ndiponso chiphunzitso chabwino+ chimene wachitsatira mosamala.+ 7 Koma uzipewa nkhani zonama+ zimene zimaipitsa zinthu zoyera ndi zimene amayi okalamba amakamba. M’malomwake, ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.+ 8 Pakuti kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ n’kopindulitsa m’zonse,+ chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwerawo.+ 9 Mawu amenewa ndi oona ndipo ndi oyenera kuwalandira ndi mtima wonse.+ 10 Pa chifukwa chimenechi, tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo+ chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi+ wa anthu a mtundu uliwonse,+ koma makamaka okhulupirika.+
11 Pitiriza kuwaphunzitsa+ ndi kuwalamula kuti azichita zimenezi.+ 12 Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono.+ M’malomwake, ukhale chitsanzo+ kwa okhulupirika+ m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.+ 13 Pamene ukundiyembekezera, pitiriza kukhala wodzipereka powerenga+ pamaso pa anthu,+ powadandaulira, ndi powaphunzitsa. 14 Usamanyalanyaze mphatso+ imene uli nayo, yomwe unapatsidwa mwaulosi+ ndiponso pamene bungwe la akulu linaika manja+ pa iwe. 15 Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.+ Dzipereke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.+ 16 Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita+ komanso zimene umaphunzitsa.+ Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.+
5 Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa,+ koma umudandaulire ngati bambo ako. Amuna achinyamata uwadandaulire ngati abale ako, 2 ndipo akazi achikulire+ ngati amayi ako. Akazi achitsikana uwadandaulire ngati alongo ako,+ ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa.
3 Lemekeza akazi amasiye amene alidi amasiye.+ 4 Koma ngati mkazi wamasiye aliyense ali ndi ana kapena adzukulu, amenewo aphunzire kukhala odzipereka kwa Mulungu m’banja mwawo choyamba,+ mwa kubwezera kwa makolo+ ndi agogo awo zowayenerera, pakuti zimenezi zimakondweretsa Mulungu.+ 5 Mkazi amene alidi wamasiye, amene akusowa womusamala,+ amadalira Mulungu+ ndipo amalimbikira mapembedzero ndi mapemphero usiku ndi usana.+ 6 Koma amene amatsatira zilakolako zake kuti azikhutiritse,+ ndi wakufa+ ngakhale kuti ali ndi moyo. 7 Choncho, uziwapatsa malamulo amenewa+ nthawi zonse kuti asakhale ndi chifukwa chowanenezera.+ 8 Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira,+ makamaka a m’banja lake,+ wakana+ chikhulupiriro+ ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.
9 Mkazi wamasiye wolembedwa pamndandanda wa akazi amasiye, akhale wazaka zoposa 60. Akhale amene anali wokhulupirika kwa mwamuna wake,*+ 10 wodziwika kuti anachita ntchito zabwino,+ analera bwino ana,+ anali kuchereza alendo,+ anasambitsa mapazi a oyera,+ anathandiza ena m’masautso,+ ndiponso anali kugwira mwakhama ntchito iliyonse yabwino.+
11 Koma usalole kuika akazi amasiye achitsikana pamndandanda umenewu, pakuti chilakolako chawo chofuna mwamuna chikaima pakati pa iwo ndi Khristu,+ amafuna kukwatiwa. 12 Zikatero, amapezeka olakwa chifukwa sanasunge chikhulupiriro chimene anasonyeza poyamba.+ 13 Komanso pa nthawi yomweyo, amayamba chizolowezi chomangokhala osachita kanthu, n’kumangoyendayenda m’makomo mwa anzawo. Kuwonjezera pa kumangokhala osachita kanthu, amakhalanso amiseche ndi olowerera nkhani za eni,+ n’kumalankhula zimene sayenera kulankhula. 14 Choncho ndimafuna kuti akazi amasiye achitsikana azikwatiwa,+ azibereka ana,+ ndi kusamalira banja, kuti wotsutsa asapeze chifukwa chonenera zachipongwe.+ 15 Ndipotu ena apatutsidwa kale moti ayamba kutsatira Satana. 16 Ngati mkazi aliyense wokhulupirira ali ndi achibale amene ndi akazi amasiye, aziwathandiza,+ kuti akazi amasiyewo asakhale cholemetsa ku mpingo. Zikatero, mpingowo ungathe kuthandiza amene alidi akazi amasiye.+
17 Akulu otsogolera+ bwino apatsidwe ulemu waukulu,+ makamaka amene amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.+ 18 Pakuti lemba limati: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Komanso limati: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.”+ 19 Usavomereze mlandu woneneza mkulu, kupatulapo ngati pali umboni wa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 20 Anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo,+ uwadzudzule+ pamaso pa onse kuti ena onse akhale ndi mantha.+ 21 Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu+ ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda kuweruziratu. Usachite kanthu ndi maganizo okondera.+
22 Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo,*+ kapena kugawana ndi anthu ena machimo awo.+ Pitiriza kukhala ndi khalidwe loyera.+
23 Usamangomwa madzi okha, koma uzimwanso vinyo pang’ono,+ chifukwa cha vuto lako la m’mimba ndi kudwaladwala kwako kuja.
24 Machimo a anthu ena amaonekera poyera,+ ndipo zimenezi zimachititsa kuti aweruzidwe. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pambuyo pake.+ 25 Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera,+ ndipo ngakhale kuti zisaonekere sizingabisike mpaka kalekale.+
6 Onse amene ali m’goli laukapolo, aziona kuti ambuye awo ndi oyenera kuwapatsa ulemu wawo wonse,+ kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitsocho asazinenere zoipa.+ 2 Komanso, akapolo amene ambuye awo ndi okhulupirira,+ asamawapeputse+ chifukwa chakuti ndi abale.+ M’malomwake, akhale akapolo odzipereka kwambiri, pakuti amene akupindula ndi utumiki wawo wabwinowo ndi okhulupirira ndiponso okondedwa.
Pitiriza kuwaphunzitsa ndi kuwadandaulira kuti azichita zimenezi.+ 3 Ngati munthu akuphunzitsa chiphunzitso china,+ ndipo sakuvomereza mawu olondola,+ mawu a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndiponso sakuvomereza chiphunzitso chogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 4 munthu ameneyo ndi wodzitukumula ndiponso wonyada,+ ndipo samvetsa kanthu kalikonse.+ M’malomwake, amakonda kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.+ Zimenezi zimayambitsa kaduka,+ mikangano, kunenerana mawu achipongwe,+ ndiponso kuganizirana zoipa. 5 Zimayambitsanso mapokoso achiwawa pa zinthu zazing’ono pakati pa anthu opotoka maganizo+ ndi osadziwa choonadi,+ poganiza kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi njira yopezera phindu.+ 6 Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo,+ ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.+ 7 Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.+ 8 Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.+
9 Komabe, anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero+ ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru.+ Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.+ 10 Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+
11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+ 12 Menya nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro.+ Gwira mwamphamvu moyo wosatha. Anakuitanira moyo umenewu ndipo unalengeza momveka bwino+ zinthu zokhudzana ndi moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri.
13 Pamaso pa Mulungu, amene amasunga zinthu zonse kuti zikhalebe zamoyo, ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri+ pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula+ 14 kuti usunge lamulolo. Ulisunge uli wopanda banga ndi wopanda chifukwa chokunenezera, kufikira kuonekera+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 15 Wachimwemwe ndi Wamphamvu yekhayo,+ iye amene ali Mfumu+ ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye+ wa olamulira monga ambuye, adzaonekera pa nthawi zake zoikidwiratu.+ 16 Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa,+ amene amakhala m’kuwala kosafikirika.+ Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.+ Iye apatsidwe ulemu+ ndipo mphamvu zake zikhalebe kosatha. Ame.
17 Lamula achuma+ a m’nthawi* ino kuti asakhale odzikweza,+ ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.+ 18 Uwalamule kuti azichita zabwino,+ akhale olemera pa ntchito zabwino,+ owolowa manja, okonzeka kugawira ena,+ 19 ndiponso asunge+ maziko abwino+ a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+
20 Ndithu Timoteyo, sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.+ Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiye “kudziwa zinthu.”+ 21 Pakuti ena apatuka pa chikhulupiriro chifukwa chodzionetsera kuti ndi odziwa zinthu chonchi.+
Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.
Mawu ake enieni, “opanda kukoma mtima kosatha.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “munthu womwa mowa mwauchidakwa amene amakonda kulongolola ndi kuchita ndewu akaledzera.”
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.
Mawu ake enieni, “mkazi wa mwamuna mmodzi.”
Kapena kuti, “kuika manja ako pamunthu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.