Numeri 18:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako. Deuteronomo 14:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Mlevi wokhala mumzinda wanu usamutaye,+ pakuti alibe gawo kapena cholowa monga iwe.+ 2 Mbiri 31:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu okhala mu Yerusalemu kuti apereke gawo loyenera kupita kwa ansembe+ ndi Alevi,+ n’cholinga choti iwo azitsatira+ mosamala chilamulo cha Yehova.+ Nehemiya 10:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akulandira chakhumi.* Aleviwo azipereka gawo limodzi mwa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu+ wathu kuzipinda zodyera+ m’nyumba yosungiramo zinthu. Malaki 3:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Kodi munthu wochokera kufumbi angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.” Inu mukunena kuti: “Takuberani motani?” “Mukundibera kudzera m’chakhumi* ndi m’zopereka.
21 “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako.
4 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu okhala mu Yerusalemu kuti apereke gawo loyenera kupita kwa ansembe+ ndi Alevi,+ n’cholinga choti iwo azitsatira+ mosamala chilamulo cha Yehova.+
38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akulandira chakhumi.* Aleviwo azipereka gawo limodzi mwa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu+ wathu kuzipinda zodyera+ m’nyumba yosungiramo zinthu.
8 “Kodi munthu wochokera kufumbi angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.” Inu mukunena kuti: “Takuberani motani?” “Mukundibera kudzera m’chakhumi* ndi m’zopereka.