-
2 Samueli 14:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mkazi wanzeru.+ Atabwera naye, Yowabu anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene ali panyengo yolira maliro, ndipo uvale zovala za panyengo yolira maliro, komanso usadzole mafuta.+ Ukatero ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa masiku ambiri.+
-
-
2 Samueli 14:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Tsopano banja lonse landiukira ine mtumiki wanu ndipo aliyense akunena kuti, ‘Bweretsa wopha m’bale wakeyo+ kuti timuphe chifukwa cha moyo wa m’bale wake amene anamupha,+ ndipo tiwononge wolandira cholowayo!’ Tsopano anthuwa adzazimitsa makala anga onyeka otsalawo, kuti pasakhale wosunga dzina la mwamuna wanga kapena mbewu yake yotsala padziko lapansi.”+
-