Miyambo
23 Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uzionetsetsa zimene zili pamaso pako,+ 2 ndipo uzidziletsa* ngati uli wadyera.+ 3 Usasonyeze kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma, chifukwa ndi zakudya zachinyengo.+
4 Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.+ Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.+ 5 Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka?+ Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.+
6 Usamadye chakudya cha aliyense womana,+ kapena kusonyeza kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma.+ 7 Pakuti iye ali ngati munthu amene wawerengetsera bwino zinthu mumtima mwake. Amakuuza kuti:+ “Idya, imwa,” koma salankhula ndi mtima wonse.+ 8 Nthongo imene wadya udzaisanza, ndipo mawu ako abwino adzakhala atapita pachabe.+
9 Usalankhule m’makutu mwa munthu wopusa,+ chifukwa iye adzanyoza mawu ako anzeru.+
10 Usasunthire kumbuyo malire akalekale,+ ndipo usalowe m’munda mwa ana amasiye.*+ 11 Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+
12 Bweretsa mtima wako kuti umve malangizo, ndi khutu lako kuti limve mawu a munthu wodziwa zinthu.+
13 Usam’mane chilango* mwana.+ Ngakhale utam’kwapula ndi chikwapu, sangafe ayi. 14 Um’kwapule ndi chikwapu, kuti upulumutse moyo wake ku Manda.+
15 Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,+ ndithu mtima wanga udzasangalala.+ 16 Impso zanga zidzasangalala milomo yako ikamalankhula zowongoka.+
17 Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+ koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+ 18 Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+ ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+
19 Iwe mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru, ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino.+
20 Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri,+ ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka.+ 21 Chifukwa chidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka,+ ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.+
22 Mvera bambo ako amene anakubereka,+ ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ 23 Gula choonadi+ ndipo usachigulitse. Gula nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.+ 24 Bambo wa munthu wolungama ndithu adzasangalala.+ Bambo wobereka mwana wanzeru adzakondwera naye.+ 25 Bambo ako ndi mayi ako adzakondwera, ndipo mayi amene anakubereka adzasangalala.+
26 Mwana wanga, ndipatse mtima wako, ndipo maso ako asangalale ndi njira zanga.+ 27 Pakuti hule lili ngati dzenje lakuya,+ ndipo mkazi wachilendo ali ngati chitsime chopapatiza. 28 Ndithudi iye mofanana ndi wachifwamba,+ amabisalira anthu panjira, ndipo amachulukitsa amuna achinyengo.+
29 Ndani ali ndi tsoka? Ndani sakhazikika maganizo? Ndani ali pa mikangano?+ Ndani ali ndi nkhawa? Ndani ali ndi zilonda popanda chifukwa? Ndani ali ndi maso ofiira? 30 Ndi anthu amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo,+ amene amabwera kudzafunafuna vinyo wosakaniza.+ 31 Usayang’ane vinyo akamaoneka wofiira, akamanyezimira m’kapu, akamatsetserekera kukhosi mwamyaa! 32 Kumapeto kwake amaluma ngati njoka,+ ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri.+ 33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo, ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota.+ 34 Ndithu udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja, komanso ngati munthu amene wagona pamwamba pa mlongoti wa ngalawa.+ 35 Udzati: “Andimenya koma sindinavulale, andikuntha koma sindinadziwe. Kodi ndidzuka nthawi yanji+ kuti ndikamwenso wina?”+