Yobu
10 “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.+
Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga.
Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.
2 Ndimuuza Mulungu kuti, ‘Musanene kuti ndine woipa.
Ndiuzeni chifukwa chimene mukulimbanirana nane.
3 Kodi ndi bwino kuti inuyo muchite zoipa,+
Kuti mukane chinthu chimene manja anu anagwira ntchito mwamphamvu pochipanga,+
Ndiponso kuti muvomereze malangizo a anthu oipa?
5 Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,+
Kapena kodi zaka zanu zili ngati masiku a mwamuna wamphamvu,
6 Kuti muyese kupeza cholakwa changa,
Ndi kuti muzifunafuna tchimo langa?+
8 Manja anu omwe ndi amene anandiumba, ndipo anandipanga+
Kuzungulira thupi langa lonse, koma tsopano mukufuna kundimeza.
12 Mwandipatsa moyo ndi kundisonyeza kukoma mtima kosatha,+
Ndipo mwa kundisamalira+ mumateteza moyo wanga.
13 Zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu.
Ndikudziwa bwino kuti zinthu zimenezi zili ndi inu.
14 Ngati ndachimwa ndipo inu mwaona zonsezo,+
Ndiponso simunandikhululukire zolakwa zanga,+
15 Ngati ndine wolakwa, tsoka kwa ine!+
Ngati ndine wosalakwa, ndisadzutse mutu wanga.+
Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.+
16 Mutu wanga ukadzikweza,+ mudzandisaka ngati kuti ndinu mkango wamphamvu,+
Ndipo mudzandichitira chinthu chinanso chodabwitsa.
17 Mudzabweretsa mboni zanu zatsopano pamaso panga,
Ndipo mudzakulitsa mkwiyo wanu pa ine.
Mavuto anga akungotsatizanatsatizana.