Deuteronomo
14 “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu.+ Musamadzichekecheke+ kapena kumeta+ nsidze* zanu chifukwa cha anthu akufa. 2 Pakuti ndinu anthu oyera+ kwa Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova wakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera,+ mwa anthu onse okhala padziko lapansi.
3 “Musadye chinthu chilichonse chonyansa.+ 4 Mitundu ya nyama zimene muyenera kudya ndi izi:+ ng’ombe, nkhosa, mbuzi, 5 mbawala yamphongo, insa, ngondo,+ mbuzi yakuthengo, mphalapala, nkhosa yakuthengo ndi chinkhoma. 6 Nyama iliyonse ya ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati imenenso imabzikula,+ imeneyo mungadye. 7 Simuyenera kudya mitundu iyi yokha mwa nyama zonse zimene zimabzikula kapena zokhala ndi ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati: ngamila,+ kalulu+ ndi mbira,+ chifukwa zimabzikula koma si zogawanika ziboda. Nyama zimenezi n’zodetsedwa kwa inu. 8 Musamadyenso nkhumba+ chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake ndipo ikafa musamaikhudze.+
9 “Mwa mitundu yonse ya zinthu zokhala m’madzi, zimene mungadye ndi izi: Chilichonse chokhala ndi zipsepse ndi mamba mungadye.+ 10 Chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba musadye.+ Chimenecho n’chodetsedwa kwa inu.
11 “Mbalame iliyonse yosadetsedwa mungadye. 12 Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13 mphamba wofiira, mphamba wakuda+ ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14 Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala.+ 15 Musadyenso nthiwatiwa,+ kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi. 16 Musadyenso nkhwezule, mantchichi,+ tsekwe, 17 vuwo,+ muimba, chiswankhono, 18 dokowe, sadzu, mleme+ ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri n’todetsedwa kwa inu.+ Timeneti simuyenera kudya. 20 Cholengedwa chilichonse chouluka chosadetsedwa mungadye.
21 “Musadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Muziipereka kwa mlendo wokhala mumzinda wanu kuti adye, kapena muziigulitsa kwa mlendo* chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.
“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+
22 “Usalephere kupereka chakhumi cha mbewu zako zonse zokolola m’munda mwako chaka ndi chaka.+ 23 Uzidzadya zinthu zako pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake. Uzidzadya chakhumi cha mbewu zako,+ kumwa vinyo wako watsopano, kudya mafuta ako, ana oyamba a ng’ombe ndi a nkhosa zako.+ Uzichita zimenezi kuti uphunzire kuopa Yehova Mulungu wako nthawi zonse.+
24 “Ndiyeno ulendo ukakhala wautali kwa iwe,+ ndipo sungathe kunyamula chakhumicho, popeza malo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuikapo dzina lake+ ali kutali ndi iwe (chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa,)+ 25 uzidzagulitsa chakhumicho ndipo uzidzatenga ndalamazo ndi kuzifumbata m’manja mwako popita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe. 26 Ndalamazo udzagulire chilichonse chimene mtima wako wakhumba,+ kaya ndi ng’ombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa+ ndi chilichonse chimene mtima wako wafuna. Ndipo uzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kukondwera,+ iweyo ndi banja lako. 27 Mlevi wokhala mumzinda wanu usamutaye,+ pakuti alibe gawo kapena cholowa monga iwe.+
28 “Kumapeto kwa zaka zitatu uzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zako zonse m’chaka chimenecho,+ ndipo uzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu. 29 Ndiyeno Mlevi,+ popeza alibe gawo kapena cholowa monga iwe, komanso mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye+ wokhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta kuti Yehova Mulungu wako akudalitse+ pa chilichonse+ chimene dzanja lako likuchita.