2 Mafumu
2 Yehova atatsala pang’ono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+ 2 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu,+ sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapita ku Beteli.+ 3 Ndiyeno ana a aneneri+ amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo.+ Khalani chete.”
4 Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Khala apa Elisa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko. 5 Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo. Khalani chete.”+
6 Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yorodano.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo. 7 Ndiyeno panali ana a aneneri 50 omwe anakaima chapatali poonekera.+ Koma Eliya ndi Elisa anakaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. 8 Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika uku ndi uku, chotero iwo anawoloka pouma.+
9 Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.”+ Elisa anati: “Chonde, magawo awiri+ a mzimu+ wanu abwere kwa ine.”+ 10 Eliya anati: “Wapempha+ chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.”
11 Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta*+ lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba.+ 12 Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo, ndipo anali kufuula kuti: “Bambo anga, bambo anga!+ Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Zitatero, Elisa sanamuonenso Eliya. Kenako Elisa anagwira zovala zake n’kuzing’amba pakati.+ 13 Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi, ndipo anabwerera kukaima m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano. 14 Ali pamenepo, anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija n’kumenya nacho madzi a mtsinjewo,+ n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?”+ Atamenya madziwo, pang’onopang’ono madziwo anagawanika uku ndi uku, ndipo Elisa anawoloka.
15 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu+ wa Eliya uli pa Elisa.” Chotero anapita kukakumana naye n’kugwada+ pamaso pake mpaka nkhope zawo pansi. 16 Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu, bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu+ wa Yehova wamunyamula ndipo wam’ponya paphiri linalake kapena m’chigwa.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatumize.” 17 Koma iwo anam’kakamiza mpaka iye anachita manyazi, choncho anati: “Atumizeni.” Chotero anatumiza amuna 50 kukafunafuna Eliya. Iwo anam’funafuna kwa masiku atatu koma sanam’peze. 18 Ndiyeno anabwerera kwa Elisa ku Yeriko.+ Anthuwo atafika, Elisa ananena kuti: “Kodi ine sindinakuuzeni kuti, ‘Musapite’?”
19 Patapita nthawi, anthu a mumzindawo anauza Elisa kuti: “Mzindawu uli pamalo abwino+ monga mmene inu mbuyathu mukuonera, koma madzi+ ake ndi oipa, ndipo nthaka ikuchititsa akazi kupita padera.”+ 20 Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni mbale yaing’ono yatsopano yolowa, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anam’bweretseradi mbaleyo. 21 Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo n’kuponyapo mchere uja,+ n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino.+ Sadzachititsanso imfa kapena kuchititsa akazi kupita padera.’” 22 Madziwo ndi abwino kufikira lero+ mogwirizana ndi mawu amene Elisa ananena.
23 Kenako Elisa ananyamuka kupita ku Beteli.+ Akuyenda kukwezeka chitunda, anyamata ena+ amene anachokera mumzinda anayamba kumunyoza mokuwa+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe!+ Choka kuno wadazi iwe!” 24 Pomalizira pake Elisa anatembenuka ndipo anawaona. Atatero anawaitanira tsoka+ m’dzina la Yehova. Kenako zimbalangondo ziwiri zazikazi+ zinatuluka m’thengo n’kukhadzulapo anyamata 42.+ 25 Elisa anapitiriza ulendo wake mpaka kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera n’kupita ku Samariya.