Deuteronomo
33 Tsopano ili ndi dalitso+ limene Mose, munthu wa Mulungu woona,+ anadalitsa nalo ana a Isiraeli iye asanafe. 2 Ndipo anati:
“Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+
Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+
Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+
Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+
Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+
3 Iye analinso kukonda anthu ake.+
Oyera awo onse ali m’manja mwanu.+
Iwowa anakhala pansi, pamapazi panu.+
Anayamba kulandira ena mwa mawu anu.+
5 Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+
Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+
Chiwerengero chonse cha mafuko a Isiraeli.+
7 Popitiriza, iye anapereka dalitso lotsatirali kwa Yuda,+ kuti:
“Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+
M’bweretseni kwa anthu ake.
Manja ake amenya nkhondo pofuna kulanditsa zinthu zake.
Mukhaletu mthandizi wake kwa adani ake.”+
“Tumimu ndi Urimu+ wanu ndizo za munthu wokhulupirika kwa inu,+
Amene munamuyesa pa Masa.+
Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a Meriba.+
9 Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinawaone.’
Ngakhale abale ake sanawavomereze,+
Ndipo ana ake sanawadziwe.
Pakuti anasunga mawu anu,+
Ndipo anapitiriza kusunga pangano lanu.+
10 Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu,+
Ndi Isiraeli m’chilamulo chanu.+
Azipereka nsembe zofukiza kuti muzinunkhiza fungo lake,+
Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+
11 Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,+
Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.+
Muvulaze koopsa ziuno za amene akumuukira,+
Ndi amene amadana naye kwambiri, kuti asamuukire.”+
“Wokondedwa+ wa Yehova akhale m’chitetezo cha Mulungu,+
Pamene akumutchinjiriza tsiku lonse,+
Ndipo iye akhale pakati pa mapewa ake.”+
“Dziko lake lipitirize kudalitsidwa ndi Yehova.+
Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba, mame,+
Ndi madzi akuya a pansi pa nthaka.+
14 Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,+
Ndi zinthu zabwino kwambiri, zokolola za miyezi yosiyanasiyana,+
15 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa, za m’mapiri a kum’mawa,+
Ndi zinthu zabwino kwambiri za m’mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.
16 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+
Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera m’chitsamba chaminga.+
Zimenezi zikhale pamutu pa Yosefe,+
Paliwombo pa munthu wopatulidwa pakati pa abale ake.+
17 Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ng’ombe wamphongo woyamba kubadwa,+
Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+
Nyanga zimenezo adzakankha nazo anthu.+
Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi.
Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+
Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.”
19 Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri.
Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.+
Pakuti adzayamwa chuma chochuluka cha m’nyanja,+
Ndi chuma chobisika cha mumchenga.”
“Wodala ndi iye wofutukula malire a dera la Gadi.+
Iye adzakhala ngati mkango,+
Ndipo adzakhadzula dzanja, adzang’amba mutu paliwombo.+
21 Adzatenga gawo labwino kwambiri kukhala lake,+
Pakuti gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+
Ndipo atsogoleri a anthu adzasonkhana.
Iye adzachitadi chilungamo cha Yehova,
Ndi zigamulo zokhudza Isiraeli.”
“Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa ndi Yehova,
Ndipo madalitso Ake amuchulukira.
Tenga chigawo cha kumadzulo ndi kum’mwera.”+
“Aseri ndi wodalitsidwa ndi ana aamuna.+
Akhale wovomerezeka ndi abale ake,+
Woponda phazi lake m’mafuta.+
25 Chitsulo ndi mkuwa ndizo zokhomera chipata chako,+
Udzayenda mtima uli phee, masiku onse a moyo wako.
26 Palibe wina wofanana ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+
Amene amayenda m’mlengalenga pokuthandiza,+
Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+
27 Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo,+
Ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.+
Adzapitikitsa mdani pamaso pako,+
Ndipo adzanena kuti, ‘Awononge!’+