2 Mbiri
33 Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+
2 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa+ za mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+ 3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka+ amene Hezekiya bambo ake anagwetsa.+ Anamanga maguwa ansembe+ a Abaala+ n’kumanga mizati yopatulika,+ ndipo anayamba kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+ 4 Anamanga maguwa ansembe+ m’nyumba ya Yehova, imene ponena za iyo Yehova anati: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+ 5 Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo+ m’mabwalo+ awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,+ ankachita zanyanga,+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.+
7 Komanso iye anaika m’nyumba ya Mulungu woona+ chifaniziro+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo, Mulungu anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha+ pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa+ mpaka kalekale.+ 8 Sindidzachotsanso phazi la Isiraeli panthaka imene ndinapatsa+ makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo+ chonse, malangizo+ onse, ndi zigamulo+ zonse zimene ndinawapatsa kudzera m’manja mwa Mose.”+ 9 Koma Manase+ anapitiriza kunyengerera Yuda+ ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.+
10 Yehova anapitiriza kulankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanamvere.+ 11 Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo. 12 Iye atasautsika mumtima mwake chifukwa cha zimenezi,+ anakhazikitsa pansi mtima wa Yehova Mulungu wake+ ndipo anadzichepetsa+ kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+
14 Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja+ kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira m’chigwa kukafika ku Chipata cha Nsomba.+ Mpandawo unazungulira n’kukafika ku Ofeli+ ndipo unali wautali kwambiri kuchokera pansi kufika pamwamba. Kuwonjezera apo, iye anaika akuluakulu a asilikali m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 15 Anachotsa milungu yachilendo,+ fano+ limene linali m’nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse ansembe+ amene anamanga m’phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu. Kenako, zinthu zimenezi anakazitaya kunja kwa mzinda. 16 Komanso Manase anakonza guwa lansembe la Yehova+ n’kuyamba kuperekerapo nsembe zachiyanjano+ ndi zoyamikira,+ ndipo anauza Ayuda kuti azitumikira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 17 Komabe anthu anali kuperekabe nsembe m’malo okwezeka,+ kungoti anali kuzipereka kwa Yehova Mulungu wawo.
18 Nkhani zina zokhudza Manase, pemphero+ limene anapereka kwa Mulungu wake, ndi mawu a anthu amasomphenya+ amene anali kulankhula naye m’dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, zatchulidwa m’nkhani za mafumu a Isiraeli.+ 19 Nkhani zokhudza pemphero lake,+ zokhudza mmene Mulungu anamvera kupembedza kwake,+ machimo ake onse,+ ndi kusakhulupirika kwake+ zinalembedwa m’mawu a amasomphenya ake. M’mawu amenewa munalembedwanso nkhani zokhudza malo amene iye anamangako malo okwezeka+ n’kuikapo mizati yopatulika+ ndi zifaniziro zogoba+ asanadzichepetse.+ 20 Pomalizira pake Manase anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda+ panyumba yake. Kenako Amoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
21 Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ 22 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ monga anachitira Manase bambo ake.+ Amoni anali kupereka nsembe+ kwa zifaniziro zonse zogoba+ zimene bambo ake+ anapanga, ndipo anapitiriza kuzitumikira.+ 23 Iye sanadzichepetse+ pamaso pa Yehova monga anadzichepetsera Manase bambo ake,+ pakuti Amoni ndiye amene anawonjezera kupalamula.+ 24 Pomalizira pake, atumiki ake anam’chitira chiwembu+ n’kumupha m’nyumba mwake momwe.+ 25 Koma anthu a m’dzikolo anapha+ anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni.+ Kenako anthu+ a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake.