Hoseya
7 “Nthawi zonse ndikafuna kuchiritsa Isiraeli,+ zolakwa za Efuraimu ndi zoipa za Samariya+ zimaonekera.+ Iwo amachita zachinyengo+ ndipo anthu akuba amalowa m’nyumba komanso gulu la achifwamba limasakaza zinthu panja.+ 2 Mumtima mwawo saganiza+ kuti ine ndidzakumbukira zochita zawo zonse zoipa.+ Tsopano ntchito zawo zawazungulira+ ndipo zili pamaso panga.+ 3 Iwo amasangalatsa mfumu ndi zoipa zawo, ndiponso amasangalatsa akalonga ndi chinyengo chawo.+ 4 Anthu onsewo ndi achigololo.+ Ali ngati ng’anjo yamoto imene wophika mkate waiyatsa. Ng’anjoyo yatentha kwambiri moti iye sakufunikira kuisonkhezera pamene akukanda ufa ndi kudikira kuti ufufume. 5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu, akalonga adzidwalitsa+ ndipo ali ndi ukali chifukwa cha vinyo.+ Mfumuyo yatambasula dzanja lake pamodzi ndi anthu onyoza. 6 Anthuwo atenthetsa mitima yawo ngati kuti aibweretsa pafupi ndi ng’anjo yamoto.+ Mitima yawoyo ikutentha mkati mwawo.+ Wophika mkate akugona usiku wonse. Pofika m’mawa, ng’anjoyo ikuyaka moto walawilawi.+ 7 Onsewo akutentha ngati ng’anjo yamoto, ndipo akuwononga oweruza awo. Mafumu awo onse agwa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akundiitana.+
8 “Efuraimu amagwirizana ndi anthu a mitundu ina.+ Iye wakhala ngati mkate wozungulira umene wapsa mbali imodzi yokha.+ 9 Alendo alanda mphamvu zake,+ ndipo iye sakudziwa zimenezi.+ Mutu wake wonse wangoti mbuu ndi imvi, koma iye sakudziwa zimenezi. 10 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+ koma iwo sanabwerere kwa Yehova Mulungu wawo.+ Sanamufunefune ngakhale kuti achita zinthu zonsezi.+ 11 Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa,+ yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+
12 “Kulikonse kumene iwo angapite, ndidzawatchera ndi ukonde.+ Ndidzawagwira ngati zolengedwa zouluka m’mlengalenga.+ Ndidzawalanga mogwirizana ndi chenjezo limene ndinauza msonkhano wawo.+ 13 Tsoka kwa iwo+ chifukwa andithawa!+ Adzawonongedwa chifukwa chakuti aphwanya malamulo anga. Ine ndinali kufuna kuwawombola,+ koma iwo alankhula mabodza otsutsana nane.+ 14 Sanapemphe thandizo kwa ine ndi mtima wawo wonse+ ngakhale kuti anali kulira mofuula ali pamabedi awo. Anali kungokhala, osachita chilichonse, chifukwa anali ndi chakudya chambiri ndi vinyo wambiri wotsekemera.+ Nthawi zonse anali kuchita zinthu zonditembenukira.+ 15 Ine ndinawalangiza+ ndipo ndinalimbitsa manja awo.+ Koma iwo anali kukonza ziwembu, chotero anakhala otsutsana nane.+ 16 Anabwerera, koma sanapite ku chipembedzo choona.+ Anakhala ngati uta wosakungika.+ Akalonga awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mwano wa lilime lawo lomwe.+ N’chifukwa chake iwo adzanyozedwa m’dziko la Iguputo.”+