Tito
1 Ine Paulo, kapolo+ wa Mulungu ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa+ ndi Mulungu. Komanso ndine wodziwa molondola+ choonadi+ chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 2 kumene kwazikidwa pa chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chomwe Mulungu amene sanganame,+ analonjeza kalekale.+ 3 Koma mu nthawi yake, anapangitsa mawu ake kuonekera kudzera mu ulaliki umene ndinapatsidwa+ mwa lamulo la Mpulumutsi wathu,+ Mulungu. 4 Ndikulembera Tito, mwana wanga+ weniweni m’chikhulupiriro chimodzi chomwe tili nacho:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wa Mulungu Atate+ ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu,+ zikhale nawe.
5 Ndinakusiya ku Kerete+ kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike+ akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo+ amene ndinakupatsa. 6 Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi+ mmodzi, wa ana okhulupirira ndi osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.+ 7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera.+ Pokhala mtumiki*+ wa Mulungu, asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa,*+ wandewu,+ kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 8 Koma akhale wochereza alendo,+ wokonda zabwino, woganiza bwino,+ wolungama, wokhulupirika,+ wodziletsa,+ 9 wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.
10 Pakuti pali anthu ambiri osalamulirika, olankhula zopanda pake,+ ndi opotoza maganizo a ena, makamaka amene akusungabe mdulidwe+ pakati pa anthu amenewa. 11 N’kofunika kuwatseka pakamwa, pakuti anthu amenewa, pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+ akuwonongabe mabanja athunthu+ mwa kuphunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa. 12 Wina wa iwo, amenenso ndi mneneri wawo, ananena kuti: “Akerete ndi anthu abodza nthawi zonse, zilombo zakutchire zolusa,+ ndiponso alesi osusuka.”
13 Umboni umenewu ndi woona. Chifukwa cha zimenezi, pitiriza kuwadzudzula mwamphamvu,+ kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.+ 14 Asamasamale nthano zachiyuda+ ndi malamulo a anthu+ amene asiya choonadi.+ 15 Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa+ ndi opanda chikhulupiriro+ kulibe choyera, m’malomwake maganizo awo ndi chikumbumtima+ chawo n’zoipa. 16 Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu,+ koma amamukana ndi zochita zawo+ chifukwa ndi onyansa ndi osamvera, ndipo ndi osayenerera+ ntchito iliyonse yabwino.