Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 14
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Machitidwe

      • Okhulupirira anawonjezeka ku Ikoniyo; anayamba kutsutsidwa (1-7)

      • Ankawayesa kuti ndi milungu ku Lusitara (8-18)

      • Paulo anapulumuka atamuponya miyala (19, 20)

      • Analimbikitsa mipingo (21-23)

      • Anabwerera ku Antiokeya wa ku Siriya (24-28)

Machitidwe 14:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 95

Machitidwe 14:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 13:45

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/1/1998, tsa. 16

Machitidwe 14:3

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 19:11; Ahe 2:3, 4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/1/1998, tsa. 16

Machitidwe 14:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 11

Machitidwe 14:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 14:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 95-96

Machitidwe 14:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 10:23

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 95-96

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/1993, tsa. 3

    6/15/1990, tsa. 11

Machitidwe 14:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 9:28

Machitidwe 14:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 35:6

Machitidwe 14:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 28:3-6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, ptsa. 11-12

Machitidwe 14:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Baibulo la Dziko Latsopano (nwt), tsa. 2146

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2008, tsa. 32

    6/15/1990, ptsa. 11-12

    5/15/1990, tsa. 25

Machitidwe 14:13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/1990, tsa. 25

Machitidwe 14:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 10:25, 26
  • +Eks 20:11; Sl 146:6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 97-98

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, ptsa. 11-12

Machitidwe 14:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 17:30

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    7/1/2013, tsa. 11

    6/15/1990, ptsa. 11-12

Machitidwe 14:17

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 17:26, 27; Aro 1:20
  • +Sl 147:8; Yer 5:24; Mt 5:45
  • +Sl 145:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 97-98

    Yandikirani, ptsa. 272-273

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 7

    Galamukani!,

    No. 3 2021 tsa. 14

    Nsanja ya Olonda,

    7/1/2013, tsa. 11

    6/15/1990, ptsa. 11-12

Machitidwe 14:19

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 17:13
  • +2Ak 11:25

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    11/1/2015, tsa. 13

Machitidwe 14:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 16:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    2/15/2013, ptsa. 28-29

Machitidwe 14:22

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 11:22, 23
  • +Mt 10:38; Yoh 15:19; Aro 8:17; 1At 3:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Nsanja ya Olonda,

    11/1/2015, ptsa. 13-14

    9/15/2014, tsa. 13

Machitidwe 14:23

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Tit 1:5
  • +Mac 13:2, 3

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 99

Machitidwe 14:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 13:13

Machitidwe 14:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 13:1, 2

Machitidwe 14:27

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 11:18

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 101

Machitidwe 14:28

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/2008, tsa. 28

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Mac. 14:2Mac 13:45
Mac. 14:3Mac 19:11; Ahe 2:3, 4
Mac. 14:5Mac 14:19
Mac. 14:6Mt 10:23
Mac. 14:9Mt 9:28
Mac. 14:10Yes 35:6
Mac. 14:11Mac 28:3-6
Mac. 14:15Mac 10:25, 26
Mac. 14:15Eks 20:11; Sl 146:6
Mac. 14:16Mac 17:30
Mac. 14:17Mac 17:26, 27; Aro 1:20
Mac. 14:17Sl 147:8; Yer 5:24; Mt 5:45
Mac. 14:17Sl 145:16
Mac. 14:19Mac 17:13
Mac. 14:192Ak 11:25
Mac. 14:20Mac 16:1
Mac. 14:22Mac 11:22, 23
Mac. 14:22Mt 10:38; Yoh 15:19; Aro 8:17; 1At 3:4
Mac. 14:23Tit 1:5
Mac. 14:23Mac 13:2, 3
Mac. 14:24Mac 13:13
Mac. 14:26Mac 13:1, 2
Mac. 14:27Mac 11:18
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe 14:1-28

Machitidwe a Atumwi

14 Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo, analowa mʼsunagoge wa Ayuda ndipo analankhula bwino kwambiri moti Ayuda ambiri limodzi ndi Agiriki anakhala okhulupirira. 2 Koma Ayuda amene sanakhulupirire, anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo kuti atsutsane ndi abalewo.+ 3 Choncho kwa nthawi yaitali, ankalankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova.* Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, polola kuti ophunzirawo azichita zizindikiro ndi zodabwitsa.+ 4 Koma gulu la anthu mumzindawo linagawanika. Ena anali kumbali ya Ayuda, ena kumbali ya atumwi. 5 Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo nʼkuwaponya miyala.+ 6 Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadera ozungulira.+ 7 Kumeneko anapitiriza kulalikira uthenga wabwino.

8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolumala miyendo ndipo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo. 9 Munthu ameneyu ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Ndiyeno Paulo atamuyangʼanitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro choti angachiritsidwe.+ 10 Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira!” Atatero, wolumalayo anadumpha nʼkuyamba kuyenda.+ 11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazo, linafuula mʼchilankhulo cha Chilukaoniya kuti: “Milungu yakhala ngati anthu ndipo yatsikira kwa ife!”+ 12 Choncho Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo ankamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene ankatsogolera polankhula. 13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi ndi polowera mumzindawo, anabweretsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pamageti. Iye ankafuna kupereka nsembe pamodzi ndi gulu la anthulo.

14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba malaya awo akunja nʼkuthamanga kukalowa mʼgulu la anthu lija akufuula kuti: 15 “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.+ Tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti musiye zinthu zachabechabezi nʼkuyamba kulambira Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+ 16 Mʼmibadwo yamʼmbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuti aziyenda mʼnjira zawo.+ 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+ 18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena zimenezi, anavutikabe kuletsa gulu la anthulo kupereka nsembe kwa iwo.

19 Ndiyeno Ayuda amene anabwera kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala nʼkumukokera kunja kwa mzindawo poganiza kuti wafa.+ 20 Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka nʼkukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka nʼkupita ku Debe.+ 21 Atalengeza uthenga wabwino mumzindawu nʼkuphunzitsa anthu ambiri ndithu kuti akhale ophunzira, anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. 22 Mʼmalo onsewa ankalimbitsa ophunzira+ komanso kuwathandiza kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro. Ankawauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 23 Anasankhanso akulu mumpingo uliwonse,+ ndipo atapemphera komanso kusala kudya,+ anawapereka kwa Yehova* yemwe anamukhulupirira.

24 Kenako anadutsa ku Pisidiya nʼkupita ku Pamfuliya.+ 25 Atamaliza kulalikira mawu a Mulungu ku Pega, anapita ku Ataliya. 26 Pochoka kumeneko anayenda ulendo wapamadzi kubwerera ku Antiokeya. Kumeneku nʼkumene mʼmbuyomo abale anawasankha kuti Mulungu awasonyeze kukoma mtima kwakukulu nʼcholinga choti agwire ntchito, yomwe tsopano pa nthawiyi anali ataimaliza.+

27 Atafika kumeneko anasonkhanitsa anthu amumpingo ndipo anawafotokozera zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. Anawafotokozeranso kuti Mulungu anatsegulanso khomo kuti anthu a mitundu ina akhale okhulupirira.+ 28 Choncho anakhala ndi ophunzirawo kwa kanthawi ndithu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena