Ezekieli
30 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Fuulani anthu inu kuti, ‘Kalanga ine! Tsiku lija layandikira.’+ 3 Tsikulo lili pafupi. Inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Limeneli lidzakhala tsiku la mitambo,+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+ 4 Lupanga lidzafikadi mu Iguputo,+ ndipo ku Itiyopiya anthu adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitika anthu akadzaphedwa mu Iguputo, chuma cha dzikolo chikadzalandidwa komanso maziko ake akadzagwetsedwa.+ 5 Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera ku mitundu ina,+ Kubi ndi anthu ochokera m’dziko la Isiraeli amene ali m’pangano, onsewa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Aiguputo.”’+
6 “Yehova wanena kuti, ‘Nawonso othandiza Iguputo adzaphedwa, ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.’+
“‘Kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene,+ anthu adzaphedwa ndi lupanga m’dzikolo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 7 ‘Onsewo adzakhala mabwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu ndipo mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yowonongedwa.+ 8 Ndikadzayatsa moto mu Iguputo, ndipo onse omuthandiza akadzawonongedwa, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 9 Pa tsikulo, amithenga ochokera kwa ine adzakwera zombo kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira.+ Itiyopiya adzamva ululu woopsa pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, pakuti tsikulo lidzafika ndithu.’+
10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+ 11 Mfumuyo ndi anthu ake, olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu,+ akubwera kudzawononga dzikolo kuti likhale bwinja. Iwo adzasolola malupanga awo kumenyana ndi Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+ 12 Ndidzaumitsa ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo+ ndi kugulitsa dzikolo kwa anthu oipa.+ Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu achilendo.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’+
13 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononganso mafano onyansa+ ndi kuthetsa milungu yopanda pake ku Nofi.+ Sipadzapezekanso mtsogoleri wochokera m’dziko la Iguputo, ndipo ndidzachititsa anthu a m’dzikolo kukhala mwamantha.+ 14 Mzinda wa Patirosi+ ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani+ ndidzautentha ndi moto ndipo ndidzapereka ziweruzo mumzinda wa No.+ 15 Ndidzatsanulira mkwiyo wanga+ pa Sini, malo otetezedwa kwambiri a Iguputo, ndipo ndidzapha khamu la anthu a ku No.+ 16 Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzamva ululu waukulu, No adzalandidwa ndi adani amene adzagumule mpanda wake. Adani adzalowa mumzinda wa Nofi masanasana. 17 Anyamata a ku Oni+ ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga. Anthu a m’mizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo. 18 Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 19 Ndidzapereka ziweruzo mu Iguputo+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
20 Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova analankhulanso ndi ine kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo.+ Dzanjalo silidzamangidwa ndi nsalu zomangira pachilonda+ kuti lichire n’kukhalanso lamphamvu kuti lizidzatha kugwira lupanga.”
22 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndidzathyola manja ake onse,+ dzanja lamphamvu ndi lothyoka lija,+ ndipo ndidzachititsa kuti lupanga ligwe m’dzanja lake.+ 23 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu ndi kuwamwazira kumayiko ena.+ 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa.+ Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri pamaso pa mfumu ya Babulo monga wovulazidwa koopsa.+ 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo ndipo Farao adzagwetsa manja ake. Ndikadzapereka lupanga langa m’manja mwa mfumu ya Babulo, iye n’kuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 26 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu+ ndi kuwamwazira kumayiko ena, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”