Nehemiya
10 Tsopano amene anatsimikizira panganoli ndi chidindo+ chawo ndi awa:
Nehemiya+ amene ndiye Tirisata,+ mwana wa Hakaliya,+
Komanso Zedekiya, 2 Seraya,+ Azariya, Yeremiya, 3 Pasuri, Amariya, Malikiya, 4 Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5 Harimu,+ Meremoti, Obadiya, 6 Danieli,+ Ginetoni, Baruki, 7 Mesulamu, Abiya, Miyamini, 8 Maaziya, Biligai ndi Semaya. Amenewa anali ansembe.
9 Panalinso Alevi awa amene anatsimikizira panganoli: Yesuwa,+ mwana wamwamuna wa Azaniya, Binui wochokera pakati pa ana a Henadadi,+ Kadimiyeli, 10 ndi abale awo awa, Sebaniya,+ Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11 Mika, Rehobu, Hasabiya, 12 Zakuri, Serebiya,+ Sebaniya, 13 Hodiya, Bani ndi Beninu.
14 Atsogoleri awa a anthu anatsimikiziranso panganoli: Parosi, Pahati-mowabu,+ Elamu, Zatu, Bani, 15 Buni, Azigadi, Bebai, 16 Adoniya,* Bigivai, Adini, 17 Ateri, Hezekiya, Azuri, 18 Hodiya, Hasumu, Bezai, 19 Harifi,* Anatoti, Nebai, 20 Magipiasi, Mesulamu, Heziri, 21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22 Pelatiya, Hanani, Anaya, 23 Hoshiya, Hananiya, Hasubu, 24 Halohesi, Pila, Sobeki, 25 Rehumu, Hasabina, Maaseya, 26 Ahiya, Hanani, Anane, 27 Maluki, Harimu ndi Bana.
28 Ndiyeno anthu ena onse, ansembe,+ Alevi,+ alonda a pazipata,+ oimba,+ Anetini,+ ndi aliyense amene anadzipatula kwa mitundu ya anthu a m’mayikowo+ kuti asunge chilamulo+ cha Mulungu woona, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi ndi aliyense wodziwa zinthu ndi wozindikira,+ 29 anali kumamatirabe kwa abale awo,+ anthu otchuka.+ Iwo anali kudzilowetsa m’lumbiro limene likanatha kuwabweretsera temberero.+ Lumbiro+ limenelo linali lakuti tidzatsatira chilamulo cha Mulungu woona+ chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu woona, ndi kusunga+ malamulo onse, zigamulo ndi mfundo+ za Yehova Ambuye wathu,+ 30 kutinso tisapereke ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu ya m’dzikoli, ndiponso tisatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana athu aamuna.+
31 Kunena za mitundu ya anthu a m’dzikolo+ imene inali kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse* pa sabata, tinalumbira kuti sitigula kalikonse kuchokera kwa iwo pa sabata+ kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitiyenera kulima minda yathu m’chaka cha 7,+ ndipo tiyenera kukhululukira ngongole wina aliyense.+
32 Kuwonjezera apo, tinadziikira malamulo akuti chaka chilichonse aliyense wa ife azipereka gawo limodzi mwa magawo atatu a sekeli kuti ndalama zimenezo akazigwiritsire ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsire ntchito pokonza mkate wosanjikiza,+ nsembe yachikhalire yambewu,+ nsembe yachikhalire yopsereza ya pa tsiku la sabata+ ndi tsiku lokhala mwezi.+ Akazigwiritsirenso ntchito pokonza madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika+ ndi nsembe yamachimo+ yophimbira machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse za panyumba ya Mulungu wathu.+
34 Komanso tinachita maere+ okhudza ansembe, Alevi ndi anthu oti azibweretsa nkhuni+ kunyumba ya Mulungu wathu, mogwirizana ndi nyumba ya makolo athu, pa nthawi zoikidwiratu, chaka ndi chaka kuti aziziyatsira moto paguwa lansembe la Yehova Mulungu wathu,+ malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo.+ 35 Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+ 36 Kutinso azibweretsa ana aamuna oyamba kubadwa+ mwa ana athu ndi ziweto+ zathu malinga ndi zolembedwa m’chilamulo.+ Komanso kuti azibweretsa ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi nkhosa+ zathu kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene anali kutumikira m’nyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tinafunika kupititsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu,+ zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano+ ndi mafuta+ kwa ansembe kumalo odyera+ m’nyumba ya Mulungu wathu. Tinafunikanso kupititsa chakhumi kwa Alevi+ pa zinthu zochokera m’nthaka yathu, pakuti Aleviwo anali kulandira chakhumi kuchokera m’mizinda yathu yonse ya zaulimi.
38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akulandira chakhumi.* Aleviwo azipereka gawo limodzi mwa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu+ wathu kuzipinda zodyera+ m’nyumba yosungiramo zinthu. 39 Pakuti ana a Isiraeli ndi ana a Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta kuzipinda zodyera. Kumeneku ndi kumene kuli ziwiya za kumalo opatulika ndi ansembe amene anali kutumikira,+ olondera pazipata+ ndi oimba,+ ndipo tisanyalanyaze nyumba ya Mulungu wathu.+