Yobu
38 Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:
2 “Kodi amene akuphimba malangizo anga
Ndi mawu ake opanda nzeruyu ndani?+
3 Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu.
Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+
5 Ndani anaika miyezo yake, ngati ukudziwa,
Kapena ndani anatambasulirapo chingwe choyezera?
6 Kodi maziko ake anazikidwa pa chiyani?+
Kapena ndani anaika mwala wake wapakona,
7 Pamene nyenyezi za m’mawa+ zinafuula pamodzi mokondwera,
Ndiponso pamene ana onse a Mulungu+ anayamba kufuula ndi chisangalalo?
8 Ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+
Imene inayamba kuyenda ngati kuti ikutumphuka m’mimba?
9 Pamene ndinaika mtambo ngati chovala chake,
Ndi mdima wandiweyani ngati nsalu yoikulungira.
10 Ndipo ndinaiikira lamulo,
Ndinaiikiranso mpiringidzo ndi zitseko.+
11 Kenako ndinaiuza kuti, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,+
Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepa.’+
12 Kodi kuyambira masiku ako oyambirira unalamula m’mawa?+
Kodi ndiwe unachititsa m’bandakucha kudziwa malo ake,
13 Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi,
Kuti anthu oipa asansidwe n’kuchotsedwamo?+
14 Dzikolo limadzisintha ngati dongo+ pansi pa chodindira,
Ndipo zinthu zimakhala pamalo awo ngati kuti zavala zovala.
19 Kodi njira yopita kumene kuwala kumakhala ili kuti?+
Nanga mdima, kwawo n’kuti,
20 Kuti uzipititse kumalire awo,
Ndi kuti udziwe njira zopita kunyumba kwawo?
21 Kodi ukudziwa popeza pa nthawiyo unali utabadwa,+
Ndiponso chifukwa chakuti masiku ako ndi ochuluka?
22 Kodi unalowapo munkhokwe ya chipale chofewa,+
Kapena umaziona nkhokwe za matalala,+
23 Zimene ndazisungira nthawi ya zowawa,
Ndi tsiku lomenyana komanso lankhondo?+
24 Kodi njira imene kuwala kumadzigawira ili kuti,
Ndiponso njira imene mphepo ya kum’mawa+ imamwazikira padziko lapansi ili kuti?
25 Ndani anagawa ngalande ya madzi osefukira,
Ndi njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+
26 Kuti achititse mvula kugwa padziko pamene palibe munthu,+
Ndi kuchipululu kumene kulibe munthu aliyense,
27 Kuti inyowetse malo owonongeka ndi mvula yamkuntho ndiponso ouma,
Komanso kuti imeretse udzu?+
29 Kodi madzi oundana amachokera m’mimba mwa ndani,
Ndipo mame oundana+ a m’mlengalenga anawabereka ndani?
31 Kodi ungamange zingwe gulu la nyenyezi la Kima,
Kapena kodi ungamasule zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+
32 Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi la Mazaroti pa nthawi yake?
Ndipo kodi ungatsogolere gulu la nyenyezi la Asi pamodzi ndi ana ake?
35 Kodi ungauze mphezi kuti zibwere kwa iwe
N’kudzakuuza kuti, ‘Ndife pano, tabwera’?
37 Ndani amene ali ndi nzeru zoti angathe kudziwa chiwerengero cholondola cha mitambo,
Kapena zosungira madzi akumwamba, ndani angathe kuzipendeketsa,+
38 Fumbi likasanduka matope n’kumayenderera ngati chitsulo chosungunula,
Ndiponso zibuma zadothi zikamatana?