Maliro
א [ʼAʹleph]
2 Chifukwa chokwiya, Yehova waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo+ wakuda.
Iye waponya pansi chokongoletsera+ Isiraeli kuchokera kumwamba.+
Sanakumbukire chopondapo mapazi+ ake pa tsiku la mkwiyo wake.
ב [Behth]
2 Yehova wameza malo okhala a Yakobo. Sanamvere chisoni malo ake alionse.+
Mu ukali wake, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri+ ya mwana wamkazi wa Yuda.
Waipitsa ufumu+ ndi akalonga+ ake ndipo wawagwetsera pansi.+
ג [Giʹmel]
3 Mu mkwiyo wake wathyola nyanga* iliyonse ya Isiraeli.+
Adani athu atatiukira, iye sanatithandize.+
Mkwiyo wake ukuyakirabe Yakobo ngati moto umene wawononga ponseponse.+
ד [Daʹleth]
4 Wakunga uta wake ngati mdani.+ Dzanja lake lamanja+ lakonzeka ngati la mdani,+
Ndipo wapitiriza kupha+ anthu onse ofunika kwambiri.
Ukali wake waukhuthula ngati moto+ m’hema+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
ה [Heʼ]
5 Yehova wakhala ngati mdani.+ Wameza Isiraeli.+
Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli zokhalamo.+ Wawononga malo ake otetezedwa ndiponso mipanda yolimba kwambiri.+
Wachititsa kuti kulira ndi maliro+ zimveke mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda.
ו [Waw]
6 Iye wapasula chisimba*+ chake ngati chisimba cha m’munda+ ndipo wathetsa zikondwerero zake.
Yehova wachititsa kuti zikondwerero+ ndi sabata ziiwalike mu Ziyoni,
Ndipo mu mkwiyo wake waukulu wakana mfumu ndi wansembe.+
ז [Zaʹyin]
7 Yehova wataya guwa lake lansembe.+ Iye wanyoza malo ake opatulika.+
Wapereka m’manja mwa adani makoma* a nsanja zake zokhalamo.+
Iwo afuula m’nyumba ya Yehova ngati pa tsiku lachikondwerero.+
ח [Chehth]
8 Yehova waganiza zogwetsa mpanda+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
Watambasula chingwe choyezera.+ Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko.+
Walilitsa+ chiunda chomenyerapo nkhondo ndi mpanda. Zonsezi zatha mphamvu.
ט [Tehth]
9 Zipata+ zake zamira munthaka. Wawononga mipiringidzo yake ndipo waithyolathyola.
Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa mitundu ina.+ Malamulo sakutsatiridwa.+
Aneneri ake sakuonanso masomphenya ochokera kwa Yehova.+
י [Yohdh]
10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi ndipo akhala chete.+
Iwo athira fumbi pamitu+ yawo ndipo avala ziguduli.*+
Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo mpaka padothi.+
כ [Kaph]
11 Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+
Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+
Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda.
ל [Laʹmedh]
12 Iwo anali kufunsa amayi awo kuti: “Kodi chakudya ndi vinyo zili kuti?”+
Anali kufunsa chifukwa anali kukomoka m’mabwalo a mzinda ndi kugona pansi ngati anthu ophedwa,
Ndiponso chifukwa moyo wawo unali kukhuthukira pachifuwa cha amayi awo.
מ [Mem]
13 Kodi ndikusonyeze umboni wotani? Kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?+
Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?+
Pakuti kuwonongeka+ kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja. Ndani angakuchiritse?+
נ [Nun]
14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.
Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+
Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.
ס [Saʹmekh]
15 Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba m’manja+ monyodola.
Akuimba mluzu+ ndi kupukusa mitu+ yawo poona mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti:
“Kodi uwu ndi mzinda umene anali kunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri, wotamandika padziko lonse lapansi’?”+
פ [Peʼ]
16 Adani ako onse akukutsegulira pakamwa.+
Akuimba mluzu ndi kukukukutira mano.+ Iwo akunena kuti: “Ameneyu timumeza.+
Ndithu, lero ndi tsiku limene takhala tikuyembekezera.+ Lafikadi! Taliona!”+
ע [ʽAʹyin]
17 Yehova wachita zimene anali kuganiza.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+
Zimene analamula kalekale.+ Wapasula zinthu ndipo sanamve chisoni.+
Wachititsa adani ako kusangalala+ chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wakweza nyanga ya adani+ ako.
צ [Tsa·dhehʹ]
18 Mtima wa anthuwo wafuulira Yehova,+ iwe mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+
Gwetsa misozi ngati mtsinje usana ndi usiku.+
Usapume. Mwana wa diso lako asaleke kulira.
ק [Qohph]
19 Nyamuka! Lira mofuula usiku, pa nthawi yoyamba ulonda+ wam’mawa.
Khuthula+ mtima wako pamaso+ pa Yehova ngati madzi.
Pemphera utakweza manja+ ako kwa iye chifukwa cha ana ako,
Amene akukomoka ndi njala m’misewu.+
ר [Rehsh]
20 Inu Yehova, yang’anani kuti muone+ yemwe mwamulanga chotere.
Kodi amayi azidya zipatso za mimba yawo, ana awo athanzi?+
Kapena kodi wansembe ndi mneneri aziphedwa m’malo opatulika a Yehova?+
ש [Shin]
21 Anyamata ndi amuna okalamba+ agona pansi m’misewu.+
Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi lupanga.+
Mwapha anthu pa tsiku la mkwiyo+ wanu. Onsewo mwawaphadi+ mopanda chisoni.+
ת [Taw]