Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 15:1-5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?

      Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+

       2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,*+

      Amene amachita zinthu zabwino+

      Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+

       3 Iye sanena miseche ndi lilime lake,+

      Sachitira mnzake choipa chilichonse,+

      Ndipo sanyoza* anzake.+

       4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+

      Koma amalemekeza anthu amene amaopa Yehova.

      Sasintha zimene walonjeza* ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+

       5 Sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

      Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

      Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.*+

  • Salimo 27:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,

      Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.

      Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+

      Kuti ndione ubwino wa Yehova,

      Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+

  • Salimo 84:1-4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 84 Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,

      Ine ndimakonda kwambiri chihema chanu chachikulu!+

       2 Moyo wanga ukulakalaka kwambiri,

      Inde, ndafookeratu chifukwa cholakalaka

      Mabwalo a Yehova.+

      Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.

       3 Ngakhale mbalame zapeza malo okhala kumeneko

      Ndipo namzeze wadzimangira chisa chake,

      Mmene amasamaliramo ana ake

      Pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu, inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,

      Mfumu yanga ndi Mulungu wanga!

       4 Osangalala ndi anthu amene akukhala mʼnyumba yanu!+

      Iwo akupitiriza kukutamandani.+ (Selah)

  • Salimo 84:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kukhala tsiku limodzi mʼmabwalo anu nʼkwabwino kuposa kukhala kwinakwake masiku 1,000!+

      Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga

      Kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oipa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena