1 Mbiri
23 Davide anali atakalamba+ ndiponso atakhutira ndi masiku a moyo wake. Chotero analonga mwana wake Solomo+ kukhala mfumu ya Isiraeli. 2 Kenako anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli komanso ansembe+ ndi Alevi.+ 3 Atatero, Alevi anawerengedwa kuyambira azaka 30 kupita m’tsogolo.+ Anawerenga mwamuna aliyense wamphamvu, mmodzi ndi mmodzi,* ndipo onse anakwana 38,000. 4 Pakati pawo panali oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova okwana 24,000. Akapitawo+ ndi oweruza+ analipo 6,000. 5 Panalinso alonda 4,000 a pachipata+ ndi anthu 4,000 oimbira Yehova zitamando+ ndi zoimbira+ zimene Davide anati, “Zimenezi ndazipanga kuti tizitamandira Mulungu.”
6 Ndiyeno Davide anawagawa m’magulu+ ndi kuwapereka kwa ana a Levi.+ Anawapereka kwa Gerisoni, Kohati, ndi Merari. 7 M’banja la Gerisoni munali Ladani ndi Simeyi. 8 Ana a Ladani anali atatu. Panali Yehiela+ mtsogoleri wawo, Zetamu ndi Yoweli.+ 9 Ana a Simeyi anali atatu. Panali Selomoti, Hazieli ndi Harana. Amenewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo ya Ladani. 10 Ana a Simeyi anali Yahati, Zina,* Yeusi, ndi Beriya. Ana anayiwa anali a Simeyi. 11 Yahati anali mtsogoleri wawo, ndipo wachiwiri wake anali Ziza. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri aamuna, choncho anakhala nyumba imodzi ya makolo+ ndiponso gulu limodzi lokhala ndi udindo wofanana.
12 Ana a Kohati+ analipo anayi. Panali Amuramu, Izara,+ Heburoni+ ndi Uziyeli.+ 13 Ana aamuna a Amuramu anali Aroni+ ndi Mose.+ Koma Aroni anapatulidwa+ kuti iye ndi ana ake aziyeretsa Malo Oyera Koposa,+ mpaka kalekale. Komanso kuti azifukiza nsembe+ yautsi pamaso pa Yehova, kumutumikira,+ ndi kupereka madalitso+ m’dzina lake mpaka kalekale. 14 Ponena za Mose munthu wa Mulungu woona,+ ana ake anapitiriza kuwawerenga pamodzi ndi fuko la Levi.+ 15 Ana a Mose anali Gerisomu+ ndi Eliezere.+ 16 Ana a Gerisomu, mtsogoleri wawo anali Sebueli.+ 17 Ana a Eliezere, mtsogoleri wawo anali Rehabiya.+ Eliezere sanakhalenso ndi ana ena aamuna, koma Rehabiya anali ndi ana ochuluka kwambiri. 18 Ana a Izara,+ mtsogoleri wawo anali Selomiti.+ 19 Ana a Heburoni anali Yeriya amene anali mtsogoleri wawo, wachiwiri wake anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli, ndipo wachinayi anali Yekameamu.+ 20 Ana a Uziyeli+ anali Mika amene anali mtsogoleri wawo, ndipo Isiya anali wachiwiri wake.
21 Ana a Merari+ anali Mali ndi Musi.+ Ana a Mali anali Eleazara+ ndi Kisi. 22 Koma Eleazara anamwalira. Iye analibe ana aamuna koma aakazi. Choncho abale awo, ana a Kisi, anawatenga kukhala akazi awo.+ 23 Ana a Musi analipo atatu. Panali Mali, Ederi, ndi Yeremoti.+
24 Amenewa ndiwo anali ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo.+ Iwowa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo mmodzi ndi mmodzi anapatsidwa udindo potsata mndandanda wa mayina awo. Amenewa anali oti azigwira ntchito yotumikira+ panyumba ya Yehova kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo.+ 25 Davide anachita zimenezi popeza anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wapereka mpumulo kwa anthu ake,+ ndipo iye adzakhala mu Yerusalemu mpaka kalekale.+ 26 Ndipo Alevi sazinyamulanso chihema chopatulika kapena ziwiya zake zilizonse zogwiritsa ntchito potumikira kumeneko.”+ 27 Malinga ndi mawu omaliza+ a Davide, amenewa ndiwo ana a Levi amene anawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo. 28 Ntchito yawo inali yotumidwa ndi ana a Aroni+ pa utumiki wa panyumba ya Yehova m’mabwalo a nyumbayo,+ m’zipinda zodyeramo,+ pa ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika,+ ndiponso pa ntchito yotumikira panyumba ya Mulungu woona. 29 Anali kutumidwanso pa ntchito zokhudza mkate wosanjikiza,+ ufa wosalala+ wa nsembe yambewu, mikate yopyapyala+ yopanda chofufumitsa,+ makeke ophika m’chiwaya,+ ufa wokanya wosakaniza ndi mafuta,+ ndiponso miyezo yosiyanasiyana.+ 30 Analinso kutumikira m’mawa ulionse+ pa nthawi yoimirira+ kuti athokoze+ ndi kutamanda+ Yehova. Analinso kuchita zimenezi madzulo. 31 Anali kutumikiranso nthawi iliyonse yopereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo za chikondwerero.+ Nthawi zonse anali kutumikira popereka nsembezo kwa Yehova, malinga ndi ziwerengero zake, komanso potsata lamulo lake. 32 Ana a Leviwa analinso ndi ntchito yolondera+ chihema chokumanako, malo oyera,+ ndiponso yolondera abale awo, ana a Aroni, pa utumiki wa panyumba ya Yehova.+