2 Mafumu
10 Ku Samariya+ kunali ana aamuna a Ahabu okwanira 70.+ Chotero Yehu analemba makalata n’kuwatumiza kwa atsogoleri+ a ku Yezereeli, kwa akuluakulu,+ ndi kwa anthu amene ankasamalira ana a Ahabu ku Samariya. M’makalatamo analembamo kuti: 2 “Inu muli ndi ana aamuna a mbuye wanu, magaleta ankhondo ndi mahatchi,+ ndiponso mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndi zida zankhondo. Choncho mukangolandira kalatayi, 3 musankhe mwana mmodzi woyenera ndi wolungama pakati pa ana aamuna a mbuye wanu, n’kumuika pampando wachifumu wa bambo ake.+ Kenako mumenyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.”
4 Iwo atalandira makalatawo anachita mantha kwambiri, ndipo anayamba kunena kuti: “Mafumu+ awiri sanathe kulimbana naye, nanga ifeyo tingalimbane naye bwanji?”+ 5 Chotero, amene anali kuyang’anira nyumba ya mfumu, ndi amene anali kuyang’anira mzinda, ndiponso akuluakulu komanso amene ankasamalira+ Ahabu, anatumiza uthenga kwa Yehu, wakuti: “Ife ndife atumiki anu, ndipo tichita chilichonse chimene mungatiuze. Sitisankha munthu aliyense kuti akhale mfumu yathu. Inuyo chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino.”
6 Pamenepo Yehu anawalemberanso kalata yachiwiri kuti: “Ngati muli kumbali yanga+ ndipo ngati muzimvera mawu anga, dulani mitu ya ana aamuna+ a mbuye wanu, ndipo mawa nthawi ngati yomwe ino mubwere nayo kwa ine ku Yezereeli.”+
Ana aamuna a mfumuwo, omwe analipo 70, anali ndi akuluakulu a mumzindawo omwe anali kuwasamalira. 7 Anthuwo atangolandira kalatayo, anatenga ana aamuna a mfumu okwanira 70 aja+ n’kuwapha. Kenako anatenga mitu yawo n’kuiika m’madengu, ndipo anaitumiza kwa Yehu ku Yezereeli. 8 Ndiyeno kunabwera mthenga+ kudzauza Yehu kuti: “Mitu ya ana+ a mfumu ija abwera nayo.” Pamenepo Yehu anati: “Kaiunjikeni milu iwiri pachipata, ndipo ikhale pamenepo kufikira m’mawa.”+ 9 M’mawa kutacha, Yehu anapita kukaima pamaso pa anthu onse. Kenako ananena kuti: “Anthu inu ndinu olungama.+ Ine ndinachitira chiwembu+ mbuye wanga, ndipo ndamupha,+ koma ndani wapha anthu onsewa? 10 Tsopano dziwani kuti mawu onse a Yehova otsutsa nyumba ya Ahabu+ amene Yehova analankhula, adzakwaniritsidwa.+ Yehova wachita zimene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya.”+ 11 Kuwonjezera apo, Yehu anapitiriza kupha onse a m’nyumba ya Ahabu amene anatsala ku Yezereeli, amuna ake onse olemekezeka,+ anzake, ndi ansembe ake,+ mpaka onse anatha.+
12 Kenako Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Ali pa ulendowo, anafika panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. 13 Pamenepo Yehu anakumana ndi abale+ ake a Ahaziya+ mfumu ya Yuda. Atawafunsa kuti, “Ndinu ndani?” iwo anayankha kuti: “Ndife abale ake a Ahaziya. Tikupita kukaona ngati ana a mfumu ndi ana a mfumukazi ali bwino.” 14 Nthawi yomweyo Yehu anati: “Amuna inu, agwireni amoyo+ anthuwa!” Choncho anawagwiradi amoyo n’kukawaphera pachitsime cha panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. Anawapha onse 42 ndipo palibe amene anamusiya ndi moyo.+
15 Yehu atachoka pamenepo, anakumana ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu+ akubwera kudzakumana naye. Atamudalitsa,+ anam’funsa kuti: “Kodi mtima wako ndi wogwirizana ndi ine mopanda chinyengo, monga momwe mtima wanga ulili ndi mtima wako?”+
Yehonadabu anayankha kuti: “Inde, ndi wotero.”
Ndiyeno Yehu anati: “Ngati ndi wotero, ndipatse dzanja lako.”
Choncho Yehonadabu anapereka dzanja lake, ndipo Yehu anamukweza m’galeta lake.+ 16 Kenako anamuuza kuti: “Tiye tipitire limodzi ukaone kuti sindilekerera zoti anthu azipikisana+ ndi Yehova.” Chotero Yehonadabu anapita limodzi ndi anthuwo atakwera m’galeta lankhondo la Yehu. 17 Pomalizira pake Yehu anafika ku Samariya. Kumeneko, iye anapha anthu onse a m’nyumba ya Ahabu amene anatsala ku Samariya, mpaka anawatha onse,+ mogwirizana ndi mawu a Yehova amene anauza Eliya.+
18 Komanso Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi n’kuwauza kuti: “Ahabu anali kupembedza Baala pang’ono,+ koma Yehu apembedza Baala kwambiri. 19 Tsopano itanani aneneri+ onse a Baala, olambira ake onse,+ ndi ansembe ake+ onse kuti abwere kwa ine. Pasapezeke aliyense wotsala chifukwa ndakonza nsembe yaikulu yoti ndipereke kwa Baala. Aliyense amene palibe sakhala ndi moyo.” Koma Yehu anawapusitsa+ n’cholinga choti awononge anthu olambira Baala.
20 Ndiyeno Yehu anati: “Lengezani* kuti kuli msonkhano wapadera wa Baala.” Choncho analengezadi. 21 Kenako Yehu anatumiza uthenga mu Isiraeli+ yense, moti olambira onse a Baala+ anabwera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene sanabwere. Iwo analowa m’kachisi wa Baala ndipo kachisiyo anadzaza kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. 22 Tsopano iye anauza munthu amene anali kuyang’anira chipinda chosungira zovala kuti: “Tulutsa zovala zoti olambira onse a Baala avale.” Choncho iye anawatulutsiradi zovalazo. 23 Kenako Yehu ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu analowa m’kachisi wa Baala. Tsopano Yehu anauza olambira a Baala kuti: “Fufuzani mosamala, ndipo muonetsetse kuti muno musakhale wolambira wa Yehova aliyense, koma olambira a Baala okha.”+ 24 Pomaliza pake, iwo anabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina. Yehu anaika amuna 80 panja oti amuthandize ndipo anawauza kuti: “Aliyense amene athawitse munthu pa anthu amene ndikuwapereka m’manja mwanu, moyo wake ulowa m’malo mwa munthuyo.”+
25 Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, nthawi yomweyo anauza asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta kuti: “Lowani, apheni! Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotuluka panja.”+ Atamva zimenezi, asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta+ aja anayamba kupha anthuwo ndi lupanga n’kumaponyera mitembo yawo panja. Anakafika mpaka m’chipinda chamkati mwa kachisiyo chotchedwa mzinda wa Baala. 26 Kenako anatulutsa zipilala zopatulika+ za m’kachisi wa Baala n’kuzitentha+ zonse. 27 Anagwetsanso chipilala chopatulika cha Baala+ ndi kachisi wa Baala,+ ndipo malowo anawasandutsa zimbudzi+ mpaka lero.
28 Chotero Yehu anachotsa Baala mu Isiraeli. 29 Kungoti iye sanasiye kutsatira machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ Machimo ake anali kulambira ana a ng’ombe agolide.+ Mmodzi wa ana a ng’ombe agolidewo anali ku Beteli, ndipo wina ku Dani.+ 30 Chotero Yehova anauza Yehu kuti: “Pa chifukwa chakuti wachita bwino, mwa kuchita zoyenera pamaso panga,+ ndiponso wachitira nyumba ya Ahabu+ mogwirizana ndi zonse za mumtima mwanga, ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.”+ 31 Koma Yehu sanayesetse kuyenda motsatira malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ Sanapatuke pa machimo a Yerobowamu amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+
32 M’masiku amenewo, Yehova anayamba kulanda dziko la Isiraeli pang’ono ndi pang’ono, ndipo Hazaeli+ anapitiriza kupha anthu m’madera onse a dziko la Isiraeli. 33 Anayambira ku Yorodano chakotulukira dzuwa, dziko lonse la Giliyadi,+ Agadi,+ Arubeni+ ndi Amanase,+ kuyambira ku Aroweli+ yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni, ngakhalenso Giliyadi ndi Basana.+
34 Nkhani zina zokhudza Yehu ndi zonse zimene anachita, ndiponso zochita zake zonse zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 35 Pomalizira pake Yehu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda ku Samariya. Kenako Yehoahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 36 Masiku amene Yehu analamulira Isiraeli ku Samariya, anakwana zaka 28.