2 Mbiri
27 Yotamu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa+ mwana wa Zadoki. 2 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Uziya bambo ake anachita,+ kungoti sanakalowe m’kachisi wa Yehova.+ Koma anthu anali kuchitabe zoipa.+ 3 Iye anamanga chipata chakumtunda+ cha nyumba ya Yehova ndipo pakhoma la Ofeli+ anamangapo zinthu zambiri. 4 M’dera lamapiri la Yuda+ anamangamo mizinda+ ndipo m’dera lankhalango+ anamangamo malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndiponso nsanja.+ 5 Yotamu anamenyana ndi mfumu ya ana a Amoni+ ndipo pomalizira pake anawaposa mphamvu. Choncho chaka chimenecho ana a Amoni anam’patsa matalente a siliva* 100 ndi tirigu+ wokwana miyezo 10,000 ya kori,*+ komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori.+ Izi n’zimene ana a Amoni anamulipira. Anamulipiranso zomwezi m’chaka chachiwiri ndi chachitatu.+ 6 Chotero Yotamu anapitiriza kulimbitsa ufumu wake, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.+
7 Nkhani zina zokhudza Yotamu,+ nkhondo zake ndi njira zake zonse, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. 8 Iye anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+ 9 Pomalizira pake, Yotamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Ahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.