Ekisodo
18 Tsopano Yetero, wansembe wa ku Midiyani, apongozi ake a Mose,+ anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi Aisiraeli, anthu a Mulungu, ndi mmene Yehova anawatulutsira ku Iguputo.+ 2 Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anatenga Zipora, mkazi wa Mose, amene Mose anali atamutumiza kwawo, 3 ndipo anatenganso ana aamuna awiri+ a Zipora. Mwana wina, Mose anamutcha dzina lakuti Gerisomu,*+ ndipo anati: “Chifukwa ndine mlendo m’dziko lino.” 4 Ndipo mwana winayo anamutcha Eliezere,*+ ndipo anati: “Mulungu wa atate anga ndiye mthandizi wanga, pakuti anandipulumutsa kulupanga la Farao.”+
5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, pamodzi ndi ana a Mose awiri aamuna ndi mkazi wake, anapita kwa Mose kuchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+ 6 Ndiyeno anatumiza mawu kwa Mose, kuti: “Ine Yetero, mpongozi wako,+ ndafika pamodzi ndi mkazi wako ndi ana ako awiri.” 7 Nthawi yomweyo Mose anatuluka kukachingamira apongozi ake, ndipo anagwada n’kuwaweramira, kenako n’kuwapsompsona.+ Pamenepo anayamba kulonjerana ndi kufunsana za moyo. Kenako anapita kukalowa m’hema.
8 Motero Mose anawafotokozera apongozi akewo zonse zimene Yehova anachitira Farao ndi Iguputo chifukwa cha Isiraeli.+ Anawafotokozeranso mavuto onse amene anakumana nawo m’njira,+ ndi mmene Yehova anali kuwalanditsira.+ 9 Yetero anasangalala kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli powalanditsa m’manja mwa Aiguputo.+ 10 Choncho Yetero anati: “Yehova adalitsike, iye amene anakulanditsani m’manja mwa Aiguputo ndiponso m’dzanja la Farao, amenenso analanditsa anthuwa m’manja mwa Aiguputo.+ 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndiye wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ Zimenezi zinaoneka Aiguputo atasonyeza kudzikuza pamaso pa Aisiraeli.” 12 Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anabweretsa* nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu.+ Ndipo Aroni ndi akulu onse a Isiraeli anabwera n’kudyera limodzi mkate ndi apongozi ake a Mose, pamaso pa Mulungu woona.+
13 Pa tsiku lotsatira, Mose anakhala pansi monga mwa masiku onse kuti atumikire anthu monga woweruza,+ ndipo anthu anali kubwera ndi kuimirira pamaso pa Mose kuyambira m’mawa mpaka madzulo. 14 Pamenepo apongozi a Mose anaona zonse zimene iye anali kuchitira anthuwo. Ndiyeno anati: “Kodi anthuwa ukuchita nawo chiyani? N’chifukwa chiyani wangokhala wekha kupereka ziweruzo ndipo anthu onse ali chiimire pamaso pako kuyambira m’mawa mpaka madzulo?” 15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa amabwera kwa ine kuti adzamve ziweruzo za Mulungu.+ 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo+ ayenera kubwera nawo kwa ine, ndipo ndiyenera kuwaweruza ndi kuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+
17 Pamenepo apongozi a Mose anamuuza kuti: “Imene ukutsatirayi si njira yabwino. 18 Ndithu mutopa nazo zimenezi, iwe ndi anthu amene uli nawowa, chifukwa ntchito imeneyi yakukulira kwambiri.+ Sungathe kuichita wekha.+ 19 Tsopano mvera zimene ndikufuna kukuuza.+ Ndikulangiza ndipo Mulungu adzakhala nawe.+ Iwe ukhale woimira anthuwa kwa Mulungu woona,+ ndipo ndiwe amene uzipititsa milandu kwa Mulungu woona.+ 20 Ndipo uziwaphunzitsa za malangizo ndi malamulo,+ ndi kuwauza njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.+ 21 Koma mwa anthu onsewa, usankhe amuna oyenerera,+ oopa Mulungu,+ okhulupirika,+ odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kukhala otsogolera anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22 Amenewa ndiwo aziweruza anthu pa nkhani iliyonse yoyenera. Ndiyeno pakakhala nkhani iliyonse yaikulu azibwera nayo kwa iwe,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza aziisamalira. Choncho amunawo athandizane nawe kunyamula mtolowu, kuti udzipeputsire ntchito.+ 23 Ukachita zimenezi, ndipo izi n’zimene Mulungu wakulamula kuchita, pamenepo udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kumahema awo mu mtendere.”+
24 Nthawi yomweyo Mose anamvera zimene apongozi ake anamuuza ndipo anachita zonse zimene ananena.+ 25 Ndipo Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli yense ndi kuwapatsa udindo wokhala atsogoleri a anthu,+ kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26 Motero iwo anali kuweruza anthuwo pa nkhani iliyonse yoyenera. Nkhani yovuta anali kupita nayo kwa Mose,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza anali kuisamalira. 27 Kenako Mose anaperekeza apongozi ake+ ndi kutsanzikana nawo, ndipo iwo anabwerera kwawo.