2 Mbiri
9 Mfumukazi ya ku Sheba+ inamva za Solomo. Choncho inabwera ku Yerusalemu kuti idzamuyese Solomo pomufunsa mafunso ovuta.+ Mfumukaziyo inabwera ndi anthu oiperekeza ambiri, ndiponso ngamila+ zitanyamula mafuta a basamu,+ golide+ wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Inafika kwa Solomo n’kuyamba kumuuza zonse zimene zinali kumtima kwake.+ 2 Solomo anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse.+ Panalibe chimene Solomo analephera kuyankha.+
3 Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+ 4 chakudya cha patebulo pake,+ mmene atumiki ake anali kukhalira pa nthawi ya chakudya, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuchitira, zovala zawo,+ anthu ake operekera zakumwa+ ndi zovala zawo, ndi nsembe zake zopsereza+ zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse,+ inazizira nkhongono ndipo inasowa chonena. 5 Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani za zochita zanu ndi nzeru zanu zimene ndinamva kudziko langa, n’zoonadi.+ 6 Sindinakhulupirire+ mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga,+ ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe ya nzeru zanu zochuluka.+ Mwaposa zinthu zimene ndinamva.+ 7 Odala+ anthu anu, odala atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.+ 8 Adalitsike Yehova Mulungu wanu,+ amene wasangalala+ nanu mwa kukuikani pampando wake wachifumu+ monga mfumu yolamulira m’malo mwa Yehova Mulungu wanu.+ Popeza Mulungu wanu anakonda+ Isiraeli kuti akhalepo mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu yawo,+ kuti muzipereka zigamulo+ ndi kuchita chilungamo.”+
9 Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.+
10 Kuwonjezera pamenepo, atumiki a Hiramu+ ndi atumiki a Solomo amene anabwera ndi golide+ kuchokera ku Ofiri, anabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ndi miyala yamtengo wapatali.+ 11 Mfumuyo inapanga masitepe a nyumba ya Yehova ndi a nyumba ya mfumu+ pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo.+ Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba.+ Zinthu zamtundu umenewu zinali zisanaonekepo m’dziko la Yuda.
12 Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi+ ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha. Solomo anapatsa mfumukaziyo zinthu zoposa zimene inabweretsa kwa iye. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+
13 Golide amene ankabwera kwa Solomo chaka chimodzi, anali wolemera matalente 666,*+ 14 osawerengera golide wa amalonda oyendayenda,+ amalonda ena amene anali kubweretsa katundu, mafumu onse a Aluya,+ ndi abwanamkubwa a m’dzikolo amene anali kubweretsa golide ndi siliva kwa Solomo.
15 Mfumu Solomo inapanga zishango 200 zikuluzikulu zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chachikulu chilichonse anachikuta ndi golide wosakaniza ndi zitsulo zina wolemera masekeli 600.)+ 16 Inapanganso zishango 300 zing’onozing’ono zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chaching’ono chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.)+ Kenako mfumuyo inaika zishangozi m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+
17 Itatero, mfumuyo inapanga mpando wachifumu waukulu wa minyanga ya njovu, n’kuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 18 Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Mpando wachifumuwo unali ndi chopondapo mapazi chagolide (ziwirizi zinali zolumikizana). Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira.+ 19 Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango+ itaimirira, mbali iyi ndi iyi. Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.+ 20 Ziwiya zonse zomweramo+ Mfumu Solomo zinali zagolide,+ ndipo ziwiya zonse za m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali zagolide woyenga bwino. Panalibe chiwiya chasiliva. Siliva sankaoneka ngati kanthu+ m’masiku a Solomo, 21 pakuti zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide, siliva,+ minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.+
22 Chotero Mfumu Solomo inali yolemera kwambiri+ ndiponso yanzeru kwambiri+ kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 23 Mafumu onse a padziko lapansi ankafuna kuonana+ ndi Solomo, kuti amve nzeru zake+ zimene Mulungu woona anaika mumtima mwake.+ 24 Aliyense anali kubweretsa mphatso+ chaka chilichonse monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide,+ zovala,+ zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi, ndi nyulu.*+ 25 Solomo anakhala ndi makola 4,000 a mahatchi.+ Analinso ndi magaleta+ ndi mahatchi ankhondo okwana 12,000. Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 26 Solomo anakhala wolamulira wa mafumu onse kuyambira ku Mtsinje* mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo.+ 27 Kuwonjezera apo, mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva akhale wochuluka kwambiri ngati miyala, ndiponso kuti matabwa a mkungudza+ akhale ochuluka kwambiri+ ngati mitengo ya mkuyu ya ku Sefela.+ 28 Anthu anali kubweretsa mahatchi+ kwa Solomo kuchokera ku Iguputo+ ndi mayiko ena onse.
29 Nkhani zina zokhudza Solomo,+ zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’mawu a mneneri Natani.+ Zalembedwanso mu ulosi wa Ahiya+ Msilo,+ ndiponso m’buku la masomphenya a Ido+ wamasomphenya, lonena za Yerobowamu+ mwana wa Nebati.+ 30 Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu zaka 40. 31 Pomalizira pake Solomo anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide bambo ake.+ Kenako mwana wake Rehobowamu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+