Yobu
33 “Tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga,
Ndipo tcherani khutu ku zonena zanga zonse.
3 Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga,+
Ndipo milomo yanga imanena nzeru moona mtima.+
5 Ngati mungathe ndiyankheni.
Ndifotokozereni mawu anu, ndipo khalani pamalo anu.
8 Komabe inu mwanena m’makutu anga,
Ndipo ine ndakhala ndikumva mawu anu akuti,
9 ‘Ndine woyera, wopanda tchimo,+
Ndilibe chondidetsa, ndilibe cholakwa.+
14 Pakuti Mulungu amalankhula koyamba,
Kenako kachiwiri,+ ngakhale anthu asamvere.
15 Iye amawalankhula m’maloto+ ndi m’masomphenya+ a usiku,
Anthu akakhala m’tulo tofa nato,
Akamagona pabedi.+
16 Pa nthawi imeneyi m’pamene amatsegula anthu makutu,+
Pa chilimbikitso chake kwa iwo, amadindapo chidindo,
17 Kuti achotse munthu pa zochita zake,+
Ndi kuti mwamuna wamphamvu am’bisire kunyada.+
19 Kuwawa kumam’dzudzula iye ali pabedi pake,
Mafupa ake amangokhalira kukangana.
21 Mnofu wake umatha, osaonekanso.
Mafupa ake amene sanali kuoneka amakhala pamtunda.
23 Ngati iye ali ndi mthenga,
Womulankhulira mmodzi pa omulankhulira 1,000,
Kuti auze munthu zimene zili zowongoka,
24 Mulungu amasangalatsidwa naye ndi kunena kuti,
‘M’pulumutseni kuti asapite m’dzenje,+
25 Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata.+
Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.’+
26 Adzadandaulira Mulungu kuti asangalale naye,+
Adzaona nkhope yake akufuula mosangalala,
Ndipo Mulungu adzabwezera kwa munthu kulungama kwa Mulunguyo.
27 Adzaimbira anthu n’kunena kuti,
‘Ndachimwa,+ ndakhotetsa zimene zinali zowongoka,
Ndipo sindinayenere kuchita zimenezi.
29 Mulungutu amachita zinthu zonsezi.
Kawiri kapena katatu konse, amachitira zimenezi mwamuna wamphamvu,
30 Kum’bweza kuti asapite kudzenje,+
Kuti aunikiridwe ndi kuwala kwa anthu amene ali moyo.+
31 Tcherani khutu inu a Yobu. Ndimvereni!
Khalani chete, ndipo ine ndipitiriza kulankhula.
32 Ngati muli ndi mawu, ndiyankheni.
Lankhulani chifukwa ine ndakondwera ndi kulungama kwanu.