-
Salimo 15:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?
Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+
2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,*+
Amene amachita zinthu zabwino+
Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+
Sasintha zimene walonjeza* ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+
-