Salimo
Pemphero la Davide.
17 Imvani dandaulo langa lopempha kuti mundichitire chilungamo, inu Yehova.
Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo.
Imvani pemphero langa lopanda chinyengo.+
3 Mwafufuza mtima wanga, mwandifufuza ngakhale usiku,+
Ndipo mwandiyenga.+
Mudzapeza kuti ndinalibe zolinga zochita choipa chilichonse.
Ndipo pakamwa panga sipanachimwe.
4 Kunena za ntchito za anthu,
Mogwirizana ndi mawu apakamwa panu, ndapewa kuyenda mʼnjira za wachifwamba.+
6 Ine ndikuitana inu, chifukwa mudzandiyankha,+ inu Mulungu.
Tcherani khutu* kwa ine. Imvani mawu anga.+
7 Sonyezani modabwitsa chikondi chanu chokhulupirika,+
Inu Mpulumutsi wa anthu amene amathawira kudzanja lanu lamanja
Kuthawa anthu amene akupandukirani.
10 Mitima yawo siimva chisoni,*
Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.
11 Tsopano adaniwo atizungulira,+
Akufufuza mpata kuti atigwetse.*
12 Ali ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama,
Ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.
13 Nyamukani, inu Yehova, mulimbane naye+ nʼkumugwetsa.
Ndipulumutseni kwa woipayo ndi lupanga lanu.
14 Ndipulumutseni ndi dzanja lanu, inu Yehova,
Kwa anthu amʼdzikoli* amene gawo lawo lili mʼmoyo uno,+
Anthu amene mwawakhutitsa ndi zinthu zabwino zimene mumapereka+
Omwe amasiyira cholowa ana awo aamuna ochuluka.