Kalata Yachiwiri kwa Timoteyo
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu,+ malinga ndi lonjezo la moyo+ loperekedwa kwa ogwirizana ndi Khristu Yesu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo mwana wanga wokondedwa:+
Kukoma mtima kwakukulu, chifundo, ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu+ zikhale nawe.
3 Ndikuyamika Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika+ monga mmene makolo anga+ anachitira, ndipo ndikuuchita ndi chikumbumtima choyera.+ Ndikumuyamika chifukwa chakuti sindiiwala za iwe m’mapembedzero anga,+ usana ndi usiku, 4 ndipo ndikakumbukira misozi yako ndimalakalaka kukuona+ kuti ndidzasangalale kwambiri. 5 Pakuti ndikukumbukira chikhulupiriro+ chopanda chinyengo+ chimene uli nacho, chimene chinayamba kukhazikika mwa agogo ako aakazi a Loisi, ndi mayi ako a Yunike, ndipo ndikukhulupirira kuti chilinso mwa iwe.
6 Pa chifukwa chimenechi, ndikukukumbutsa kuti mphatso+ ya Mulungu imene ili mwa iwe, yomwe unailandira pamene ndinaika manja anga pa iwe,+ uikolezere ngati moto.+ 7 Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wamantha,+ koma wamphamvu,+ wachikondi, ndi woti tiziganiza bwino.+ 8 Chotero, usachite manyazi ndi ntchito yochitira umboni za Ambuye wathu,+ kapena za ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye.+ Khala wokonzeka kumva zowawa+ mu mphamvu ya Mulungu+ chifukwa cha uthenga wabwino. 9 Iye anatipulumutsa+ ndi kutiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu,+ koma mwa chifuniro chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu. Iye anatikomera mtima m’njira imeneyi kalekalelo mwa Khristu Yesu.+ 10 Koma tsopano izi zatsimikizirika bwino chifukwa cha kuonekera+ kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amene wathetsa mphamvu imfa.+ Kudzera mu uthenga wabwino,+ iye watidziwitsa bwinobwino+ mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+ 11 Uthenga wabwino umenewu ndi umene anandiikira kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi.+
12 N’chifukwa chake ndikuvutika chonchi,+ koma sindikuchita manyazi.+ Pakuti ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo ndikukhulupirira kuti adzasunga+ chimene ndachiika m’manja mwake kufikira tsikulo.+ 13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine, komanso chikhulupiriro ndi chikondi zomwe zili mwa Khristu Yesu.+ 14 Chuma chapadera+ chimene anachiika m’manja mwakochi, uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene uli mwa ife.+
15 Iwe ukudziwa kuti anthu onse m’chigawo cha Asia+ andisiya.+ Ena mwa iwo ndi Fugelo ndi Heremogene. 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+ 17 M’malomwake, pamene anali ku Roma, anandifunafuna mwakhama mpaka anandipeza.+ 18 Ambuye amulole kukapeza chifundo+ chochokera kwa Yehova m’tsikulo.+ Za utumiki wonse umene anachita ku Efeso, iwe ukuzidziwa bwino.
2 Choncho iwe mwana wanga,+ pitiriza kupeza mphamvu+ m’kukoma mtima kwakukulu+ kumene kuli mwa Khristu Yesu. 2 Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri+ zokhudza ine, zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.+ 3 Monga msilikali wabwino+ wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kumva zowawa.+ 4 Msilikali amene ali pa nkhondo+ sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita,+ pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali. 5 Komanso, ngati munthu akuchita nawo mpikisano ngakhale pa masewera,+ savekedwa nkhata yaulemerero kumutu akapanda kupikisana nawo motsatira malamulo. 6 Mlimi wogwira ntchito molimbikira ndiye ayenera kukhala woyamba kudya zipatso zimene anabzala.+ 7 Uziganizira zimene ndikukuuzazi nthawi zonse. Ndithudi, Ambuye adzakuthandiza kuzindikira+ zinthu zonse.
8 Kumbukira kuti, malinga ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira,+ Yesu Khristu anauka kwa akufa+ ndipo anali mbewu ya Davide.+ 9 Chifukwa cha uthengawu, ndikumva zowawa mpaka kutsekeredwa m’ndende+ ngati wochita zoipa. Komabe, mawu a Mulungu samangika.+ 10 Pa chifukwa chimenechi, ndikupirirabe zinthu zonse chifukwa cha anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ kuti iwonso alandire chipulumutso chimene chimabwera chifukwa chokhala ogwirizana ndi Khristu Yesu, ndiponso alandire ulemerero wosatha.+ 11 Mawu awa ndi oona,+ akuti: Ndithudi, ngati tinafa naye limodzi, tidzakhalanso ndi moyo limodzi naye.+ 12 Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso limodzi ndi iye monga mafumu.+ Tikamukana,+ iyenso adzatikana, 13 ndipo tikakhala osakhulupirika,+ iye adzakhalabe wokhulupirika, pakuti sangadzikane.
14 Uziwakumbutsa+ zimenezi nthawi zonse. Uziwachenjeza mwamphamvu+ pamaso pa Mulungu,+ kuti asamakangane pa mawu.+ Kuchita zimenezo kulibe phindu m’pang’ono pomwe chifukwa kumawononga chikhulupiriro cha omvetsera. 15 Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka+ pamaso pa Mulungu, wantchito+ wopanda chifukwa chochitira manyazi+ ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+ 16 Koma pewa nkhani zopeka zimene zimaipitsa zinthu zoyera,+ pakuti kusaopa Mulungu kudzachulukirachulukira+ mwa anthu olankhula zotero, 17 ndipo mawu awo adzafalikira ngati chilonda chonyeka.+ Ena mwa anthu amenewo ndi Hemenayo ndi Fileto.+ 18 Anthu amenewa apatuka pa choonadi,+ ponena kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale+ ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena.+ 19 Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire,+ ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova+ aleke kuchita zosalungama.”+
20 M’nyumba yaikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha ayi, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Ziwiya zina zimakhala za ntchito yolemekezeka koma zina zimakhala za ntchito yonyozeka.+ 21 Choncho, ngati munthu akupewa ziwiya za ntchito yonyozekazo, adzakhala chiwiya cha ntchito yolemekezeka, choyera, chofunika kwa mwiniwake, ndi chokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.+ 22 Chotero, thawa zilakolako zaunyamata,+ koma tsatira chilungamo,+ chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere+ limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.+
23 Ndiponso, uzikana mafunso opusa ndi opanda nzeru,+ podziwa kuti amayambitsa mikangano.+ 24 Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu,+ koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.+ Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa,+ wougwira mtima pokumana ndi zoipa,+ 25 ndi wolangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa,+ kuti adziwe choonadi molondola.+ 26 Komanso kuti mwina nzeru zawo zingabwereremo kuti awonjoke mumsampha+ wa Mdyerekezi, poona kuti wawagwira amoyo+ pofuna kukwaniritsa cholinga chake.
3 Koma dziwa kuti, masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.+ 2 Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo,+ osayamika, osakhulupirika,+ 3 osakonda achibale awo,+ osafuna kugwirizana ndi anzawo,+ onenera anzawo zoipa,+ osadziletsa, oopsa,+ osakonda zabwino,+ 4 achiwembu,+ osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada,+ okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu,+ 5 ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu+ koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uwapewe.+ 6 Pakati pa anthu amenewa pamachokera anthu amene amalowerera mozemba m’mabanja,+ ndi kugwira amayi osiyanasiyana kuti akhale akapolo awo. Amayiwo amakhala ofooka, olemedwa ndi machimo, ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana,+ 7 amene amakhala akuphunzira nthawi zonse, koma satha kudziwa choonadi molondola.+
8 Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure+ anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+ 9 Ngakhale zili choncho, iwo sadzapita patali, chifukwa misala yawo idzaonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi misala ya anthu awiri aja.+ 10 Koma iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga. 11 Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo,+ ndi ku Lusitara.+ Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.+ 12 Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13 Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+
14 Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa anthu amene anakuphunzitsa.+ 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke+ kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.+ 16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa,+ kudzudzula,+ kuwongola zinthu+ ndi kulangiza m’chilungamo,+ 17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino+ ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.+
4 Pamaso pa Mulungu ndi pa Khristu Yesu, amene anaikidwiratu kudzaweruza+ amoyo ndi akufa,+ akadzaonekera+ bwinobwino ndiponso akadzabwera mu ufumu wake,+ ndikukulamula mwamphamvu kuti, 2 lalikira mawu.+ Lalikira modzipereka, m’nthawi yabwino+ ndi m’nthawi yovuta.+ Dzudzula,+ tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.+ 3 Pakuti idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso cholondola,+ koma mogwirizana ndi zilakolako zawo, adzadzipezera aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.+ 4 Iwo adzasiya kumvetsera choonadi, n’kutembenukira ku nkhani zonama.+ 5 Koma iwe ukhalebe woganiza bwino+ pa zinthu zonse, imva zowawa,+ gwira ntchito ya mlaliki,*+ ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.+
6 Pakuti ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe yachakumwa,+ ndipo nthawi yakuti ndimasuke+ yatsala pang’ono kukwana. 7 Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.+ Ndasunga chikhulupiriro.+ 8 Kuyambira panopa mpaka m’tsogolo, andisungira chisoti chachifumu chachilungamo.+ Ambuye, woweruza wolungama,+ adzandipatsa mphotoyo+ m’tsikulo.+ Sadzapatsa ine ndekha ayi, komanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.
9 Uchite chilichonse chotheka kuti ubwere kwa ine posachedwa.+ 10 Pakuti Dema+ wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi* ino,+ ndipo wapita ku Tesalonika. Keresike wapita ku Galatiya,+ ndipo Tito wapita ku Dalimatiya. 11 Luka yekha ndiye amene ali ndi ine. Pobwera utengenso Maliko, pakuti iye ndi wofunika kwa ine chifukwa amandithandiza+ pa utumiki wanga. 12 Koma Tukiko+ ndamutuma ku Efeso. 13 Unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa+ kwa Karipo ndi mipukutu, makamaka yazikopa ija.
14 Alekizanda,+ wosula zinthu zamkuwa uja, anandichitira zoipa zambiri. Yehova adzamubwezera malinga ndi ntchito zake,+ 15 ndipo iwenso uchenjere naye, chifukwa anatsutsa mawu athu mwamphamvu.
16 Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.+ Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.+ 17 Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine+ ndi kundipatsa mphamvu,+ kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.+ Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.+ 18 Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse+ ndipo adzandisungira ufumu wake wakumwamba.+ Iye apatsidwe ulemerero mpaka muyaya. Ame.
19 Undiperekere moni kwa Purisika+ ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.+
20 Erasito+ anatsalira ku Korinto,+ koma Terofimo+ ndinamusiya akudwala ku Mileto.+ 21 Uchite chilichonse chotheka kuti ufike kuno nyengo yachisanu isanayambe.
Ebulo, Pude, Lino ndiponso Kalaudiya ndi abale onse, akupereka moni.
22 Ambuye akhale nawe chifukwa cha mzimu umene umaonetsa.+ Kukoma mtima kwake kwakukulu kukhale nanu.