Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 2 Peter 1:1-3:18
  • 2 Petulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Petulo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Petulo

Kalata Yachiwiri ya Petulo

1 Ine Simoni Petulo, kapolo+ ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera anthu amene apeza chikhulupiriro chofanana ndi chathu,+ mwa chilungamo+ cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+

2 Ndikufuna kuti mulandire kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wowonjezereka.+ Kuti muchite zimenezi, mumudziwe molondola+ Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu. 3 Pakuti Mulungu, mwa mphamvu yake, watipatsa kwaulere zinthu zonse zofunika kuti munthu akhale moyo+ wodzipereka kwa Mulungu.+ Talandira zinthu zimenezi kudzera mwa kudziwa molondola za iye amene anatiitana,+ kudzera mu ulemerero+ ndi ubwino wake. 4 Kudzera mwa zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mwa malonjezo amenewa mukhale ndi makhalidwe+ a Mulungu.+ Iye watipatsa kwaulere malonjezo amenewa chifukwa tapulumuka ku khalidwe loipa limene lili m’dzikoli,+ limene limayamba chifukwa cha chilakolako choipa.

5 Pa chifukwa chimenechi, inunso yesetsani mwakhama+ kuwonjezera pa chikhulupiriro chanu makhalidwe abwino,+ pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu,+ 6 pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa+ kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu,+ 7 pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.+ 8 Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo zikusefukira, zidzakutetezani kuti musakhale ozilala kapena osabala zipatso+ pa zimene mukuchita mogwirizana ndi kumudziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.

9 Munthu amene alibe zinthu zimenezi ndi wakhungu, wotseka maso ake kuti asaone kuwala,+ ndipo waiwala+ kuti anayeretsedwa+ ku machimo ake akale. 10 Pa chifukwa chimenechi abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana+ ndi kuwasankha,+ pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono.+ 11 Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo kuti mulowe+ mwaulemerero mu ufumu wosatha+ wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+

12 Pa chifukwa chimenechi, nthawi zonse ndizikukumbutsani+ zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba m’choonadi+ chimene munachilandira.+ 13 Chotero ndikuona kuti n’koyenera kumakugwedezani mwa kukukumbutsani+ pamene ndidakali mumsasa uno,+ 14 popeza ndikudziwa kuti ndatsala pang’ono kutuluka mumsasa wangawu,+ monga momwe Ambuye wathu Yesu Khristu anandisonyezera.+ 15 Choncho nthawi zonse ndizichita chilichonse chotheka, kuti ndikadzachoka+ mudzathe kukumbukira zinthu zimenezi.

16 Ndithudi, pamene ifeyo tinakudziwitsani za mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu ndi za kukhalapo* kwake,+ sitinatengere nkhani zabodza zopekedwa mochenjera ndi anthu,+ koma tinachita zimenezo chifukwa tinachita kuona ndi maso athu ulemerero wake.+ 17 Pakuti iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate,+ pamene mawu anamveka kwa iye kuchokera mu ulemerero waukulu, kuti: “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye.”+ 18 Zoonadi, mawu amenewa tinawamva+ kuchokera kumwamba tili naye limodzi m’phiri loyera.+

19 Choncho mawu aulosiwa+ ndi odalirika kwambiri,+ ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale+ imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda*+ ikadzatuluka. 20 Choyamba, mukudziwa kuti ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu.+ 21 Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu,+ koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu+ motsogoleredwa ndi mzimu woyera.+

2 Komabe, pakati pa anthuwo panadzakhala aneneri onyenga. Momwemonso padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.+ Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga ndipo adzakana ngakhale iye amene anawagula,+ n’kudzibweretsera chiwonongeko chofulumira. 2 Kuwonjezera apo, ambiri adzatsatira+ khalidwe lotayirira+ la aphunzitsiwo, ndipo chifukwa cha amenewa, anthu adzalankhula monyoza njira ya choonadi.+ 3 Komanso chifukwa chosirira mwansanje, adzakudyerani masuku pamutu ndi mawu achinyengo.+ Koma chiweruzo chawo chimene chinagamulidwa kalekale+ chikubwera mofulumira, ndipo chiwonongeko chawo sichikuzengereza.+

4 Ndithu, Mulungu sanalekerere angelo+ amene anachimwa aja osawapatsa chilango, koma mwa kuwaponya mu Tatalasi,*+ anawaika m’maenje a mdima wandiweyani powasungira chiweruzo.+ 5 Anaperekanso chilango padziko lakale lija ndipo sanalilekerere,+ koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo,+ pomupulumutsa pamodzi ndi anthu ena 7,+ pamene anabweretsa chigumula+ padziko la anthu osaopa Mulungu. 6 Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto,+ kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.+ 7 Koma anapulumutsa Loti, munthu wolungama+ amene anavutika mtima kwambiri ndi kulowerera kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayirira.+ 8 Munthu wolungama ameneyo anali kuzunzika tsiku ndi tsiku ndi zimene anali kuona ndi kumva pamene anali kukhala pakati pawo, ndiponso chifukwa cha zochita zawo zosamvera malamulo. 9 Chotero, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.+ Koma anthu osalungama amawasungira tsiku loweruza kuti adzawawononge,+ 10 koma makamaka anthu amene amafunafuna kugonana ndi anthu ena n’cholinga choti awaipitse,+ ndiponso amene amanyoza owalamulira.+

Anthu amenewa ndi opanda mantha ndiponso ndi omva zawo zokha, ndipo sanjenjemera ndi anthu aulemerero. M’malomwake, amalankhula zinthu zowanyoza.+ 11 Koma angelo, ngakhale kuti ndi amphamvu kwambiri, saneneza aphunzitsi onyengawo ndi mawu onyoza,+ pakuti amalemekeza Yehova.+ 12 Ndipo anthu amenewa, mofanana ndi nyama zopanda nzeru zimene zimabadwira kuti zidzagwidwe ndi kuwonongedwa, amalankhula monyoza za zinthu zimene sakuzidziwa,+ moti adzawonongedwa chifukwa cha njira yawo yachiwonongeko, 13 ndipo akudzilakwira okha+ monga mphoto yawo ya kuchita zoipa.+

Iwo amaona kuti kuchita masana zinthu zokhutiritsa chilakolako cha thupi lawo n’kosangalatsa.+ Anthu amenewa ali ngati mawanga ndi zilema pakati panu, ndipo amakondwera kwadzaoneni akamakuphunzitsani zinthu zonyenga pamene akudya nanu limodzi.+ 14 Ali ndi maso odzaza ndi chigololo+ komanso olephera kupewa kuchita tchimo,+ ndipo amakopa anthu apendapenda. Ali ndi mtima wophunzitsidwa kusirira mwansanje.+ Iwo ndi ana otembereredwa.+ 15 Popeza anasiya njira yowongoka, asocheretsedwa. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anakonda mphoto ya kuchita zoipa,+ 16 koma anadzudzulidwa pa cholakwa chake.+ Nyama yosalankhula yonyamula katundu inalankhula ngati munthu+ ndi kulepheretsa zochita zamisala za mneneriyo.+

17 Amenewa ndi akasupe opanda madzi,+ ndi nkhungu yotengeka ndi mphepo yamkuntho, ndipo anawasungira mdima wandiweyani.+ 18 Pakuti amalankhula mawu odzitukumula opanda pake, ndipo pogwiritsa ntchito zilakolako za thupi+ komanso makhalidwe otayirira, amakopa+ amene akungopulumuka+ kumene kwa anthu ochita zolakwa. 19 Pamene akuwalonjeza ufulu,+ eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa.+ Pakuti aliyense amene wagonjetsedwa, amakhala kapolo kwa womugonjetsayo.+ 20 Ndithudi, ngati anapulumuka ku zoipitsa za dzikoli+ mwa kumudziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, koma alowereranso m’zinthu zomwe zija ndi kugonjetsedwa nazo,+ potsirizira pake makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.+ 21 Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njira ya chilungamo,+ kusiyana n’kuidziwa bwinobwino kenako n’kupatuka pa lamulo loyera lomwe anapatsidwa.+ 22 Mwambi woona uja wakwaniritsidwa pa iwo. Mwambiwo umati: “Galu+ wabwerera kumasanzi ake, ndipo nkhumba imene inasambitsidwa yapita kukagubudukanso m’matope.”+

3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yachiwiri imene ndikukulemberani, ndipo monga yoyamba ija,+ ndikulimbikitsa mphamvu zanu zotha kuganiza bwino mwa kukukumbutsani,+ 2 kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kale,+ ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu kudzera mwa atumwi anu.+ 3 Choyamba, inu mukudziwa kuti m’masiku otsiriza+ kudzakhala onyodola+ amene azidzatsatira zilakolako zawo,+ 4 amene azidzati:+ “Kukhalapo* kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti?+ Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.”+

5 Anthu amenewa, mwa kufuna kwawo amalephera kuzindikira mfundo iyi yakuti, panali kumwamba+ kuchokera kalekale, ndipo mwa mawu a Mulungu, dziko lapansi linali loumbika motsendereka pamwamba pa madzi+ ndi pakati pa madzi,+ 6 ndipo mwa zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.+ 7 Ndipo mwa mawu amodzimodziwo, kumwamba+ kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi,+ azisungira moto+ m’tsiku lachiweruzo+ ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.+

8 Komabe okondedwa, musalephere kuzindikira mfundo imodzi iyi yakuti, tsiku limodzi kwa Yehova* lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi.+ 9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+ 10 Komabe, tsiku la Yehova+ lidzafika ngati mbala,+ pamene kumwamba kudzachoka+ ndi mkokomo waukulu,+ koma zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka,+ ndipo dziko lapansi+ ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.+

11 Choncho popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. 12 Muzichita zimenezi poyembekezera+ ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova,+ pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka,+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka. 13 Koma pali kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.+

14 Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga,+ opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.+ 15 Kuwonjezera apo, muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso, monganso mmene m’bale wathu wokondedwa Paulo anakulemberani mogwirizana ndi nzeru+ zimene anapatsidwa.+ 16 Iye anafotokoza zimenezi ngati mmene anachitiranso m’makalata ake onse. Komabe m’makalata akewo muli zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osaphunzitsidwa ndi amaganizo osakhazikika akuzipotoza, ngati mmene amachitiranso ndi Malemba ena onse,+ n’kumadziitanira okha chiwonongeko.

17 Choncho inu okondedwa, popeza mukudziwiratu zimenezi,+ chenjerani kuti musasochere pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulowo, kuopera kuti mungalephere kukhala olimba ndipo mungagwe.+ 18 Ndithu musatero ayi, koma pitirizani kulandira kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+ Kwa iye kukhale ulemerero, kuyambira panopa mpaka muyaya.+

Onani Zakumapeto 8.

“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.

“Tatalasi” ndi mkhalidwe wonyozeka wofanana ndi kukhala m’ndende. Uwu ndiwo mkhalidwe umene Mulungu anaikamo angelo osamvera m’nthawi ya Nowa.”

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena