Kalata Yoyamba ya Petulo
1 Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu,+ amene muli alendo osakhalitsa,+ amene mwamwazikana+ ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia, ndi ku Bituniya. 2 Ndikukulemberani inu amene Mulungu Atate+ anakudziwiranitu mwa kukuyeretsani ndi mzimu+ kuti mukhale omvera ndi owazidwa+ magazi a Yesu Khristu, kuti:+
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere ziwonjezeke kwa inu.+
3 Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano+ kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo+ mwa kuukitsidwa+ kwa Yesu Khristu. 4 Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka,+ chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba,+ 5 inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro.+ Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso,+ ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera+ mu nthawi ya mapeto.+ 6 Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti padakali pano n’koyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana amene akukuchititsani chisoni.+ 7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu, chimene chayesedwa+ ndipo n’chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto,+ chidzakuchititseni kutamandidwa ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, zochita za Yesu Khristu zikadzaululika.*+ 8 Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda.+ Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chachikulu ndiponso chosaneneka, 9 popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.+
10 Aneneri amene analosera+ za kukoma mtima kwakukulu kumene munali kudzasonyezedwa,+ anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndi mosamala.+ 11 Anali kufufuza nyengo+ yake kapena mtundu wa nyengo imene mzimu+ umene unali mwa iwo unali kuwasonyeza yokhudzana ndi Khristu.+ Mzimuwo unali kuchitira umboni za masautso a Khristu+ ndi za ulemerero+ wobwera pambuyo pake. 12 Zinaululidwa kwa iwo kuti sanali kudzitumikira okha,+ koma anali kutumikira inu mwa zinthu zimene tsopano zalengezedwa+ kwa inu. Zimenezi zalengezedwa kwa inu ndi olengeza uthenga wabwino, mwa mzimu woyera+ wotumizidwa kuchokera kumwamba. M’zinthu zimenezi angelo akulakalaka kusuzumiramo.+
13 Konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu,+ khalanibe oganiza bwino,+ ndipo ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwakukulu+ kumene kudzafika kwa inu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ 14 Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira+ zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. 15 Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse,+ 16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+
17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+ 18 Pajatu mukudziwa kuti sizinali zinthu zotha kuvunda,+ siliva kapena golide, zimene zinakumasulani+ ku khalidwe lanu lopanda phindu limene munalilandira kuchokera kwa makolo anu mwa chikhalidwe chanu. 19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali,+ monga a nkhosa yopanda chilema ndi yopanda mawanga,+ magazi a Khristu.+ 20 Iye anadziwikiratu dziko lisanakhazikitsidwe,+ koma anaonekera pa nthawi ya mapeto chifukwa cha inuyo,+ 21 amene kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu,+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kum’patsa ulemerero,+ kuti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu.+
22 Tsopano, popeza mwayeretsa+ miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo,+ kondanani kwambiri kuchokera mumtima.+ 23 Pakuti inu mwabadwa mwatsopano,+ osati kuchokera m’mbewu yotha kuwonongeka,+ koma m’mbewu+ yosatha kuwonongeka,+ kudzera m’mawu+ a Mulungu wamoyo ndi wamuyaya.+ 24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa la udzu.+ Udzuwo umafota ndipo duwalo limathothoka,+ 25 koma mawu a Yehova amakhala kosatha.”+ “Mawu”+ amenewo ndi amene alengezedwa+ kwa inu monga uthenga wabwino.
2 Chotero, lekani zoipa zonse,+ zachinyengo zonse, zachiphamaso, kaduka ndi mtundu uliwonse wa miseche.+ 2 Koma monga makanda obadwa kumene,+ muzilakalaka mkaka wosasukuluka+ umene uli m’mawu a Mulungu, kuti mwa kumwa mkakawo, mukule ndi kukhala oyenera chipulumutso,+ 3 pakuti mwalawa n’kuona kuti Ambuye ndi wokoma mtima.+
4 Pamene mukubwera kwa iye, amene ndiye mwala wamoyo+ umene anthu+ anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso uli wamtengo wapatali kwa iye,+ 5 inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa n’kukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera, n’cholinga chakuti mupereke nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+ 6 Pakuti Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala m’Ziyoni, mwala wochita kusankhidwa mwapadera, wapakona pa maziko, wamtengo wapatali, ndipo aliyense woukhulupirira sadzakhumudwa.”+
7 Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa ndinu okhulupirira, koma kwa osakhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri,”+ 8 komanso “mwala wopunthwitsa ndi thanthwe lokhumudwitsa.”+ Anthu amenewa akupunthwa chifukwa samvera mawu, ndipo anaikidwiratu kale kuti adzatero.+ 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+ 10 Pakuti kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.+ Munali anthu amene sanakuchitireni chifundo, koma tsopano ndinu amene mwachitiridwa chifundo.+
11 Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli,+ ndikukudandaulirani kuti muzipewa zilakolako za thupi+ zimene zili pa nkhondo yolimbana ndi moyo.+ 12 Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli,+ kuti pamene akukunenerani monga anthu ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino,+ adzatamande Mulungu m’tsiku lake loyendera.+
13 Chifukwa cha Ambuye, gonjerani+ dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu:+ kaya mfumu+ chifukwa ili ndi udindo waukulu, 14 kapena nduna chifukwa n’zotumidwa ndi mfumuyo kuti zizipereka chilango kwa ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.+ 15 Pakuti chifuniro cha Mulungu n’chakuti, mwa kuchita zabwino muwatseke pakamwa anthu opanda nzeru olankhula zaumbuli.+ 16 Khalani mfulu,+ koma ufulu wanu usakhale ngati chophimbira zoipa,+ koma monga akapolo a Mulungu.+ 17 Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.+ Kondani gulu lonse la abale,+ opani Mulungu,+ lemekezani mfumu.+
18 Antchito a panyumba akhale ogonjera+ mabwana awo ndi mantha oyenera,+ osati kwa mabwana abwino ndi ololera okha, koma ngakhalenso kwa ovuta kuwakondweretsa. 19 Pakuti zili bwino ngati wina, chifukwa cha chikumbumtima chake kwa Mulungu, akupirira zowawa ndi kuvutika popanda mlandu.+ 20 Kodi kupirira kumenyedwa mbama mutachimwa kuli ndi phindu lanji?+ Koma ngati mukupirira povutika chifukwa cha kuchita zabwino,+ zimenezo n’zabwino kwa Mulungu.+
21 Ndipotu anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu,+ ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.+ 22 Iye sanachite tchimo,+ ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.+ 23 Pamene anali kunenedwa zachipongwe,+ sanabwezere zachipongwe.+ Pamene anali kuvutika,+ sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye+ amene amaweruza molungama. 24 Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 25 Pakuti munali ngati nkhosa zosochera,+ koma tsopano mwabwerera kwa m’busa+ wanu ndi woyang’anira miyoyo yanu.
3 Momwemonso+ inu akazi, muzigonjera+ amuna anu kuti ngati ali osamvera+ mawu akopeke,+ osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu,+ 2 poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera+ ndi ulemu wanu waukulu. 3 Ndipo kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, monga kumanga tsitsi,+ kuvala zodzikongoletsera zagolide,+ kapena kuvala malaya ovala pamwamba. 4 Koma kukhale kwa munthu wobisika+ wamumtima, atavala zovala zosawonongeka,+ ndizo mzimu wabata ndi wofatsa+ umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. 5 Pakuti ndi mmenenso kale akazi oyera amene anali kuyembekeza Mulungu anali kudzikongoletsera. Analinso kugonjera amuna awo, 6 monga mmene Sara analili womvera kwa Abulahamu, ndipo anali kumutcha kuti “mbuyanga.”+ Tsopano inuyo mwakhala ana ake, ndipo mukhalabe ana ake mukapitiriza kuchita zabwino ndi kusaopa chochititsa mantha chilichonse.+
7 Inunso amuna,+ pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino,+ ndi kuwapatsa ulemu+ monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe,+ pakuti mudzalandira nawo limodzi moyo+ umene Mulungu adzakupatseni chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.
8 Pomaliza, nonsenu mukhale amaganizo amodzi,+ omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu,+ ndiponso amaganizo odzichepetsa.+ 9 Osabwezera choipa pa choipa+ kapena chipongwe pa chipongwe,+ koma m’malomwake muzidalitsa,+ chifukwa anakuitanirani njira ya moyo imeneyi, kuti mudzalandire dalitso.
10 Pakuti “amene akufuna kusangalala ndi moyo ndi kuona masiku abwino,+ aletse lilime+ lake kuti lisalankhule zoipa ndi milomo yake kuti isalankhule chinyengo,+ 11 koma aleke zoipa+ ndipo achite zabwino. Ayesetse kupeza mtendere ndi kuusunga.+ 12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+
13 Ndithudi, ndani angakuchitireni zoipa mukakhala odzipereka pochita zabwino?+ 14 Koma ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe odala.+ Musaope zimene iwo amaopa,+ ndipo musade nazo nkhawa.+ 15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.
16 Khalani ndi chikumbumtima chabwino,+ kuti ngakhale azikunenerani zoipa ndi kulankhula monyoza za khalidwe lanu labwino monga otsatira Khristu, adzachite manyazi.+ 17 Pakuti ndi bwino kuvutika chifukwa chochita zabwino,+ ngati Mulungu walola, kusiyana ndi kuvutika chifukwa chochita zoipa.+ 18 Pajatu ngakhale Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi.+ Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama,+ kuti akufikitseni kwa Mulungu.+ Iye anaphedwa m’thupi,+ koma anaukitsidwa monga mzimu.+ 19 Kenako anapita kukalalikira kwa mizimu imene inali m’ndende,+ 20 imene inali yosamvera+ pa nthawi imene Mulungu anali kuleza mtima+ m’masiku a Nowa, pamene chingalawa chinali kupangidwa,+ chimene chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, miyoyo 8 yokha.+
21 Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano.+ Chimenechi ndicho ubatizo, (osati kuchotsa litsiro la m’thupi, koma kupempha chikumbumtima chabwino kwa Mulungu,)+ mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+ 22 Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu,+ pakuti anapita kumwamba, ndipo angelo,+ maulamuliro, ndi mphamvu zinakhala pansi pake.+
4 Choncho, pakuti Khristu anavutika m’thupi,+ nanunso dzikonzekeretseni ndi maganizo omwewo,+ chifukwa munthu amene wavutika m’thupi walekana nawo machimo,+ 2 kuti pamene akukhala ndi moyo m’thupi ku nthawi yotsala ya moyo wake,+ asatsatenso zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.+ 3 Pakuti nthawi+ imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli+ pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira,+ zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo,+ maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.+ 4 Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa,+ anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.+ 5 Koma anthu amenewa adzayankha mlandu kwa yemwe ali+ wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.+ 6 Ndipotu, pa chifukwa chimenechi uthenga wabwino unalengezedwanso kwa akufa,+ kuti aweruzidwe mwa thupi mogwirizana ndi kuona kwa anthu,+ koma akhale ndi moyo mwa mzimu+ mogwirizana ndi kuona kwa Mulungu.
7 Koma mapeto a zinthu zonse ayandikira.+ Choncho khalani oganiza bwino,+ ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.+ 8 Koposa zonse, khalani okondana kwambiri,+ pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.+ 9 Muzicherezana popanda kudandaula.+ 10 Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene wakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.+ 11 Ngati wina akulankhula, alankhule monga mwa mawu opatulika+ a Mulungu. Ngati wina akutumikira,+ atumikire modalira mphamvu imene Mulungu amapereka,+ kuti m’zinthu zonse Mulungu alemekezeke+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ulemerero+ ndi mphamvu, ndi zake mpaka muyaya. Ame.
12 Okondedwa, musadabwe ndi moto umene ukuyaka pakati panu, ngati kuti mukukumana ndi chinthu chachilendo. Motowo ukuyaka pofuna kukuyesani.+ 13 Koma muzikondwera+ pamene mukugawana nawo masautso a Khristu,+ kuti mukasangalalenso ndi kukondwera kwambiri pa nthawi imene ulemerero wake udzaonekere.*+ 14 Ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu,+ ndinu odala+ chifukwa zikusonyeza kuti mzimu waulemerero, umene ndi mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.+
15 Koma pasakhale wina wa inu wovutika+ chifukwa cha kupha munthu, kuba, kuchita choipa china kapena kulowerera nkhani za ena.+ 16 Koma ngati akuvutika+ chifukwa chokhala Mkhristu, asachite manyazi,+ koma apitirize kulemekeza Mulungu m’dzina la Khristuyo. 17 Pakuti ino ndiyo nthawi yoikidwiratu yakuti chiweruzo chiyambe, ndipo chiyambira panyumba ya Mulungu.+ Tsopano ngati chikuyambira pa ife,+ ndiye mapeto a anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu adzakhala otani?+ 18 “Ndipo ngati munthu wolungama adzapulumuka movutikira,+ kodi munthu wosaopa Mulungu ndi wochimwa adzaoneka n’komwe?”+ 19 Choncho amene akuvutika mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, aike miyoyo yawo m’manja mwa Mlengi wokhulupirika, pamene akupitiriza kuchita zabwino.+
5 Choncho, ndikulangiza akulu amene ali pakati panu mowadandaulira, pakuti inenso ndine mkulu+ ngati iwowo. Ndinenso mboni+ ya masautso a Khristu, ndiponso ndidzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere.+ Kwa iwo ndikuti: 2 Wetani+ gulu la nkhosa za Mulungu+ lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.+ Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake,+ koma ndi mtima wonse. 3 Osati mochita ufumu+ pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu,+ koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.+ 4 Ndipo m’busa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosafwifwa,+ yaulemerero.+
5 Chimodzimodzinso inu anyamata. Muzigonjera+ amuna achikulire. Koma nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa,+ chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+
6 Choncho dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.+ 7 Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ pakuti amakuderani nkhawa.+ 8 Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.+ Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.+ 9 Koma inu khalani olimba+ m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye, podziwa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.+ 10 Koma mukavutika kwa kanthawi,+ Mulungu, yemwe amapereka kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanirani ku ulemerero wake wosatha+ kudzera mu mgwirizano wanu+ ndi Khristu, adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani+ ndi kukupatsani mphamvu.+ 11 Mphamvu zikhale kwa iye+ mpaka muyaya. Ame.
12 Ndakulemberani m’mawu ochepa kudzera mwa Silivano,+ m’bale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi+ kuti ndikulimbikitseni ndi kupereka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu.+ 13 Mayi* amene ali ku Babulo,+ wosankhidwa mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14 Patsanani moni popsompsonana mwa chikondi chaubale.+
Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mtendere ukhale nanu.+
Mawu ake enieni, “Yesu Khristu akadzaululika.”
Mawu ake enieni, “akadzaululika.”
Onani Zakumapeto 2.
Mawu ake enieni, “udzaululike.”
Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
“Mawu akuti “mayi,” n’kutheka kuti akutanthauza mpingo.