Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 1 John 1:1-5:21
  • 1 Yohane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Yohane
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Yohane

Kalata Yoyamba ya Yohane

1 Tikukulemberani za iye amene analiko kuyambira pa chiyambi,+ amene amabweretsa mawu opatsa moyo,+ amene tamumva+ ndiponso kumuona ndi maso athu,+ amene tamuyang’anitsitsa+ mwachidwi ndi kumukhudza ndi manja athu.+ 2 (Ife taona ndipo tikuchitira umboni+ ndi kunena kwa inu za moyo wosatha+ umene unachokera kwa Atate ndipo unaonetsedwa kwa ife.)+ 3 Zimene taziona ndi kuzimva, tikukuuzani+ kuti inunso mugwirizane nafe.+ Ndipotu, ifeyo ndife ogwirizana+ ndi Atate ndi Mwana wake Yesu Khristu.+ 4 Choncho tikulemba zimenezi kuti tikhale ndi chimwemwe chachikulu.+

5 Umenewu ndi uthenga umene taumva kuchokera kwa iye ndipo tikuulengeza kwa inu,+ kuti Mulungu ndiye kuwala+ ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.+ 6 Ngati tinena kuti: “Ndife ogwirizana naye,” koma tikupitiriza kuyenda mu mdima,+ ndiye kuti tikunama ndipo sitikuchita choonadi.+ 7 Komatu, ngati tikuyenda m’kuunika ngati mmene iye alili m’kuunika,+ ndiye kuti ndife ogwirizana,+ ndipo magazi+ a Yesu Mwana wake akutiyeretsa+ ku uchimo wonse.+

8 Tikanena kuti: “Tilibe uchimo,”+ ndiye kuti tikudzinamiza+ ndipo mwa ife mulibe choonadi. 9 Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu,+ adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.+ 10 Tikanena kuti: “Sitinachimwe,” ndiye kuti tikumuchititsa iye kukhala wabodza, ndipo mawu ake sali mwa ife.+

2 Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.+ Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi+ wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.+ 2 Iye ndi nsembe+ yophimba+ machimo athu.+ Osati athu+ okha, komanso a dziko lonse lapansi.+ 3 Tikapitiriza kusunga malamulo ake ndiye kuti tikumudziwa.+ 4 Munthu amene amanena kuti: “Ine ndikumudziwa,”+ koma sasunga malamulo ake,+ ameneyo ndi wabodza, ndipo mwa munthu ameneyo mulibe choonadi.+ 5 Koma aliyense wosunga mawu ake,+ amasonyeza kuti amakondadi Mulungu.+ Chifukwa cha zimenezi, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+ 6 Amene amanena kuti ndi wogwirizana+ naye, ayenera kupitiriza kuyenda mmene iyeyo anayendera.+

7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lamulo lakale+ limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi.+ Lamulo lakale limeneli ndiwo mawu amene munamva. 8 Komabe, ndikukulemberani lamulo latsopano limene Yesu analitsatira, limenenso inuyo mukulitsatira, chifukwa chakuti mdima+ ukupita ndipo kuwala kwenikweni+ kwayamba kale kuunika.

9 Amene amanena kuti ali m’kuunika koma amadana+ ndi m’bale wake, ndiye kuti ali mu mdima mpaka pano.+ 10 Amene amakonda m’bale wake ndiye kuti ali m’kuunika,+ ndipo palibe chimene chingamukhumudwitse.+ 11 Koma amene amadana ndi m’bale wake ndiye kuti ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdimawo,+ ndiponso sakudziwa kumene akupita+ chifukwa maso ake achita khungu chifukwa cha mdimawo.

12 Ndikukulemberani inu ana anga okondedwa, pakuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.+ 13 Ndikulembera abambo inu, chifukwa mukumudziwa amene wakhala alipo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulemberanso inu anyamata+ chifukwa mwagonjetsa woipayo.+ Ndikulembera inu ana+ chifukwa mukuwadziwa Atate.+ 14 Ndikulembera inu abambo+ chifukwa mukumudziwa iye amene wakhalapo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba+ ndipo mawu a Mulungu akhaladi mwa inu+ ndiponso mwagonjetsa woipayo.+

15 Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko.+ Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.+ 16 Pakuti chilichonse cha m’dziko,+ monga chilakolako cha thupi,+ chilakolako cha maso+ ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,+ sizichokera kwa Atate, koma kudziko.+ 17 Ndiponso, dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake,+ koma wochita chifuniro+ cha Mulungu adzakhala kosatha.+

18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto,+ ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera,+ ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri.+ Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. 19 Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu,+ chifukwa akanakhala a m’gulu lathu, akanakhalabe ndi ife.+ Sikuti onse ali m’gulu lathu ayi, ndipo iwo achoka m’gulu lathu, kuti zimenezi zidziwike.+ 20 Inu munadzozedwa ndi woyerayo,+ ndipo nonsenu ndinu odziwa choonadi.+ 21 Ndikukulemberani izi, osati chifukwa chakuti simudziwa choonadi,+ koma chifukwa chakuti mukuchidziwa,+ ndiponso chifukwa chakuti palibe bodza lililonse limene limachokera m’choonadi.+

22 Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?+ Ameneyu ndiye wokana Khristu,+ amene amakana Atate ndi Mwana.+ 23 Aliyense amene amakana Mwana sangakhale pa ubwenzi ndi Atate.+ Amene wavomereza+ Mwana amakhalanso pa ubwenzi ndi Atate.+ 24 Koma zimene inu munamva pa chiyambi zikhalebe mumtima mwanu.+ Zimene munamva pa chiyambi zikakhalabe mumtima mwanu, mudzakhalanso ogwirizana+ ndi Mwana ndi Atate.+ 25 Ndipotu, lonjezo limene iye watipatsa ndi la moyo wosatha.+

26 Ndikukulemberani za anthu amene akufuna kukusocheretsani.+ 27 Inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu+ ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Chotero simukufunikira wina aliyense kuti azikuphunzitsani,+ koma popeza kuti munadzozedwadi moona+ osati monama, chifukwa cha kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse.+ Monga mmene mwaphunzitsidwira, pitirizani kukhala ogwirizana+ naye. 28 Tsopano inu ana anga okondedwa,+ khalanibe ogwirizana+ naye, kuti akadzaonetsedwa,+ tidzakhale ndi ufulu wa kulankhula.+ Kutinso tisadzachititsidwe manyazi ndi kuchotsedwa kwa iye pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake. 29 Ngati mwadziwa kuti iye ndi wolungama,+ mwadziwa kuti aliyense wochita zolungama anabadwa kuchokera kwa iye.+

3 Taganizirani za chikondi chachikulu+ chimene Atate watisonyeza. Watitchula kuti ndife ana a Mulungu,+ ndipo ndifedi ana ake. N’chifukwa chake dziko+ silitidziwa, pakuti silimudziwa iyeyo.+ 2 Okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu,+ koma padakali pano sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani.+ Tikudziwa kuti akadzaonekera,+ tidzakhala ngati iyeyo,+ chifukwa tidzamuona mmene alili.+ 3 Ndipo aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi mwa iye, amadziyeretsa+ pakuti iye ndi woyera.+

4 Aliyense amene amachita tchimo+ samvera malamulo,+ choncho tchimo+ ndilo kusamvera malamulo. 5 Inu mukudziwanso kuti iye anaonekera kuti achotse machimo athu,+ ndipo mwa iye mulibe tchimo.+ 6 Aliyense amene ali wogwirizana+ ndi Yesu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo.+ Aliyense amene amachita tchimo ndiye kuti sanamuone kapena kumudziwa.+ 7 Ana inu, wina asakusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama ngati mmene Yesu alili wolungama.+ 8 Amene amachitabe tchimo anachokera kwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi.+ Choncho, Mwana wa Mulungu anaonekera+ kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.+

9 Aliyense amene ali mwana wa Mulungu sapitiriza kuchita tchimo,+ chifukwa mbewu ya Mulungu yopatsa moyo imakhalabe mwa munthu ameneyo, ndipo sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.+ 10 Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama+ sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake.+ 11 Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambira pa chiyambi,+ kuti tizikondana,+ 12 osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha+ m’bale wake. N’chifukwa chiyani iye anapha m’bale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za m’bale wake zinali zolungama.+

13 Abale, musadabwe kuti dziko limakudani.+ 14 Tikudziwa kuti tinali akufa koma tsopano ndife amoyo+ chifukwa timakonda abale athu.+ Amene sakonda m’bale wake ndiye kuti adakali mu imfa.+ 15 Aliyense amene amadana+ ndi m’bale wake ndi wopha munthu,+ ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu+ sadzalandira moyo wosatha.+ 16 Tadziwa chikondi+ chifukwa chakuti iye anapereka moyo wake chifukwa cha ife,+ ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.+ 17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+ 18 Ana anga okondedwa,+ tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha,+ koma tizisonyezana chikondi chenicheni+ m’zochita zathu.+

19 Mwa njira imeneyi tidzadziwa kuti ndife ochokera m’choonadi,+ ndipo tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu 20 pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse,+ chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.+ 21 Okondedwa, ngati mitima yathu sititsutsa, tikhoza kulankhula momasuka ndi Mulungu,+ 22 ndipo chilichonse chimene tingapemphe, iye adzatipatsa,+ chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zinthu zomukondweretsa.+ 23 Lamulo lake ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu+ ndiponso tizikondana,+ monga mmene iye anatilamulira. 24 Komanso, munthu wosunga malamulo ake amakhalabe wogwirizana naye.+ Iyenso amakhala wogwirizana ndi munthuyo, ndipo chifukwa cha mzimu+ umene anatipatsa, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+

4 Okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa,+ koma muziyesa mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokeradi kwa Mulungu,+ chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.+

2 Kuti tidziwe ngati mawu ali ouziridwa ndiponso ochokera kwa Mulungu,+ timadziwira izi: Mawuwo amavomereza zoti Yesu Khristu anabwera monga munthu.+ 3 Koma mawu alionse ouziridwa amene amatsutsa zoti Yesu anabwera monga munthu, amenewo si ochokera kwa Mulungu,+ ndipo ndi ouziridwa ndi wokana Khristu amene munamva kuti akubwera,+ ndipo tsopano ali kale m’dziko.+

4 Ana okondedwa, inu ndinu ochokera kwa Mulungu, ndipo mwagonjetsa anthu amenewo,+ chifukwa amene muli ogwirizana+ naye ndi wamkulu+ kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.+ 5 Iwo ndi ochokera m’dziko,+ n’chifukwa chake amalankhula zochokera m’dziko ndipo dziko limawamvera.+ 6 Ife ndife ochokera kwa Mulungu.+ Amene amadziwa Mulungu amatimvera,+ ndipo amene sachokera kwa Mulungu satimvera.+ Mmenemu ndi mmene timadziwira mawu ouziridwa oona kapena abodza.+

7 Okondedwa, tiyeni tipitirize kukondana,+ chifukwa chikondi+ chimachokera kwa Mulungu,+ ndipo aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu ndipo akudziwa Mulungu.+ 8 Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.+ 9 Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake+ pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha+ kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.+ 10 Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe+ yophimba+ machimo athu.+

11 Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tiyenera kukondana.+ 12 Palibe amene anaonapo Mulungu.+ Tikapitiriza kukondana, Mulungu apitiriza kukhala mwa ife ndipo chikondi chake kwa ife chikhala chokwanira.+ 13 Tikudziwa kuti ndife ogwirizana+ naye, ndiponso iye ndi wogwirizana ndi ife+ chifukwa watipatsa mzimu wake.+ 14 Komanso ife taona+ ndipo tikuchitira umboni+ kuti Atate anatumiza Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko.+ 15 Aliyense amene amavomereza kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu,+ amakhala wogwirizana ndi Mulungu ndipo Mulungu amakhala wogwirizana naye.+ 16 Ife tikudziwa ndipo tikukhulupirira za chikondi+ chimene Mulungu ali nacho kwa ife.

Mulungu ndiye chikondi,+ ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi,+ amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana+ naye. 17 Chikondi chimenechi chakhala chokwanira kwa ife kuti tidzathe kulankhula momasuka+ m’tsiku lachiweruzo,+ chifukwa mmene Yesu Khristu alili, ndi mmenenso ife tilili m’dzikoli.+ 18 M’chikondi mulibe mantha,+ koma chikondi chimene chili chokwanira chimathetsa mantha,+ chifukwa mantha amachititsa munthu kukhala womangika. Amene ali ndi mantha, chikondi chake si chokwanira.+ 19 Koma ife timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.+

20 Ngati wina amanena kuti: “Ndimakonda Mulungu,” koma amadana ndi m’bale wake, ndiye kuti ndi wabodza.+ Pakuti amene sakonda m’bale wake+ amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.+ 21 Ndipo iye anatipatsa lamulo ili lakuti,+ munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.+

5 Onse amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, ndi ana a Mulungu,+ ndipo onse amene amakonda Atate amakondanso mwana wake.+ 2 Tikamakonda+ ana a Mulungu,+ ndiye kuti tikukonda Mulungu ndiponso tikusunga malamulo ake.+ 3 Chifukwa kukonda+ Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo+ ndi osalemetsa.+ 4 Onse amene ali ana+ a Mulungu amagonjetsa dziko.+ Ndipo tagonjetsa+ dziko ndi chikhulupiriro chathu.+

5 Kodi ndani amene amagonjetsa+ dziko?+ Kodi si amene amakhulupirira+ kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?+ 6 Ameneyu ndi Yesu Khristu, amene anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi. Sanabwere kudzera mwa madzi+ okha, koma anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi.+ Ndipo mzimu+ ndi umene ukuchitira umboni, chifukwa mzimu ndiwo choonadi. 7 Pakuti pali mboni zitatu, 8 mzimu,+ madzi,+ ndi magazi,+ ndipo zitatuzi n’zogwirizana.+

9 Ngati timakhulupirira umboni umene anthu amapereka,+ n’zoonekeratu kuti umboni umene Mulungu amapereka ndi woposa umboni wa anthu. Timakhulupirira umboni wa Mulungu chifukwa chakuti amachitira umboni+ za Mwana wake. 10 Munthu wokhulupirira Mwana wa Mulungu ndiye kuti walandira umboni+ umene wapatsidwa. Munthu wosakhulupirira Mulungu ndiye kuti akumuona ngati wonama,+ chifukwa sanakhulupirire kuti zimene Mulungu wanena+ zokhudza Mwana wake, ndi zoona.+ 11 Umboni umene waperekedwa ndi wakuti, Mulungu anatipatsa moyo wosatha,+ ndipo tinaulandira kudzera mwa Mwana wake.+ 12 Munthu amene wavomereza Mwana ndiye kuti ali ndi moyo umenewu ndipo amene sanavomereze Mwana wa Mulungu alibe moyo umenewu.+

13 Ndikukulemberani izi kuti mudziwe kuti inu amene mumakhulupirira m’dzina la Mwana wa Mulungu+ muli ndi moyo wosatha.+ 14 Ifetu timamudalira+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.+ 15 Komanso, popeza timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse,+ timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.+

16 Ngati wina waona m’bale wake akuchita tchimo losabweretsa imfa,+ amupempherere, ndipo Mulungu adzamupatsa moyo.+ Panotu ndikunena za ochita machimo osabweretsa imfa.+ Koma palinso tchimo lobweretsa imfa. Ndipo sindikunena kuti mupempherere munthu amene wachita tchimo loterolo.+ 17 Kusalungama kulikonse ndi tchimo.+ Komabe pali tchimo limene silibweretsa imfa.

18 Tikudziwa kuti munthu aliyense amene ali mwana wa Mulungu+ sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, koma mwana*+ wa Mulungu amamuyang’anira, ndipo woipayo samugwira.+ 19 Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu,+ koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.+ 20 Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anabwera,+ ndipo anatipatsa nzeru+ kuti timudziwe woonayo.+ Ndipo ife ndife ogwirizana+ ndi woonayo, kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona+ ndiponso wopereka moyo wosatha.+ 21 Inu ana okondedwa, pewani mafano.+

Onani Zakumapeto 8.

“Mwana” ameneyu ndi Yesu Khristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena