Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Lamentations 1:1-5:22
  • Maliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maliro
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Maliro

MALIRO

א [Aleph]*

1 Yerusalemu amene anali ndi anthu ambiri tsopano watsala yekhayekha wopanda anthu.+

Amene anali ndi anthu ambiri poyerekeza ndi mitundu ina, wakhala ngati mkazi wamasiye.+

Amene anali wolemekezeka pakati pa zigawo zina wayamba kugwira ntchito yaukapolo.+

ב [Beth]

 2 Iye akulira kwambiri usiku+ ndipo misozi ikutsika mʼmasaya ake.

Pa anthu onse amene ankamukonda, palibe aliyense amene akumutonthoza.+

Anzake onse amuchitira zachinyengo+ ndipo asanduka adani ake.

ג [Gimel]

 3 Yuda watengedwa kupita kudziko lina+ ndipo akuvutika komanso akugwira ntchito yaukapolo.+

Iye akuyenera kukhala pakati pa mitundu ina ya anthu+ ndipo sanapeze malo oti azikhala mwamtendere.

Onse amene amamufunafuna amupeza ali pamavuto.

ד [Daleth]

 4 Misewu yopita ku Ziyoni ikulira chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+

Mageti ake onse awonongedwa.+ Ansembe ake akuusa moyo.

Anamwali* ake agwidwa ndi chisoni ndipo iyeyo akumva ululu mumtima.

ה [He]

 5 Tsopano adani ake akumulamulira. Iwo sakuda nkhawa.+

Yehova wamuchititsa kuti akhale ndi chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo ake.+

Ana ake agwidwa ndi adani ndipo atengedwa kupita ku ukapolo.+

ו [Waw]

 6 Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni* wamuchokera.+

Akalonga ake ali ngati mbawala zamphongo zimene zikusowa msipu,

Ndipo akuyenda mofooka pamaso pa amene akuwathamangitsa.

ז [Zayin]

 7 Pa nthawi imene ankazunzika komanso pamene ankasowa pokhala, Yerusalemu anakumbukira

Zinthu zake zonse zamtengo wapatali zimene anali nazo kalekale.+

Anthu ake atagwidwa ndi adani moti panalibe munthu woti amuthandize,+

Adaniwo anamuona ndipo anamuseka* chifukwa chakuti wagwa.+

ח [Heth]

 8 Yerusalemu wachita tchimo lalikulu.+

Nʼchifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.

Anthu onse amene ankamulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chochititsa manyazi, chifukwa aona maliseche ake.+

Iyenso akulira+ ndipo watembenukira kumbali chifukwa cha manyazi.

ט [Teth]

 9 Zovala zake zadetsedwa.

Iye sanaganizire za tsogolo lake.+

Wagwa modabwitsa ndipo palibe aliyense woti amutonthoze.

Inu Yehova, onani kuvutika kwanga, chifukwa mdani wanga akudzitukumula.+

י [Yod]

10 Mdani wamulanda zinthu zake zonse zamtengo wapatali.+

Yerusalemu waona anthu a mitundu ina akulowa mʼmalo ake opatulika,+

Mitundu imene munalamula kuti isamalowe mumpingo wanu.

כ [Kaph]

11 Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+

Asinthanitsa zinthu zawo zamtengo wapatali ndi chakudya kuti akhale ndi moyo.

Inu Yehova ndiyangʼaneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi* wachabechabe.

ל [Lamed]

12 Inu nonse amene mukudutsa munsewu, kodi mukuona ngati imeneyi ndi nkhani yaingʼono?

Ndiyangʼaneni kuti muone.

Kodi palinso ululu wina woposa ululu umene ndikumva chifukwa cholangidwa,

Ululu umene Yehova wachititsa kuti ndiumve pa tsiku la mkwiyo wake woyaka moto?+

מ [Mem]

13 Iye watumiza moto mʼmafupa mwanga+ kuchokera kumwamba ndipo wafooketsa fupa lililonse.

Watchera ukonde kuti ukole mapazi anga. Wandikakamiza kuti ndibwerere mʼmbuyo.

Wandichititsa kuti ndikhale mkazi amene wasiyidwa yekhayekha.

Ndikudwala tsiku lonse.

נ [Nun]

14 Machimo anga amangidwa mʼkhosi mwanga ngati goli. Iye wawamanga mwamphamvu ndi dzanja lake.

Aikidwa mʼkhosi mwanga moti mphamvu zanga zatha.

Yehova wandipereka mʼmanja mwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.+

ס [Samekh]

15 Yehova wandichotsera anthu anga onse amphamvu nʼkuwakankhira pambali.+

Wandiitanitsira msonkhano kuti aphwanye anyamata anga.+

Yehova wapondaponda namwali, mwana wamkazi wa Yuda, moponderamo mphesa.+

ע [Ayin]

16 Ndikulira chifukwa cha zinthu zimenezi.+ Misozi ikutuluka mʼmaso mwanga.

Chifukwa aliyense amene akananditonthoza kapena kunditsitsimula, ali kutali ndi ine.

Ana anga awonongedwa ndipo mdani wanga wapambana.

פ [Pe]

17 Ziyoni watambasula manja ake.+ Palibe aliyense woti amutonthoze.

Yehova walamula adani onse a Yakobo amene amuzungulira kuti amuukire.+

Yerusalemu wakhala chinthu chonyansa kwa iwo.+

צ [Tsade]

18 Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndapandukira malamulo ake.*+

Mvetserani, inu anthu a mitundu yonse ndipo muone ululu umene ndikumva.

Anamwali* anga ndi anyamata anga atengedwa kupita ku ukapolo.+

ק [Qoph]

19 Ndaitana anthu amene ankandikonda, koma anthuwo andichitira zachinyengo.+

Ansembe anga ndiponso akuluakulu atha mumzinda.

Atha pamene amafunafuna chakudya choti adye kuti akhale ndi moyo.+

ר [Resh]

20 Taonani, inu Yehova. Ine ndili pamavuto aakulu.

Mʼmimba mwanga mukubwadamuka.

Mtima wanga wasweka, chifukwa ndapanduka kwambiri.+

Panja, lupanga lapha ana anga.+ Mʼnyumba, anthu akufanso.

ש [Shin]

21 Anthu amva mmene ndikuusira moyo, koma palibe aliyense woti anditonthoze.

Adani anga onse amva za tsoka langa.

Iwo akusangalala chifukwa inu mwatibweretsera tsoka.+

Koma inu mubweretsadi tsiku limene munanena,+ kuti iwowo adzakhale ngati ine.+

ת [Taw]

22 Kuipa kwawo konse kuonekere pamaso panu ndipo muwalange koopsa,+

Ngati mmene mwandilangira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse.

Ndikuusa moyo kwambiri ndipo mtima wanga ukudwala.

א [Aleph]

2 Yehova waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni* mumtambo wa mkwiyo wake.

Iye waponya pansi kukongola kwa Isiraeli kuchokera kumwamba kupita padziko lapansi.+

Sanakumbukire chopondapo mapazi ake+ pa tsiku la mkwiyo wake.

ב [Beth]

 2 Yehova wameza mopanda chifundo malo onse amene Yakobo ankakhala.

Mokwiya kwambiri, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri ya mwana wamkazi wa Yuda.+

Iye wagwetsera pansi komanso kuipitsa ufumu+ ndi akalonga ake.+

ג [Gimel]

 3 Iye wathetsa mphamvu zonse za* Isiraeli atakwiya kwambiri.

Adani athu atatiukira, iye sanatithandize,+

Ndipo mkwiyo wakewo unapitiriza kuyakira Yakobo ngati moto umene wawononga chilichonse chimene chili pafupi.+

ד [Daleth]

 4 Wakunga* uta wake ngati mdani. Wakweza dzanja lake lamanja kuti atiukire ngati ndife adani ake.+

Iye anapitiriza kupha anthu onse ofunika kwambiri.+

Anakhuthulira ukali wake ngati moto+ mutenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.+

ה [He]

 5 Yehova wakhala ngati mdani.+

Wameza Isiraeli.

Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli.

Wawononga malo ake onse okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.

Ndipo wachititsa kuti paliponse pakhale maliro komanso kulira mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda.

ו [Waw]

 6 Iye wapasula msasa wake+ ngati chisimba chamʼmunda.

Iye wathetsa zikondwerero zake.+

Yehova wachititsa kuti zikondwerero ndi sabata ziiwalike mu Ziyoni,

Ndipo chifukwa cha mkwiyo wake waukulu sakuganiziranso za mfumu ndi wansembe.+

ז [Zayin]

 7 Yehova wakana guwa lake lansembe.

Iye wasiya malo ake opatulika.+

Wapereka mʼmanja mwa adani makoma a nsanja zake zotetezeka.+

Adaniwo afuula mʼnyumba ya Yehova+ ngati pa tsiku lachikondwerero.

ח [Heth]

 8 Yehova watsimikiza kuti awononge mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+

Watambasula chingwe choyezera.+

Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko.

Wachititsa kuti malo okwera omenyerapo nkhondo ndi mpanda zilire.

Zonse pamodzi zachititsidwa kuti zisakhalenso ndi mphamvu.

ט [Teth]

 9 Mageti ake amira munthaka.+

Wawononga ndi kuthyolathyola mipiringidzo yake.

Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa anthu a mitundu ina.+

Anthu sakutsatira malamulo.* Ndipo ngakhale aneneri ake sakuona masomphenya ochokera kwa Yehova.+

י [Yod]

10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi ndipo akhala chete.+

Iwo athira fumbi pamitu yawo ndipo avala ziguduli.+

Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa mitu yawo mpaka pansi.

כ [Kaph]

11 Maso anga atopa ndi kugwetsa misozi.+

Mʼmimba mwanga mukubwadamuka.

Chiwindi changa chakhuthulidwa pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+

Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda akukomoka mʼmabwalo a mzinda.+

ל [Lamed]

12 Iwo ankafunsa amayi awo kuti: “Kodi chakudya ndi vinyo zili kuti?”+

Pamene ankakomoka mʼmabwalo a mzinda ngati munthu amene wavulazidwa,

Ndiponso pamene moyo wawo unkachoka ali mʼmanja mwa mayi awo.

מ [Mem]

13 Kodi ndikupatse umboni wotani,

Kapena kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?*

Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?

Chifukwa kuwonongeka kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja.+ Ndani angakuchiritse?+

נ [Nun]

14 Masomphenya amene aneneri anu anaona ndi abodza komanso achabechabe,+

Ndipo sanaulule zolakwa zanu nʼcholinga choti musatengedwe kupita ku ukapolo,+

Koma ankaona masomphenya abodza komanso okusocheretsani.+

ס [Samekh]

15 Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba mʼmanja monyoza.+

Akuimba mluzu modabwa+ ndipo akupukusira mitu yawo mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti:

“Kodi uwu ndi mzinda umene ankaunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri ndipo anthu padziko lonse lapansi amasangalala nawoʼ?”+

פ [Pe]

16 Adani ako onse atsegula pakamwa pawo.

Akuimba mluzu ndi kukukuta mano nʼkumanena kuti: “Ameneyu tamumeza.+

Lero ndi tsiku limene takhala tikuliyembekezera.+ Lafika ndipo taliona!”+

ע [Ayin]

17 Yehova wachita zimene ankafuna.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+

Zimene analamula kalekale.+

Wakuwononga mopanda chisoni.+

Wachititsa kuti adani ako asangalale chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wawonjezera mphamvu* za adani ako.

צ [Tsade]

18 Anthu akulirira Yehova ndi mtima wawo wonse, iwe mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.

Misozi iyende ngati mtsinje masana ndi usiku.

Usapume ndipo diso* lako lisasiye kulira.

ק [Qoph]

19 Nyamuka! Lira mofuula usiku, pa nthawi yoyamba ulonda.

Khuthula mtima wako pamaso pa Yehova ngati madzi.

Pemphera utakweza manja ako kwa iye chifukwa cha ana ako,

Amene akukomoka ndi njala pamphambano za misewu yonse.+

ר [Resh]

20 Inu Yehova, yangʼanani kuti muone amene mwamulanga mwaukali.

Kodi azimayi azidya ana awo amene* abereka, ana awo athanzi?+

Kapena kodi ansembe ndi aneneri aziphedwa mʼmalo opatulika a Yehova?+

ש [Shin]

21 Anyamata ndi amuna okalamba afa ndipo mitembo yawo ili pansi mʼmisewu.+

Anamwali* anga ndi anyamata anga aphedwa ndi lupanga.+

Mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu. Mwawapha mopanda chisoni.+

ת [Taw]

22 Munaitana zoopsa kuchokera kumbali zonse ngati kuti mukuitana anthu pa tsiku lachikondwerero.+

Pa tsiku la mkwiyo wa Yehova panalibe aliyense amene anathawa kapena kupulumuka.+

Ana onse amene ndinabereka komanso kuwalera, mdani wanga anawapha.+

א [Aleph]

3 Ine ndine munthu amene ndakumana ndi mavuto chifukwa Mulungu anatikwiyira kwambiri ndipo anatilanga.

 2 Iye wandithamangitsa ndipo wachititsa kuti ndiyende mumdima, osati mʼmalo owala.+

 3 Ndithudi, iye amandimenya ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.+

ב [Beth]

 4 Wachititsa kuti mnofu ndi khungu langa ziwonongeke.

Iye waphwanya mafupa anga.

 5 Wandizungulira kumbali zonse. Wachititsa kuti poizoni wowawa+ komanso mavuto zindizungulire.

 6 Wandikakamiza kuti ndikhale mʼmalo amdima, ngati anthu oti anafa kalekale.

ג [Gimel]

 7 Wandimangira mpanda kuti ndisathawe,

Wandimanga ndi maunyolo olemera akopa.*+

 8 Komanso ndikalira modandaula kuti andithandize, iye amakana* pemphero langa.+

 9 Watseka njira zanga ndi miyala yosema.

Wachititsa njira zanga kuti zikhale zovuta kuyendamo.+

ד [Daleth]

10 Iye wandibisalira ngati chimbalangondo kuti andigwire, wandibisalira ngati mkango.+

11 Wandichotsa panjira zanga ndipo wandikhadzulakhadzula.*

Wandichititsa kuti ndikhale wopanda kanthu.+

12 Wakunga* uta wake ndipo wandisandutsa chinthu choti azilasapo mivi yake.

ה [He]

13 Walasa impso zanga ndi mivi* yotuluka mʼkachikwama kake.

14 Ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu onse ndipo amandiimba mʼnyimbo yawo nʼkumandinyoza tsiku lonse.

15 Wandikhutitsa zinthu zowawa ndipo wandichititsa kuti ndidye chitsamba chowawa.+

ו [Waw]

16 Wagulula mano anga ndi miyala.

Wandiviviniza mʼphulusa.+

17 Inu mwachititsa kuti ndisakhale pamtendere, moti ndaiwala kuti zinthu zabwino zimakhala bwanji.

18 Choncho ndikunena kuti: “Ulemerero wanga ndi chiyembekezo changa mwa Yehova zatha.”

ז [Zayin]

19 Kumbukirani kuti ndikuvutika ndipo ndilibe pokhala.+ Kumbukiraninso kuti ndimadya chitsamba chowawa ndi poizoni wowawa.+

20 Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.+

21 Ndikukumbukira zimenezi mumtima mwanga. Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima wodikira.+

ח [Heth]

22 Chifukwa cha chikondi chokhulupirika cha Yehova, ife sitinatheretu,+

Ndipo chifundo chake sichitha.+

23 Chifundocho chimakhala chatsopano mʼmawa uliwonse+ ndipo ndinu wokhulupirika kwambiri.+

24 Ine ndanena kuti: “Yehova ndi cholowa changa.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”+

ט [Teth]

25 Yehova ndi wabwino kwa munthu amene akumuyembekezera,+ kwa munthu amene akupitiriza kumufunafuna.+

26 Ndi bwino kuti munthu akhale chete*+ nʼkumayembekezera chipulumutso cha Yehova.+

27 Ndi bwino kuti munthu akumane ndi mavuto ali wamngʼono.+

י [Yod]

28 Mulungu akalola kuti zimenezi zimuchitikire, muloleni akhale payekha ndipo akhale chete.+

29 Iye agonjere ndipo aike nkhope yake mufumbi.+ Mwina pangakhale chiyembekezo choti apulumutsidwa.+

30 Aperekere tsaya lake kwa munthu amene akumumenya. Anyozedwe mokwanira.

כ [Kaph]

31 Chifukwa Yehova sadzatitaya mpaka kalekale.+

32 Ngakhale kuti wachititsa kuti timve chisoni, adzatichitiranso chifundo mogwirizana ndi chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chochuluka.+

33 Chifukwa iye sasangalala ndi kuzunza anthu kapena kuwachititsa kuti amve chisoni.+

ל [Lamed]

34 Mulungu savomereza kuti anthu azipondereza akaidi onse padziko lapansi,+

35 Savomereza kuti munthu alephere kuchitira mnzake chilungamo pamaso pa Wamʼmwambamwamba,+

36 Kapena kuchitira munthu zachinyengo pa mlandu wake

Yehova savomereza zimenezi.

מ [Mem]

37 Ndiye ndi ndani amene anganene kuti chinthu chichitike, chinthucho nʼkuchitikadi Yehova asanalamule?

38 Zinthu zoipa komanso zinthu zabwino,

Sizitulukira limodzi pakamwa pa Wamʼmwambamwamba.

39 Kodi pali chifukwa chilichonse choti munthu adandaulire ndi zotsatira za tchimo lake?+

נ [Nun]

40 Tiyeni tifufuze ndi kuganizira mozama makhalidwe athu+ ndipo tibwerere kwa Yehova.+

41 Tiyeni tichonderere Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo tikweze manja athu+ nʼkunena kuti:

42 “Ife tachimwa komanso tapanduka+ ndipo inu simunatikhululukire.+

ס [Samekh]

43 Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni.+

Mwatithamangitsa ndipo mwatipha mopanda chifundo.+

44 Mwadzitchinga ndi mtambo kuti pemphero lathu lisafike kwa inu.+

45 Mwatisandutsa nyansi ndi zinyalala pakati pa anthu a mitundu ina.”

פ [Pe]

46 Adani athu onse akutsegula pakamwa pawo nʼkumatinenera zoipa.+

47 Tikungokhala ndi mantha nthawi zonse ndipo tsoka latigwera.+ Tawonongedwa ndipo tatsala mabwinja okhaokha.+

48 Maso anga akungotuluka misozi ngati mitsinje chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+

ע [Ayin]

49 Maso anga akungotuluka misozi ndipo sikusiya,+

50 Mpaka Yehova atayangʼana pansi nʼkutiona ali kumwamba.+

51 Zimene maso anga aona zachititsa kuti ndikhale wachisoni chifukwa cha zimene zachitikira ana onse aakazi amumzinda wanga.+

צ [Tsade]

52 Adani anga akundisaka ngati mbalame popanda chifukwa.

53 Anandiponya mʼdzenje kuti andiphe ndipo ankandigenda ndi miyala.

54 Ndinamira mʼmadzi moti ndinanena kuti: “Ndifa basi!”

ק [Qoph]

55 Inu Yehova, ndinaitana dzina lanu mofuula ndili mʼdzenje lakuya kwambiri.+

56 Imvani mawu anga. Musatseke khutu lanu pamene ndikulira kupempha kuti mundithandize komanso kuti mundipatse mpumulo.

57 Pa tsiku limene ndinakuitanani, munandiyandikira nʼkundiuza kuti: “Usaope.”

ר [Resh]

58 Inu Yehova, mwandiweruzira milandu yanga. Mwawombola moyo wanga.+

59 Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira. Chonde, ndiweruzeni mwachilungamo.+

60 Mwaona zonse zimene achita pondibwezera ndiponso ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.

ש [Sin] kapena [Shin]

61 Inu Yehova, mwamva mawu awo onyoza ndipo mwaona ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+

62 Mwamva mawu ochokera pakamwa pa anthu amene akundipondereza. Mwamvanso ziwembu zimene akunongʼonezana tsiku lonse kuti andichitire.

63 Tawaonani, akakhala pansi kapena kuimirira akumandinyoza mʼnyimbo zawo.

ת [Taw]

64 Inu Yehova, mudzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.

65 Mudzaumitsa mtima wawo, ndipo zimenezi zidzakhala temberero lawo.

66 Inu Yehova, mudzawathamangitsa mutakwiya ndipo mudzawawononga kuti asapezekenso padziko lapansi.

א [Aleph]

4 Golide amene anali wowala komanso woyengedwa bwino,+ sakuwalanso.

Miyala yopatulika+ yamwazika pamphambano zonse za misewu.+

ב [Beth]

 2 Ana okondedwa a Ziyoni amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengedwa bwino,

Tsopano akuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi,

Ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.

ג [Gimel]

 3 Ngakhale mimbulu imapereka bere kwa ana ake kuti ayamwe,

Koma mwana wamkazi wa anthu anga wakhala wankhanza+ ngati nthiwatiwa zamʼchipululu.+

ד [Daleth]

 4 Lilime la mwana woyamwa lamamatira kummero chifukwa cha ludzu.

Ana akupempha chakudya+ koma palibe amene akuwapatsa.+

ה [He]

 5 Anthu amene ankadya chakudya chabwino agona mʼmisewu chifukwa cha njala.+

Anthu amene ankavala zovala zamtengo wapatali+ kuyambira ali ana, agona pamilu yaphulusa.

ו [Waw]

 6 Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira nʼchachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+

Mzinda umenewu unawonongedwa mʼkanthawi kochepa, ndipo panalibe dzanja limene linauthandiza.+

ז [Zayin]

 7 Anaziri ake+ anali oyera kwambiri, anali oyera kuposa mkaka.

Anali ofiira kuposa miyala yamtengo wapatali ya korali. Anali onyezimira ngati miyala ya safiro.

ח [Heth]

 8 Tsopano ayamba kuoneka akuda kuposa makala.

Anthu sakuthanso kuwazindikira mʼmisewu.

Khungu lawo lafota moti lamamatira kumafupa awo.+ Langoti gwaa ngati mtengo wouma.

ט [Teth]

 9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala.+

Amenewa anafooka nʼkufa chifukwa chosowa chakudya ndipo anafa ngati abayidwa ndi lupanga.

י [Yod]

10 Azimayi amene amakhala achifundo, aphika ana awo ndi manja awo.+

Anawo akhala chakudya chawo pa nthawi yachisoni pamene mwana wamkazi wa anthu anga wawonongedwa.+

כ [Kaph]

11 Yehova wasonyeza ukali wake.

Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+

Ndipo iye wayatsa moto mʼZiyoni, umene wawotcha maziko ake.+

ל [Lamed]

12 Mafumu apadziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,

Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pamageti a Yerusalemu.+

מ [Mem]

13 Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+

Amene anakhetsa magazi a anthu olungama mumzindawo.+

נ [Nun]

14 Ansembe ndi aneneriwo akungoyendayenda mʼmisewu ngati anthu akhungu.+

Aipitsidwa ndi magazi,+

Moti palibe amene angathe kukhudza zovala zawo.

ס [Samekh]

15 Anthu akuwafuulira kuti: “Chokani! Anthu odetsedwa inu! Chokani! Chokani! Musatikhudze!”

Iwo alibe pokhala ndipo akungoyendayenda.

Anthu a mitundu ina akunena kuti: “Sitilola kuti amenewa azikhala ndi ife kuno.*+

פ [Pe]

16 Yehova wawabalalitsa+

Ndipo sadzawakomeranso mtima.

Anthu sadzalemekezanso ansembe+ kapena kuchitira chifundo amuna achikulire.”+

ע [Ayin]

17 Ngakhale panopa maso athu afooka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+

Tinafufuza thandizo ku mtundu wa anthu umene sukanatha kutipulumutsa.+

צ [Tsade]

18 Akutisakasaka kulikonse kumene tikupita,+ moti sitingathenso kuyenda mʼmabwalo a mizinda yathu.

Mapeto a moyo wathu ayandikira. Masiku athu atha chifukwa mapeto a moyo wathu afika.

ק [Qoph]

19 Anthu amene ankatithamangitsa anali aliwiro kuposa ziwombankhanga zouluka mʼmwamba.+

Iwo anatithamangitsa mʼmapiri. Anatibisalira mʼchipululu.

ר [Resh]

20 Wodzozedwa wa Yehova,+ amene ndi mpweya wotuluka mumphuno mwathu, wagwidwa mʼdzenje lawo lalikulu.+

Ponena za ameneyu, ife tinkanena kuti: “Tidzakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.”

ש [Sin]

21 Kondwa ndipo usangalale, iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala mʼdziko la Uzi.

Koma iwenso kapu ya tsoka idzakupeza.+ Udzaledzera ndipo udzavula nʼkukhala maliseche.+

ת [Taw]

22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,* chilango chimene anakupatsa chifukwa cha zolakwa zako chatha.

Sadzakutenganso kupita nawe ku ukapolo.+

Koma Mulungu adzatembenukira kwa iwe, mwana wamkazi wa Edomu, kuti aone zolakwa zako.

Machimo ako adzawaika poyera.+

5 Inu Yehova, kumbukirani zimene zatichitikira.

Tiyangʼaneni kuti muone mmene tikuchitira manyazi.+

 2 Cholowa chathu chaperekedwa kwa anthu achilendo. Nyumba zathu zaperekedwa kwa anthu ochokera kudziko lina.+

 3 Takhala ana amasiye opanda bambo. Amayi athu akhala ngati akazi amasiye.+

 4 Madzi akumwa ndi nkhuni, tikuchita kugula.+

 5 Anthu amene akutithamangitsa atsala pangʼono kutigwira.

Tatopa koma tilibe mwayi woti tipume.+

 6 Kuti tipeze chakudya chokwanira, tikudalira Iguputo+ ndi Asuri.+

 7 Makolo athu amene anachimwa anafa, koma ifeyo ndi amene tikuvutika ndi zolakwa zawo.

 8 Antchito ndi amene akutilamulira. Palibe amene akutilanditsa mʼmanja mwawo.

 9 Kuti tipeze chakudya, timaika moyo wathu pachiswe+ chifukwa cha anthu amene ali ndi malupanga mʼchipululu.

10 Khungu lathu latentha kwambiri ngati ngʼanjo chifukwa cha njala yaikulu.+

11 Achitira zachipongwe* akazi athu amene ali mʼZiyoni ndi anamwali amene ali mʼmizinda ya Yuda.+

12 Akalonga athu anawapachika powamanga dzanja limodzi.+ Anthuwo sankalemekezanso amuna achikulire.+

13 Anyamata akunyamula mphero, ndipo tianyamata tikudzandira chifukwa cholemedwa ndi mitolo ya nkhuni.

14 Amuna achikulire sakupezekanso pageti la mzinda+ ndipo anyamata asiya kuimba nyimbo.+

15 Chisangalalo chamumtima mwathu chatha. Kuvina kwathu kwasanduka kulira maliro.+

16 Chisoti chathu chachifumu chagwa. Tsoka kwa ife chifukwa tachimwa!

17 Chifukwa cha zimenezi, mtima wathu wadwala.+

Ndipo chifukwa cha zinthu zimenezi, maso athu achita mdima,+

18 Chifukwa cha Phiri la Ziyoni limene lakhala bwinja+ ndipo tsopano nkhandwe zikuyendayenda mmenemo.

19 Koma inu Yehova mudzakhala pampando wanu wachifumu mpaka kalekale.

Mpando wanu wachifumu udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

20 Nʼchifukwa chiyani mwatiiwala kwamuyaya nʼkutisiya kwa nthawi yaitali chonchi?+

21 Inu Yehova, tibwezereni kwa inu ndipo ife tibwerera kwa inu mwamsanga.+

Bwezeretsani zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.+

22 Koma inu mwatikanitsitsa.

Mukupitiriza kutikwiyira kwambiri.+

Chaputala 1-4 ndi nyimbo zoimba polira ndipo anazilemba potsatira afabeti ya Chiheberi kapena mwandakatulo.

Kapena kuti, “Atsikana.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “anamunyoza.”

Apa Yerusalemu akumuyerekezera ndi munthu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pake.”

Kapena kuti, “Atsikana.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga iliyonse ya.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Waponda.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamkazi wa diso.”

Kapena kuti, “zipatso zawo zimene.”

Kapena kuti, “Atsikana.”

Kapena kuti, “amkuwa.”

Kapena kuti, “amatsekereza.”

Mabaibulo ena amati, “wandichititsa kukhala wopanda chochita.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Waponda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana aamuna.”

Kapena kuti, “adikirire moleza mtima.”

Kapena kuti, “azikhala kuno ngati alendo.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “Agwiririra.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena