Yobu
3 Pambuyo pa zimenezi m’pamene Yobu anatsegula pakamwa pake n’kuyamba kutemberera tsiku limene anabadwa.+ 2 Tsopano Yobu anati:
3 “Liwonongeke tsiku limene ndinabadwa,+
Ndiponso usiku umene wina ananena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu wapangika m’mimba.’
6 Usiku umenewo utengedwe ndi mdima.+
Usasangalale pakati pa masiku a pachaka,
Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.
9 Nyenyezi za m’chisisira cha m’mawa mwake zizime.
Lidikire kuwala koma lisakuone,
Ndipo lisaone kuwala kwa m’bandakucha.
12 N’chifukwa chiyani mawondo anakumana nane,
Ndipo mabere+ ndinakumana nawo chifukwa chiyani kuti ndiyamwe?
13 Panopa bwenzi nditagona kuti ndisasokonezedwe,+
Bwenzi ndili m’tulo pa nthawiyo, ndipo bwenzi pano ndikupuma+
14 Limodzi ndi mafumu ndi aphungu a padziko lapansi,+
Amene anadzimangira malo omwe tsopano ali bwinja.+
15 Kapena ndi akalonga amene ali ndi golide,
Amene amadzaza nyumba zawo ndi siliva.
16 Kapena ngati pakati pomwe papita pachabe mosadziwa,+ bwenzi ine kulibe,
Mofanana ndi ana amene sanaone kuwala.+
20 N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene ali ndi mavuto,
Ndiponso moyo kwa opwetekedwa mtima?+
21 N’chifukwa chiyani anthu ena amadikirira imfa, koma siwabwerera,+
Ngakhale amakumba pansi poifunafuna, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika?
22 Amenewa amasangalala kwadzaoneni,
Amakondwera akapeza manda.
23 N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa mwamuna wamphamvu amene njira yake yabisika,+
Amene Mulungu akum’pingapinga?+
24 Pakuti chakudya changa chimabwera limodzi ndi kuusa moyo,*+
Ndipo ngati madzi, kubuula kwanga kumakhuthuka.+
25 Chinthu chochititsa mantha chimene ndinali kuchita nacho mantha, chandibwerera,
Ndipo chimene ndinali kuchiopa chabwera kwa ine.+
26 Sindinali wopanda nkhawa kapena wopanda mavuto,
Komanso sindinali pa mtendere, komabe zosautsa mtima zandibwerera.”