Yobu
19 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Kodi amuna inu musautsa moyo wanga mpaka liti,+
Ndi kundilasa ndi mawu?+
5 Ngati amuna inu mukudzikweza polimbana nane,+
Ndipo mukuonetsa kuti chitonzo changa n’chondiyenerera,+
6 Dziwani kuti Mulungu mwiniwakeyo ndi amene wandisocheretsa,
Ndipo wandizunguliza ndi ukonde wake wosakira nyama.+
7 Inetu ndakhala ndikukuwa kuti, ‘Chiwawa!’ koma palibe woyankha.+
Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.+
8 Iye watchinga njira yanga ndi mpanda wamiyala+ mwakuti sindingathe kudutsa.
Ndiponso waika mdima panjira zanga.+
10 Akundikokera pansi mbali zonse, ine n’kuchoka.
Wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.
12 Asilikali ake agwirizana n’kubwera kudzamanga njira yawo kuti alimbane nane,+
Ndipo azungulira hema wanga.
14 Anzanga apamtima anditaya.+
Anthu amene ndinali kuwadziwa andiiwala,
15 Iwo amene anali kukhala m’nyumba mwanga monga alendo.+ Akapolo anga aakazi akukhala ngati sakundidziwa.
Ndakhala mlendo weniweni m’maso mwawo.
16 Ndaitana wantchito wanga koma sakundiyankha.
Ndikukhalira kumuchonderera ndi pakamwa panga kuti andimvere chisoni.
17 Mpweya wanga wasanduka wonyansa kwa mkazi wanga,+
Ndipo ndakhala wonunkha kwa ana obadwa kwa mayi anga.
19 Amuna onse amene anali anzanga apamtima akudana nane,+
Ndipo amene ndinali kuwakonda anditembenukira.+
22 N’chifukwa chiyani amuna inu mukungokhalira kundizunza ngati mmene akuchitira Mulungu?+
Kodi simunatope ndi kundinenera zoipa?
23 Tsopano ndikulakalaka mawu anga akanalembedwa!
Ndithu akanalembedwa m’buku!
24 Akanalembedwa ndi chitsulo chogobera+ n’kukhuthulirapo mtovu,
Akanalembedwa pathanthwe mochita kugoba kuti akhale kwamuyaya.
25 Ineyo ndikudziwa bwino kuti wondiwombola+ ali moyo,
Ndipo adzabwera pambuyo panga n’kuimirira+ pafumbi.
26 Pambuyo pa khungu langa limene alisenda, zidzakhala chonchi.
Koma ndili wowonda choncho, ndidzaona Mulungu.
Maso angawa, osati a mlendo winawake, adzamuonadi Mulungu.*
Impso zanga zasiya kugwira ntchito mkati mwanga.