Yobu
21 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Amuna inu, mvetserani mwatcheru mawu anga.
Zimenezi zikhale zokutonthozani.
3 Ndilezereni mtima kuti ndilankhule.
Ndikamaliza kulankhula, aliyense wa inu akhoza kuyamba kunyoza.+
4 Kodi ineyo ndauza munthu nkhawa zanga?
Kapena n’chifukwa chiyani mzimu wanga sukukwiya?
6 Ndikakumbukira, zikundisokoneza maganizo,
Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.
8 Ana awo akhazikika nawo limodzi pamaso pawo,
Ndiponso mbadwa zawo zakhazikika iwo akuona.
10 Ng’ombe zawo zamphongo zimapereka bere, ndipo siziwononga mphamvu zobereketsa.
Ng’ombe zawo zazikazi zimabereka+ ndipo sizibereka ana akufa.
11 Iwo amalola ana awo kutuluka panja ngati nkhosa,
Ndipo anawo amakhala akudumphadumpha pabwalo.
16 Komatu, ulemerero wawo saupeza chifukwa cha mphamvu zawo.+
Malangizo a anthu oipa atalikirana nane.+
Kodi ndi kangati pamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?+
18 Kodi iwo amakhala ngati udzu wouluzika ndi mphepo?+
Kapena ngati mankhusu* ouluka ndi mphepo yamkuntho?
19 Zoipa zimene munthu anachita, Mulungu adzazisungira ana ake omwe,+
Adzam’patsa mphoto yake, ndipo iye adzaidziwa.+
21 Kodi adzatha kusangalala ndi ana ake iyeyo atapita,
Chiwerengero cha miyezi yake chitadulidwa pakati?+
23 Munthu ameneyo adzafa ali wokhutira.+
Adzafa ali pa mtendere ndiponso wosatekeseka.
24 Ntchafu zake zitadzaza mafuta,
Ndiponso mafuta a m’mafupa mwake akadali ofewa.
27 Inetu ndikudziwa bwino maganizo anu amuna inu,
Ndiponso zachiwawa zimene mungapangane kuti mundichitire.+
28 Popeza mukuti, ‘Kodi nyumba ya wolemekezeka ili kuti,
Ndipo hema wa oipa ali kuti? Kodi malo awo okhala ali kuti?’+
29 Kodi simunafunse anthu oyenda m’misewu,
Ndipo simuonetsetsa zizindikiro zawo,
30 Kuti pa tsiku la tsoka woipa amapulumuka,+
Ndipo pa tsiku la mkwiyo amawomboledwa?