Yobu
6 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Zikanakhala bwino masautso anga+ onse akanayezedwa kulemera kwake,
Ndiponso pa nthawi yomweyo mavuto anga akanaikidwa pasikelo.
4 Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilasa,+
Ndipo ine ndikumwa poizoni wa miviyo.+
Zoopsa zochokera kwa Mulungu zasonkhana kuti zilimbane nane.+
7 Moyo wanga wakana kukhudza zinthu zoterozo.
Zili ngati matenda m’chakudya changa.
8 Zikanakhala bwino pempho langa likanayankhidwa,
Ndiponso Mulungu akanandipatsa chiyembekezo.
10 Ngakhale zimenezo, bwenzi zili zonditonthoza.
Ndikadadumpha ndi chisangalalo+ ngakhale kuti ndikumva ululu wosalekeza,
Chifukwa sindinabise mawu+ a Woyerayo,+ ngakhale kuti iye sakanandichitira chisoni.
11 Kodi ndili ndi mphamvu zochuluka motani, kuti ndizidikirabe?+
Ndipo kodi mapeto anga ndi otani, kuti ndipitirize kutalikitsa moyo wanga?
12 Kodi mphamvu zanga ndi mphamvu za miyala?
Kapena kodi mnofu wanga ndi wamkuwa?
13 Ndilibenso mphamvu zodzithandizira,
Ndipo sindingathenso kugwira ntchito bwinobwino.
15 Ngakhale abale anga amene, achita zachinyengo+ ngati mtsinje woyenda nthawi yozizira,
Ngati makwawa a mitsinje yoyenda nthawi yozizira, imene imauma.
16 Mitsinjeyo imakhala ndi madzi akuda chifukwa cha kusungunuka kwa madzi oundana,
Ndipo chipale chofewa nachonso chimasungunukira momwemo.
18 Njira zawo zimakhala zokhotakhota.
Mitsinjeyo imapita kumalo opanda kanthu, n’kutha.
22 Kodi ndinanena kuti, ‘Mundipatse kanthu,
Kapena mutapeko pa chuma chanu n’kundiperekera mphatso?
23 Kapena mundipulumutse m’manja mwa mdani,+
Ndi kundiwombola m’manja mwa anthu ankhanza?’+
26 Kodi mwapangana kuti mudzudzule mawu anga,
Chonsecho mawu a munthu wopanda chiyembekezo+ amatengedwa ndi mphepo?+
29 Chonde sinthani maganizo anu, kuti pachitike chilungamo.
Ndithu sinthani maganizo. Inetu ndikadali wolungama.+
30 Kodi palilime panga pali zosalungama?
Kapena kodi m’kamwa mwanga simuzindikira mavuto?