Yobu
22 Tsopano Elifazi wa ku Temani anayankha kuti:
2 “Kodi mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu?+
Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye?
3 Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?+
Kapena amapindula chilichonse chifukwa chakuti suchita cholakwa?+
6 Umalanda abale ako chikole popanda chifukwa,+
Umalanda zovala anthu osauka n’kuwasiya ali maliseche.
10 N’chifukwa chake misampha ya mbalame yakuzungulira,+
Ndipo ukusokonezeka ndi zoopsa zadzidzidzi.
11 N’chifukwa chake pali mdima, moti sungathe kuona,
Ndipo madzi osefukira akumiza.
13 Komabe iwe wanena kuti: ‘Mulungu akudziwa chiyani?
Kodi angathe kuweruza pali mdima wandiweyani?
14 Mitambo imamutchingira malo moti saona,
Ndipo iye amayenda pamwamba pa thambo.’
15 Kodi upitiriza kuyenda panjira yakalekale
Imene anthu ochita zoipa anayendamo,
16 Anthu amene anatengedwa nthawi yawo isanakwane,+
Amene maziko+ awo amakhuthulidwa ngati madzi a mumtsinje,
17 Ndiponso amene amauza Mulungu woona kuti: ‘Tichokereni!+
Kodi Wamphamvuyonse angatichite chiyani?’
18 Chonsecho iye wadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,+
Ndipo malangizo a anthu oipa ali kutali ndi ine.+
19 Olungama adzaona chiwonongeko chawo n’kusangalala,+
Ndipo wosalakwa adzawaseka kuti:
20 ‘Zoonadi adani athu afafanizidwa,
Ndipo zimene azisiya, moto udzazinyeketsa.’
21 Um’dziwe bwino Mulungu ndi kukhala naye pa mtendere.
Ukatero zinthu zabwino zidzabwera kwa iwe.
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuyonse,+ udzabwezeretsedwa mwakale.
Ukaika zosalungama kutali ndi hema wako,
24 Ndipo ukataya golide wako wamtengo wapatali m’fumbi,
Ukataya golide wa ku Ofiri+ m’miyala ya m’zigwa,*
25 Ndithu Wamphamvuyonse adzakhala golide wako wamtengo wapatali,
Ndiponso siliva wako wabwino kwambiri.+