Yobu
23 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Ngakhale lero, sindikusangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Chotero ndikudandaula.+
Dzanja langa likulemera chifukwa chakuti ndikuusa moyo.
4 Bwenzi nditapita pamaso pake ndi nkhani yoti aweruze.
M’kamwa mwanga bwenzi nditadzazamo mfundo zodziikira kumbuyo.
5 Bwenzi nditadziwa mawu amene amanena pondiyankha,
Ndipo bwenzi nditaganizira zimene amandiuza.+
7 Kumeneko, wowongoka mtima adzathetsa nkhani zake ndi iye,
Ndipo ine ndikanapulumuka kwa woweruza wanga mpaka kalekale.
8 Ndikapita kum’mawa, iye kulibe.
Ndikabwerako, sindimuona.+
9 Ndimapita kumanzere kumene iye akugwira ntchito, koma sindimuona.
Amatembenukira kudzanja lamanja, koma ine osamuona,
10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+
Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+
12 Sindisiya malamulo otuluka pakamwa pake.+
Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake+ kuposa zimene akufuna kuti ndichite.
17 Pakuti sindinaletsedwe kulankhula chifukwa cha mdima,
Kapenanso chifukwa chakuti mdima wandiweyani waphimba nkhope yanga.