2 Akorinto
10 Tsopano ineyo Paulo, ndikukudandaulirani mwa kufatsa+ ndi kukoma mtima+ kwa Khristu, ngakhale kuti ndimaoneka wosanunkha kanthu+ ndikakhala pakati panu, koma wolimba mtima polankhula nanu ndili kwina.+ 2 Ndithu ndikanakonda kuti anthu amene akuona kuti ifeyo timachita zinthu motsatira maganizo a dzikoli,* asinthe maganizo awo, kuti ndikadzabwera kumeneko ndisadzachite zinthu zazikulu zotsutsana nawo.+ 3 Pakuti ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse,+ sitikumenya nkhondo motsatira maganizo a dzikoli.+ 4 Pakuti zida za nkhondo yathu si zochokera m’dziko lino,+ koma ndi zida zamphamvu zimene Mulungu watipatsa,+ zimene zimatha kugwetsa zinthu zozikika molimba. 5 Pakuti tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu,+ ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu. 6 Komanso ndife okonzeka kupereka chilango pa aliyense wosamvera,+ inuyo mukadzasonyeza kuti ndinu omvera pa chilichonse.+
7 Mukuona zinthu mogwirizana ndi maonekedwe ake akunja.+ Ngati aliyense amakhulupirira mumtima mwake kuti ndi wotsatira Khristu, adziwenso kuti, monga mmene iye alili wotsatira Khristu, ifenso ndife otsatira Khristu.+ 8 Pakuti ngakhale nditati ndidzitamandire+ mopitirirako muyezo za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa kuti tikulimbikitseni, osati kukupasulani,+ sindingachite manyazi. 9 Ponena zimenezi, sindikufuna kuti muganize kuti makalata anga cholinga chake n’kukuopsezani. 10 Pakuti ena amati: “Makalata ake ndi olemerera ndi amphamvu, koma iyeyo akakhala pakati pathu amaoneka wofooka+ ndipo nkhani zake n’zosagwira mtima.”+ 11 Munthu woteroyo adziwe kuti zimene tikunena m’makalata athu tili kwina, tidzachitanso zomwezo tikadzakhala pakati panu.+ 12 Pakuti sitidzayesa n’komwe kudziona ngati ndife ofanana ndi anthu enaake kapena kudziyerekezera ndi ena amene amadzikweza.+ Ndithudi anthu amenewo samvetsa kanthu kalikonse chifukwa akuyezana okhaokha pogwiritsira ntchito miyezo yawo yomwe, ndipo akudziyerekezera ndi iwo eni.+
13 Koma ifeyo tidzadzitamandira, osati pa zinthu zimene zili kunja kwa malire amene tapatsidwa,+ koma pa zinthu zimene zili mkati mwa malire a gawo limene Mulungu anatipatsa pochita kutiyezera, limene analifikitsa mpaka kwanuko.+ 14 Choncho sitikupitirira malire a gawo lathu, ngati kuti gawolo silikufika kwa inu. Ayi ndithu, pakuti tinayamba ndife kufika kwanuko polengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 15 Sitikudzitamandira kunja kwa malire a gawo limene tinapatsidwa, podzitamandira chifukwa cha ntchito za munthu wina ayi,+ koma tili ndi chiyembekezo chakuti chikhulupiriro chanu chikadzawonjezeka,+ ntchito yathunso idzakula pakati panu, limene ndi gawo lathu.+ Ndiyeno tidzachitanso zowonjezereka, 16 polengeza uthenga wabwino kumayiko akutali kupitirira kwanuko,+ kuti tisadzitamande m’gawo la wina, mmene anakonzamo kale. 17 “Koma amene akudzitamandira, adzitamande mwa Yehova.”+ 18 Pakuti wodzikweza yekha si amene amavomerezedwa,+ koma amene Yehova+ wamuvomereza.+