Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 31:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Chifukwa inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+

      Chifukwa cha dzina lanu,+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+

  • Salimo 79:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+

      Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.

      Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+

  • Salimo 109:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma inu, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,

      Ndithandizeni kuti dzina lanu lilemekezedwe.+

      Ndipulumutseni chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino.+

  • Salimo 143:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha dzina lanu.

      Ndipulumutseni mʼmavuto anga, chifukwa ndinu wachilungamo.+

  • Ezekieli 36:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene munalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+

  • Danieli 9:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Imvani, inu Yehova. Tikhululukireni,+ inu Yehova. Timvereni ndipo muchitepo kanthu, inu Yehova! Musazengereze inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu. Chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”+

  • Mateyu 6:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma inu muzipemphera chonchi:+

      ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu+ liyeretsedwe.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena