Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Philippians 1:1-4:23
  • Afilipi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Afilipi
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Afilipi

Kwa Afilipi

1 Ine Paulo ndili pamodzi ndi Timoteyo monga akapolo+ a Khristu Yesu. Ndikulembera oyera onse ogwirizana ndi Khristu Yesu amene ali ku Filipi,+ komanso oyang’anira ndi atumiki othandiza:+

2 Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+

3 Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira za inu.+ 4 Ndimachita zimenezi m’pembedzero langa lililonse limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu.+ 5 Ndimamuyamika chifukwa cha chopereka+ chanu chimene mwakhala mukupereka ku uthenga wabwino, kuchokera pa tsiku loyamba mpaka pano. 6 Pakuti ndikutsimikizira kuti iyeyo amene anayambitsa ntchito yabwino kwa inu, adzaipitiriza ndi kuimalizitsa+ m’tsiku+ la Yesu Khristu. 7 N’zoyenera kwa ineyo kuganizira nonsenu mwa njira imeneyi, pakuti inu ndinu apamtima panga,+ ndiponso nonsenu ndinu ogawana+ nane m’kukoma mtima kwakukulu, m’maunyolo anga m’ndende,+ ndi pa kuteteza+ uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.+

8 Mulungu ndiye mboni yanga kuti ndikufunitsitsa nditakuonani nonsenu. Ndikufunitsitsa nditakuonani ndi chikondi chachikulu+ ngati chimene Khristu Yesu ali nacho. 9 Ndipo ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirire kukula,+ limodzi ndi kudziwa zinthu molondola,+ komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.+ 10 Chitani zimenezi kuti muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti,+ kuti mukhale opanda cholakwa+ ndi osakhumudwitsa+ ena kufikira tsiku la Khristu. 11 Muchite zimenezi kutinso mudzazidwe ndi zipatso zolungama+ kudzera mwa Yesu Khristu, kuti Mulungu akalemekezedwe ndi kutamandidwa.+

12 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zondichitikira zija, zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino+ m’malo moulepheretsa. 13 Moti, kumangidwa kwanga+ chifukwa cha Khristu, kwadziwika ndi aliyense+ pakati pa Asilikali Oteteza Mfumu ndi ena onse.+ 14 Abale ambiri mwa Ambuye, alimba mtima chifukwa cha kumangidwa kwanga, ndipo akuonetsa kulimba mtima kowonjezereka polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.+

15 N’zoona kuti ena akulalikira Khristu mwakaduka ndiponso mwampikisano,+ koma ena akulalikira ndi cholinga chabwino.+ 16 Achiwiriwa akufalitsa Khristu chifukwa cha chikondi, pakuti akudziwa kuti ine ndili m’ndende muno kuti nditeteze+ uthenga wabwino. 17 Koma oyambawo akutero chifukwa cha mtima wokonda mikangano,+ osati ndi cholinga chabwino. Pakuti akungofuna kundiwonjezera masautso+ m’ndende muno. 18 Akatero ndiye kuti achita chiyani? Palibe! Mulimonse mmene zingakhalire, kaya ndi mwachiphamaso+ kapena m’choonadi, Khristu akufalitsidwabe.+ Choncho ine ndikukondwera. Ndipotu ndipitiriza kukondwera, 19 chifukwa ndikudziwa kuti mwa mapembedzero+ anu, ndi mwa mzimu wa Yesu Khristu,+ ndidzamasulidwa. 20 Zidzatero mogwirizana n’kuti ndikudikira mwachidwi,+ ndiponso ndili ndi chiyembekezo+ chakuti sindidzachititsidwa manyazi+ mwa njira iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula,+ Khristu alemekezedwe mwa thupi langa tsopano, monga mmene zakhala zikuchitikira m’mbuyo monsemu.+ Kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalira.+

21 Pakuti kwa ine, ndikakhala moyo, ndikhalira moyo Khristu,+ ndipo ndikamwalira+ ndipindula. 22 Tsopano ngati ndipitirizabe kukhala ndi moyo m’thupi limene ndili naloli, ntchito ya manja anga idzawonjezeka,+ koma choti ndisankhe pamenepa, sindinena. 23 Ndapanikizika ndi zinthu ziwirizi,+ koma chimene ndikufuna ndicho kumasuka ndi kukhala ndi Khristu.+ Pakuti kunena zoona, chimenechi ndiye chabwino kwambiri.+ 24 Komabe, kukhalabe m’thupi kwa ine n’kofunika, makamaka chifukwa cha inu.+ 25 Choncho, pokhala wotsimikiza za chimenechi, ndikudziwa kuti ndikhalabe ndi moyo.+ Chotero ndidzakhala ndi inu nonse kuti mupite patsogolo,+ ndi kuti musangalale pa chikhulupiriro chanu. 26 Inde, kuti kusangalala kwanu kusefukire mwa Khristu Yesu, chifukwa cha ine pokhalanso limodzi ndi inu.

27 Chachikulu, makhalidwe anu akhale oyenera+ uthenga wabwino wa Khristu. Kuti kaya ndabwera kudzakuonani kapena pamene ine kulibe, ndizimva za inu, kuti mukulimbikira mu mzimu umodzi. Ndipo ndi mtima umodzi,+ mukulimbika pamodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha uthenga wabwino. 28 Komanso simukuchita mantha m’njira iliyonse ndi okutsutsani.+ Kwa iwo, chimenechi ndi chizindikiro chakuti adzawonongedwa, koma kwa inu, ndi chizindikiro cha chipulumutso.+ Chizindikiro chimenechi n’chochokera kwa Mulungu. 29 Zili choncho chifukwa inu munapatsidwa mwayi. Osati mwayi wokhulupirira+ Khristu wokha, komanso wovutika+ chifukwa cha iye. 30 Ndiye chifukwa chake inunso muli ndi mavuto ofanana ndi amene munawaona kwa ine,+ ndiponso amene mukumva kuti ndikukumana nawo panopa.+

2 Chotero, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu,+ kaya kutonthozana kulikonse kwa chikondi, kaya mzimu woganizirana,+ kaya chikondi chachikulu+ chilichonse ndi chifundo, 2 chititsani chimwemwe changa kusefukira pokhala ndi maganizo amodzi,+ ndi chikondi chofanana. Mukhalenso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi.+ 3 Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano+ kapena wodzikuza,+ koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.+ 4 Musamaganizire zofuna zanu zokha,+ koma muziganiziranso zofuna za ena.+

5 Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.+ 6 Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu,+ kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.+ 7 Sanatero ayi, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo,+ ndi kukhala wofanana ndi anthu.+ 8 Kuposanso pamenepo, atakhala munthu,+ anadzichepetsa ndi kukhala womvera mpaka imfa.+ Anakhala womvera mpaka imfa ya pamtengo wozunzikirapo.*+ 9 Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.+ Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.+ 10 Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo.+ 11 Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake+ kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye,+ polemekeza Mulungu Atate.+

12 Chotero, okondedwa anga, monga mmene mwakhalira omvera nthawi zonse,+ osati pokhapokha ine ndikakhalapo,* koma mofunitsitsa kwambiri tsopano pamene ine kulibe, pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha+ ndi kunjenjemera. 13 Pakuti Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu+ kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.+ 14 Muzichita zinthu zonse popanda kung’ung’udza+ ndi kutsutsana,+ 15 kuti mukhale opanda chifukwa chokunenezani nacho ndiponso osalakwa.+ Mukhale ana a Mulungu opanda chilema+ pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota,+ umene mukuwala pakati pawo monga zounikira m’dzikoli.+ 16 Muchite zimenezi pamene mukupitirizabe kugwira mwamphamvu mawu amoyo,+ kuti ndikakhale ndi chifukwa chosangalalira m’tsiku la Khristu,+ poona kuti sindinathamange pachabe, kapena kuchita khama pachabe.+ 17 Ngakhale kuti ndikudzipereka ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa+ pansembe+ ndi pa ntchito yotumikira anthu imene chikhulupiriro chakupatsani,+ ndine wokondwa ndipo ndikukondwera+ ndi inu nonse. 18 Tsopano inunso khalani okondwa ndipo sangalalani limodzi ndi ine.+

19 Koma ine, mwa Ambuye Yesu ndikuyembekeza kutumiza Timoteyo kwa inu posachedwapa, kuti ndidzasangalale+ ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu. 20 Pakuti ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi+ za inu moona mtima. 21 Pakuti ena onse akungofuna za iwo eni,+ osati za Khristu Yesu. 22 Koma inu mukudziwa kudalirika kumene iye anaonetsa, kuti monga mwana+ ndi bambo ake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino. 23 Choncho, ameneyu ndiye munthu amene ndikuyembekeza kumutumiza kwa inu, ndikangodziwa mmene zinthu zikhalire kwa ine. 24 Ndithudi, ndikukhulupirira mwa Ambuye kuti inenso ndibwera posachedwa.+

25 Komabe, ndaona kuti n’kofunika kutumiza Epafurodito kwa inu.+ Ameneyu ndi m’bale wanga, wantchito mnzanga+ ndi msilikali mnzanga.+ Komanso iye ndi nthumwi yanu ndi wonditumikira pa zosowa zanga. 26 Pakuti iye akulakalaka kukuonani nonsenu, ndipo akuvutika maganizo chifukwa munamva kuti anali kudwala. 27 Inde, n’zoona, anadwaladi kutsala pang’ono kufa. Koma Mulungu anam’chitira chifundo.+ Ndipo chifundo chimenecho sanachitire iye yekha ayi, koma inenso, kuti chisoni changa chisawonjezeke. 28 Choncho, ndikumutumiza mofulumira kwambiri, kuti inu mukamuona musangalale, ndiponso kuti chisoni changa chichepe. 29 Chotero, mulandireni monga mwa nthawi zonse,+ mwa Ambuye ndi chimwemwe chonse. Ndipo abale okhala ngati iyeyu muziwalemekeza kwambiri,+ 30 pakuti chifukwa cha ntchito ya Ambuye, anatsala pang’ono kufa.+ Anaika moyo wake pachiswe, kuti adzanditumikire m’malo mwa inu,+ popeza simuli kuno.

3 Pomalizira abale anga, pitirizani kukondwera mwa Ambuye.+ Kukulemberani zinthu zimodzimodzi si vuto kwa ine, koma ndi chitetezo kwa inu.

2 Chenjerani ndi agalu.+ Chenjerani ndi ochita ntchito zovulaza. Chenjerani ndi anthu amene amachita mdulidwe.+ 3 Pakuti ife ndife amdulidwe weniweni,+ amene tikuchita utumiki wopatulika mwa mzimu wa Mulungu.+ Timadzitamandira mwa Khristu Yesu,+ ndipo sitidalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika,+ 4 ngakhale kuti ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika.

Ngati alipo munthu woganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndiye woposa ameneyo.+ 5 Ineyo ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini,+ Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinali kuzunza mpingo.+ Kunena za chilungamo mwa kutsatira chilamulo, ndinakhaladi wopanda chifukwa chondinenezera. 7 Koma zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine, zimenezo ndaziona kukhala zopanda phindu chifukwa cha Khristu.+ 8 Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.+ Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala,+ kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu. 9 Ndiponso kuti ndikapezeke wogwirizana ndi iye ndikuchita chilungamo. Osati chilungamo changachanga chobwera ndi chilamulo,+ koma chobwera mwa kukhulupirira+ Khristu, chochokera kwa Mulungu pa maziko a chikhulupiriro.+ 10 Ndachita zimenezi kuti ndim’dziwe komanso kuti ndidziwe mphamvu ya kuuka kwake kwa akufa.+ Kutinso ndigawane naye m’masautso+ ake, ndi kulolera kufa imfa monga yake.+ 11 Ndachita izi kuti ndiyesetse ndi kuona ngati n’zotheka kudzauka nawo pa kuuka koyambirira+ kuchokera kwa akufa.

12 Si kuti ndalandira kale mphotoyo, kapena kuti ndakhala kale wangwiro+ ayi. Koma ndikuyesetsabe+ kuti ndione ngati inenso ndingapeze+ chimene chinachititsanso Khristu Yesu kundipeza.+ 13 Abale, ine sindidziyesa ngati ndalandira kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo+ ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.+ 14 Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza+ mphoto+ ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba,+ chodzera mwa Khristu Yesu. 15 Choncho, tiyeni tonse amene tili okhwima mwauzimu,+ tikhale ndi maganizo amenewa.+ Ndipo ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa m’mbali ina iliyonse, Mulungu adzakuululirani maganizo oyenerawo. 16 Komabe, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera+ m’njira yomweyo.

17 Mogwirizana, khalani otsanzira+ ine abale, ndipo muzionetsetsa amene akuyenda mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani.+ 18 Pakuti alipo ambiri amene ndinali kuwatchula kawirikawiri, koma tsopano ndikuwatchula ndi misozi, amene akuyenda monga adani a mtengo wozunzikirapo* wa Khristu.+ 19 Amenewo mapeto awo ndi chiwonongeko,+ ndipo mulungu wawo ndi mimba yawo.+ Ulemerero wawo uli m’zinthu zawo zochititsa manyazi,+ ndipo maganizo awo ali pa zinthu za dziko lapansi.+ 20 Koma ife, ndife nzika+ zakumwamba,+ kumenekonso tikuyembekezera mwachidwi+ mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu.+ 21 Iyeyo adzakonzanso thupi lathu lonyozekali+ kuti lifanane ndi thupi lake laulemerero.+ Adzatero malinga ndi mphamvu+ imene ali nayo, yotha kugonjetsera+ ngakhale zinthu zonse kwa iye mwini.

4 Choncho abale anga okondedwa, inu amene ndimakukondani ndiponso amene ndimalakalaka kukuonani, inu chimwemwe changa ndi chisoti changa chaulemerero,+ pitirizani kulimbikira+ mwa Ambuye.

2 Ndikudandaulira Eodiya ndi Suntuke, kuti akhale amaganizo amodzi+ mwa Ambuye. 3 Ndikupempha iwenso wantchito mnzanga weniweni,+ kuti upitirize kuwathandiza amayi amenewa. Iwo ayesetsa limodzi ndi ine pa ntchito+ ya uthenga wabwino. Achita zimenezi limodzinso ndi Kilementi ndi antchito anzanga ena onse,+ amene mayina awo+ ali m’buku la moyo.+

4 Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye.+ Ndibwerezanso, Kondwerani.+ 5 Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.+ Ambuye ali pafupi.+ 6 Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse,+ koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero,+ pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.+ 7 Mukatero, mtendere+ wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu+ ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

8 Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera,+ zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.+ 9 Zinthu zimene munaphunzira, zimene munazivomereza, zimene munazimva, ndi zimene munaziona kwa ine, muzichita zimenezo,+ ndipo Mulungu wamtendere+ adzakhala nanu.

10 Ine ndikukondwera kwambiri mwa Ambuye, kuti tsopano mwayambanso kundiganizira.+ Ndipo n’zimene munalidi kufuna kungoti munali kusowa mpata. 11 Si kuti ndikulankhula izi kusonyeza kuti ndikusowa kanthu, pakuti m’zochitika zosiyanasiyana ine ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo.+ 12 Ndithudi, kukhala wosowa ndimakudziwa,+ kukhala ndi zochuluka ndimakudziwanso. M’zinthu zonse ndi m’zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. Ndaphunziranso chinsinsi chokhala ndi zochuluka, ndi chokhala wosowa.+ 13 Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.+

14 Komabe, munachita bwino pondithandiza+ m’chisautso changa.+ 15 Ndipo inu Afilipi, mukudziwanso kuti pamene ndinayamba kulengeza uthenga wabwino, komanso pamene ndinanyamuka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi womwe umene unathandizana nane pa nkhani ya kupatsa ndi kulandira, kupatulapo inu nokha.+ 16 Chifukwa ngakhale ku Tesalonika, inu munanditumizira kenakake pa zosowa zanga ndipo munachita zimenezi kawiri konse. 17 Si kuti mtima wanga uli pa mphatsoyo ayi,+ koma ndikufunitsitsa kuti mulandire madalitso+ amene adzawonjezere phindu pa zimene muli nazo. 18 Komabe, ine ndili ndi zonse zimene ndimafunikira, ndipo n’zokwanira ndi zosefukira. Sindikusowa kanthu, pakuti tsopano ndalandira kwa Epafurodito+ zinthu zochokera kwa inu. Zili ngati fungo lonunkhira bwino+ ndiponso nsembe yovomerezeka+ yosangalatsa kwa Mulungu. 19 Nayenso Mulungu wanga+ adzakupatsani zosowa zanu zonse+ mogwirizana ndi kuchuluka kwa chuma chake+ chaulemerero, kudzera mwa Khristu Yesu. 20 Tsopano kwa Mulungu wathu ndi Atate, kukhale ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.

21 Mundiperekere moni+ kwa aliyense amene ali woyera mwa+ Khristu Yesu. Abale amene ali nane akukupatsani moni. 22 Oyera onse akupereka moni, koma makamaka a m’nyumba ya Kaisara.+

23 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.+

Onani Zakumapeto 9.

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena