Kwa Aefeso
1 Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu,+ ndikulembera oyera amene ali ku Efeso, okhulupirikawo+ okhala mogwirizana+ ndi Khristu Yesu, kuti:
2 Kukoma mtima kwakukulu,+ ndi mtendere+ wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.
3 Atamandike Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ pakuti watidalitsa+ ndi dalitso lililonse lauzimu m’malo akumwamba+ mogwirizana ndi Khristu. 4 Wachita zimenezi monga mmene anatisankhira+ kuti tikakhale ogwirizana ndi Yesuyo dziko lisanakhazikitsidwe,+ kuti tikakhale oyera ndi opanda chilema+ pamaso pa Mulungu m’chikondi.+ 5 Pakuti anatisankhiratu+ kuti adzatitenga+ kukhala ana ake+ kudzera mwa Yesu Khristu, malinga ndi zomukomera iyeyo ndiponso chifuniro chake.+ 6 Anatero kuti kukoma mtima kwakukulu kwaulemerero+ kumene anatisonyeza kudzera mwa wokondedwa wake+ kutamandike.+ 7 Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi+ ake, inde, takhululukidwa+ machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.+
8 Iye anatipatsa mochuluka kukoma mtima kumeneku mwa nzeru zonse+ ndi kuzindikira konse, 9 moti anatiululira chinsinsi chopatulika+ cha chifuniro chake. Chinsinsicho n’chogwirizana ndi zokomera mwiniwakeyo ndiponso zimene anafuna mumtima mwake,+ 10 kuti akakhazikitse dongosolo+ lake, ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikidwiratu.+ Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso+ zinthu zonse pamodzi mwa Khristu,+ zinthu zakumwamba+ ndi zinthu zapadziko lapansi.+ Inde, kuzisonkhanitsanso mwa iye. 11 Mogwirizana ndi iyeyo tinaikidwa kukhala odzalandira cholowa,+ pakuti anatisankhiratu mwa kufuna kwake, iye amene amayendetsa zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake.+ 12 Anachita zimenezo kuti ife tichititse kuti ulemerero wake utamandike,+ ifeyo amene takhala oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu.+ 13 Koma inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi,+ omwe ndi uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu.+ Kudzeranso mwa iye, mutakhulupirira munaikidwa chidindo+ cha mzimu woyera wolonjezedwawo,+ 14 umene ndi chikole+ cha cholowa chathu cham’tsogolo,+ kuti anthu a Mulungu+ adzamasulidwe ndi dipo,+ n’cholinga choti iye adzatamandidwe ndi kupatsidwa ulemerero.
15 Ndiye chifukwa chake inenso, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chimene muli nacho mwa Ambuye Yesu ndi mmene mumachisonyezera m’zochita zanu ndi oyera onse,+ 16 sindileka kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndikupitirizabe kukutchulani m’mapemphero anga,+ 17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemerero, akupatseni mzimu wa nzeru+ ndi kuti mumvetse zimene Iye akuulula mogwirizana ndi kumudziwa molondola.+ 18 Popeza maso+ a mtima wanu aunikiridwa,+ ndikukutchulanibe m’mapemphero anga kutinso mudziwe chiyembekezo+ chimene anakuitanirani, chuma chaulemerero+ chimene wasungira oyera monga cholowa,+ 19 ndi kukula kwa mphamvu zake zopambana+ zimene wazipereka kwa ife okhulupirira. Kukula kumeneko n’kogwirizana ndi ntchito+ ya mphamvu yake yodabwitsa, 20 imene waigwiritsa ntchito pa Khristu pamene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumukhazika kudzanja lake lamanja+ m’malo akumwamba.+ 21 Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse,+ ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense,+ osati mu nthawi* ino yokha,+ komanso imene ikubwerayo.+ 22 Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a iyeyo,+ ndipo anamuika mutu wa zinthu zonse+ chifukwa cha mpingo, 23 umene ndi thupi lake.+ Mpingowo ndi wodzaza+ ndi iye, amene amadzaza zinthu zonse mokwanira.+
2 Ndiponso, Mulungu anapangitsa inuyo kukhala amoyo pamene munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu.+ 2 Munali kuyenda m’zimenezo mogwirizana ndi nthawi*+ za m’dzikoli, momveranso wolamulira+ wa mpweya umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka,+ tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.+ 3 Inde, tonsefe pa nthawi inayake pamene tinali pakati pawo, tinali kukhala motsatira zilakolako za thupi lathu.+ Tinali kuchita zofuna za thupi+ ndi maganizo, ndipo mwachibadwa tinali ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,+ mofanana ndi ena onse. 4 Koma Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka,+ mwachikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,+ 5 anatikhalitsa amoyo pamodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa m’machimo,+ (pakuti inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu)+ 6 ndipo anatikweza+ pamodzi, ndi kutikhazika pamodzi m’malo akumwamba+ mogwirizana ndi Khristu Yesu. 7 Anachita zimenezi kuti mu nthawi* zimene zikubwera+ padzasonyezedwe chuma chopambana+ cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anatisonyeza mogwirizana+ ndi Khristu Yesu.
8 Mwa kukoma mtima kwakukulu kumeneku, ndithudi mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro,+ osati mwa inu nokha,+ koma monga mphatso ya Mulungu.+ 9 Si chifukwanso cha ntchito ayi,+ kuti munthu asakhale ndi chifukwa chodzitamandira.+ 10 Pakuti ndife ntchito ya manja ake,+ ndipo tinalengedwa+ mogwirizana+ ndi Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino,+ zimene Mulungu anakonzeratu+ kuti tiyendemo.
11 Chotero nthawi zonse muzikumbukira kuti poyamba munali anthu a mitundu ina mwakuthupi.+ Anthu otchedwa “odulidwa,” amene anadulidwa mwakuthupi ndi manja,+ anali kukutchani “osadulidwa.” 12 Muzikumbukiranso kuti pa nthawi imene ija munali opanda Khristu,+ otalikirana+ ndi mtundu wa Isiraeli komanso alendo osadziwika pa mapangano a lonjezolo.+ Munalibe chiyembekezo+ ndipo inu munalibe Mulungu m’dzikoli.+ 13 Koma tsopano mogwirizana ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwakhala pafupi chifukwa cha magazi+ a Khristu. 14 Pakuti iye ndiye mtendere wathu,+ amene analumikiza mbali ziwiri+ kukhala imodzi,+ ndi kugwetsa khoma+ lowalekanitsa limene linali pakati pawo.+ 15 Ndi thupi lake,+ anathetsa chidani chimene chinalipo,+ chimene ndi Chilamulo chokhala ndi malamulo operekedwa monga malangizo.+ Anachithetsa kuti mogwirizana ndi iye, alenge munthu mmodzi watsopano+ kuchokera ku magulu awiri a anthu,+ ndi kukhazikitsa mtendere. 16 Ndiponso kuti kudzera mwa mtengo wozunzikirapo*+ ayanjanitse+ magulu awiri a anthuwo kwa Mulungu, ndipo anthuwo akhale thupi limodzi,+ chifukwa anali atapheratu chidanicho+ kudzera mwa iye mwini. 17 Chotero iye anabwera n’kulengeza uthenga wabwino wa mtendere+ kwa inuyo, inu akutali, ndipo analengezanso mtendere kwa apafupi,+ 18 chifukwa kudzera mwa iye, magulu onse awirife+ tingathe kufikira+ Atate mwa mzimu umodzi.+
19 Chotero, simulinso anthu osadziwika+ kapena alendo m’dziko la eni,+ koma ndinu nzika+ zinzawo za oyerawo,+ ndipo ndinu a m’banja+ la Mulungu. 20 Mwamangidwa pamaziko+ a atumwi+ ndi aneneri,+ ndipo Khristu Yesuyo ndiye mwala wapakona wa mazikowo.+ 21 Mogwirizana ndi iye, nyumba yonse, pokhala yolumikizana bwino,+ ikukula kukhala kachisi woyera wa Yehova.+ 22 Mogwirizana ndi iye,+ inunso mukumangidwa pamodzi kukhala malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.+
3 Pa chifukwa chimenechi, ine Paulo, ndine wandende+ mwa Khristu Yesu m’malo mwa inu, anthu a mitundu ina+ . . . 2 Ndithudi munamva kuti ndinaikidwa kukhala woyang’anira+ kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kuti ndikuthandizeni, 3 ndiponso kuti anandiululira chinsinsi chopatulika,+ monga ndalemba kale mwachidule. 4 Pa chifukwa chimenechi, inuyo mukawerenga zimenezi mutha kuzindikira kuti chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu ndikuchimvetsa bwino.+ 5 M’mibadwo ina, chinsinsi+ chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene chaululidwira+ tsopano kwa atumwi ndi aneneri+ ake oyera mwa mzimu. 6 Chinsinsi chimenechi n’chakuti anthu a mitundu ina nawonso akhale odzalandira cholowa, ndipo akhalenso ziwalo za thupi+ ndiponso otenga nawo mbali m’lonjezo pamodzi ndi ife,+ mogwirizana ndi Khristu Yesu kudzera mwa uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki+ wa zimenezi mogwirizana ndi mphatso yaulere ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene ndinapatsidwa mogwirizana ndi mmene mphamvu yake imagwirira ntchito.+
8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunapatsidwa kwa ine, munthu wochepa pondiyerekeza ndi wochepetsetsa+ wa oyera onse. Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa mitundu ina+ uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera+ cha Khristu, 9 ndiponso kuti ndionetse anthu mmene chinsinsi chopatulikacho+ chikuyendetsedwera.+ Kuyambira kalekale, chinsinsi chimenechi chakhala chobisika mwa —Mulungu, amene analenga zinthu zonse.+ 10 Zinakhala choncho kuti maboma ndi maulamuliro+ amene ali m’malo akumwamba adziwe tsopano mbali zambirimbiri za nzeru ya Mulungu+ kudzera mwa mpingo.+ 11 Izi n’zogwirizana ndi cholinga chamuyaya chimene iye anakhala nacho chokhudza Khristuyo,+ yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula ndiponso njira yofikira Mulungu+ popanda kukayikira pokhala ndi chikhulupiriro mwa Yesuyo. 13 N’chifukwa chake ndikukupemphani kuti musabwerere m’mbuyo poona masautso+ angawa, amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu, pakuti akutanthauza ulemerero kwa inu.
14 Pa chifukwa chimenechi ndikupinda mawondo+ anga kwa Atate,+ 15 amene amapangitsa banja lililonse,+ kumwamba ndi padziko lapansi, kukhala ndi dzina.+ 16 Kutinso mogwirizana ndi chuma+ cha ulemerero wake, akuloleni kuti munthu wanu wamkati+ akhale wamphamvu, mwa mphamvu ya mzimu wake,+ 17 komanso kuti mwa chikhulupiriro chanu, Khristu akhale m’mitima yanu, pamodzi ndi chikondi+ chimene chiyenera kukhala pakati panu, ndiponso kuti muzike mizu+ ndi kukhala okhazikika pamaziko.+ 18 Cholinga n’chakuti, inu pamodzi ndi oyera onse muthe kudziwa bwino+ m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama,+ 19 ndiponso kuti mudziwe chikondi cha Khristu+ chimene chimaposa kudziwa zinthu zonse, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse+ amene Mulungu amapereka.
20 Tsopano kwa iye amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,+ malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito+ mwa ife, 21 kwa iye kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo ndi mwa Khristu Yesu, ku mibadwo yonse kwamuyaya.+ Ame.
4 Chotero ine, amene ndili m’ndende+ chifukwa cha Ambuye, ndikukuchondererani kuti muziyenda moyenera+ kuitana kumene munaitanidwa nako.+ 2 Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse,+ mofatsa, moleza mtima,+ ndiponso mololerana m’chikondi.+ 3 Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.+ 4 Pali thupi limodzi+ ndi mzimu umodzi,+ mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi+ chimene munaitanidwira. 5 Palinso Ambuye mmodzi,+ chikhulupiriro chimodzi,+ ubatizo umodzi,+ 6 ndi Mulungu mmodzi+ amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse ndipo amachita zinthu kudzera mwa onse ndiponso mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse.
7 Tsopano aliyense wa ife anapatsidwa kukoma mtima kwakukulu+ malinga ndi mmene Khristu anamuyezera mphatso yaulereyi.+ 8 Chotero iye anati: “Atakwera kumwamba anagwira anthu ukapolo ndipo anapereka mphatso za amuna.”+ 9 Tsopano, kodi mawu akuti “anakwera kumwamba”+ amatanthauza chiyani? Amatanthauza kuti anayamba watsika pansi, padziko.+ 10 Amene anatsikayo ndi amenenso anakwera+ kukakhala pamwambamwamba pa kumwamba konse,+ kuti adzazitse+ zinthu zonse.
11 Ndipo anapereka ena monga atumwi,+ ena monga aneneri,+ ena monga alaliki,*+ ena monga abusa ndi aphunzitsi,+ 12 kuti awongolere oyerawo,+ achite ntchito yotumikira, amange thupi la Khristu,+ 13 kufikira tonse tidzafike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira tidzakhale munthu wachikulire,+ wofika pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.+ 14 Inde, kuti tisakhalenso tiana, otengekatengeka+ ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso+ chonyenga+ cha anthu, mwa kuchenjera kwa anthu popeka mabodza. 15 Koma polankhula zoona,+ tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi,+ pansi pa iye amene ndi mutu,+ Khristu. 16 Kuchokera kwa iye, thupi lonselo+ limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.+
17 Choncho, ndikunena izi ndi kuzichitira umboni mwa Ambuye, kuti musamayendenso monga mmene anthu a mitundu ina+ amayendera, potsatira maganizo awo opanda pake.+ 18 Pamene akuyenda motero, alinso mu mdima wa maganizo,+ otalikirana+ ndi moyo wa Mulungu, chifukwa cha umbuli+ umene uli mwa iwo, chifukwanso cha kukakala+ kwa mitima yawo. 19 Popeza iwo tsopano sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino,+ anadzipereka okha ku khalidwe lotayirira+ kuti achite chonyansa+ chamtundu uliwonse mwadyera.+
20 Koma inu simunaphunzire Khristu kukhala wotero,+ 21 malinga ngati munamumvadi. Ndiponso, monga mmene choonadi+ chilili mwa Yesu, munaphunzitsidwa mwa iye,+ 22 kuti muvule umunthu wakale+ umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa+ malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo.+ 23 Ndipo munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu,+ 24 ndi kuvala+ umunthu watsopano+ umene unalengedwa+ mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni+ ndi pa kukhulupirika.
25 Chotero, popeza tsopano mwataya chinyengo,+ aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnzake,+ chifukwa ndife ziwalo za thupi limodzi.+ 26 Kwiyani, koma musachimwe.+ Dzuwa lisalowe muli chikwiyire,+ 27 ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.+ 28 Wakubayo asabenso,+ koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino,+ kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.+ 29 Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu,+ koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.+ 30 Komanso, musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu,+ umene mwaikidwa chidindo chake,+ cha pa tsiku limene mudzamasulidwa ndi dipo.+
31 Kuwawidwa mtima konse kwa njiru,+ kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe+ zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.+ 32 Koma khalani okomerana mtima,+ achifundo chachikulu,+ okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.+
5 Chotero muzitsanzira Mulungu,+ monga ana ake okondedwa, 2 ndipo yendanibe m’chikondi,+ monganso Khristu anakukondani+ n’kudzipereka yekha chifukwa cha inu. Iye anadzipereka yekha monga chopereka+ ndiponso monga nsembe yafungo lokoma kwa Mulungu.+
3 Dama*+ ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo+ zisatchulidwe n’komwe pakati panu,+ monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira.+ 4 Musatchule ngakhale za khalidwe lochititsa manyazi,+ nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana,+ zomwe ndi zinthu zosayenera. M’malomwake, muziyamika Mulungu.+ 5 Pakuti mfundo iyi mukuidziwa, ndipo mukuimvetsa bwino, kuti wadama+ kapena wodetsedwa kapena waumbombo,+ umene ndiwo kupembedza mafano, sadzalowa mu ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.+
6 Munthu asakupusitseni ndi mawu opanda pake,+ pakuti mkwiyo wa Mulungu udzafika pa ana a kusamvera, ochita zinthu zimene ndatchulazi.+ 7 Choncho musachite nawo zimenezo.+ 8 Pakuti poyamba munali mdima,+ koma tsopano ndinu kuwala+ mogwirizana ndi Ambuye. Yendanibe ngati ana a kuwala. 9 Pakuti zipatso za kuwala ndizo chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.+ 10 Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka+ kwa Ambuye n’chiti, 11 ndipo musamachite nawo+ ntchito zosapindulitsa za mu mdima.+ M’malomwake, muzidzudzula ntchitozo.+ 12 Pakuti zimene iwo amachita mseri n’zochititsa manyazi ngakhale kuzitchula.+ 13 Tsopano zinthu zimene zikudzudzulidwa+ zimaonekera poyera chifukwa cha kuwala, pakuti chilichonse chimene chaonekera+ chimakhala kuwala. 14 N’chifukwa chake iye akunena kuti: “Dzuka,+ wogona iwe! Uka kwa akufa,+ ndipo Khristu adzakuunika.”+
15 Choncho samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera+ si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. 16 Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu*+ chifukwa masikuwa ndi oipa.+ 17 Pa chifukwa chimenechi, lekani kukhala opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira+ chifuniro+ cha Yehova. 18 Ndiponso, musamaledzere naye vinyo,+ mmene muli makhalidwe oipa,+ koma khalanibe odzaza ndi mzimu.+ 19 Mukakhala pakati panu muziimba masalimo,+ nyimbo zotamanda+ Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba+ nyimbo zotamanda+ Yehova m’mitima mwanu, 20 m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. Nthawi zonse muziyamika+ Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse.
21 Gonjeranani+ poopa Khristu. 22 Akazi agonjere+ amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye, 23 chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake+ monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo,+ pokhala mpulumutsi wa thupilo. 24 Ndipotu, monga mmene mpingo umagonjerera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse.+ 25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 ndipo anauyeretsa+ pousambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.+ 27 Anatero kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero,+ wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zotero, koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.+
28 Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29 pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda,+ mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo, 30 chifukwa ndife ziwalo za thupi lake.+ 31 “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 32 Chinsinsi chopatulika+ chimenechi n’chachikulu. Tsopano ndikulankhula za Khristu ndi mpingo.+ 33 Komabe, aliyense wa inu akonde mkazi wake+ ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri+ mwamuna wake.
6 Ananu, muzimvera makolo anu+ mwa+ Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo.+ 2 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,”+ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo:+ 3 “Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.”+ 4 Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma muwalere+ m’malangizo*+ a Yehova* ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe+ kake.
5 Akapolo inu, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu.+ Muziwaopa ndi kuwalemekeza+ moona mtima, monga mmene mumachitira ndi Khristu. 6 Osati mwachiphamaso ngati ofuna kukondweretsa anthu,+ koma monga akapolo a Khristu, ochita chifuniro cha Mulungu ndi moyo wonse.+ 7 Khalani akapolo amaganizo abwino, monga otumikira Yehova+ osati anthu, 8 pakuti mukudziwa kuti chabwino chilichonse chimene wina aliyense angachite adzachilandiranso kwa Yehova,+ kaya munthuyo akhale kapolo kapena mfulu.+ 9 Inu ambuye, muzichitiranso akapolo anu chimodzimodzi ndipo muleke kuwaopseza,+ pakuti mukudziwa kuti Ambuye wa nonsenu, wa iwowo ndi wa inuyo,+ ali kumwamba ndipo alibe tsankho.+
10 Potsiriza ndikuti, pitirizani kupeza mphamvu+ kuchokera kwa Ambuye ndiponso kuchokera ku mphamvu+ zake zazikulu. 11 Valani zida zonse zankhondo+ zochokera kwa Mulungu kuti musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo+ za Mdyerekezi, 12 chifukwa sitikulimbana+ ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma,+ maulamuliro,+ olamulira dziko+ a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa+ m’malo akumwamba. 13 Pa chifukwa chimenechi, nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu+ kuti musadzagonje m’tsiku loipa, ndipo mutachita zonse bwinobwino, mudzathe kulimba.+
14 Chotero khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi+ m’chiuno mwanu,+ mutavalanso chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,+ 15 mapazi+ anu mutawaveka nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere.+ 16 Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro,+ chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto+ ya woipayo. 17 Komanso landirani chisoti cholimba+ chachipulumutso, ndiponso lupanga+ la mzimu,+ lomwe ndilo mawu a Mulungu.+ 18 Pamene mukutero, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu,+ mwa mtundu uliwonse wa pemphero+ ndi pembedzero. Kuti muchite zimenezi, khalani maso mosalekeza ndi kupemphera mopembedzera m’malo mwa oyera onse, 19 kuphatikizapo ineyo. Chitani zimenezi kuti ndikatsegula pakamwa panga kuti ndilankhule, ndizitha kulankhula+ mwaufulu+ kuti ndidziwitse ena chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino,+ 20 umene ndili kazembe+ wake womangidwa ndi unyolo, ndiponso kuti ndilankhule za uthengawo molimba mtima monga mmene ndiyenera kuchitira.+
21 Tsopano, kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanga ndi mmene ine ndilili, Tukiko,+ m’bale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakufotokozerani zonse.+ 22 Ndamutumiza kwa inu ndi cholinga chimenechi, kuti mudziwe mmene zinthu zilili kwa ife ndi kuti atonthoze mitima yanu.+
23 Mtendere ndi chikondi ndiponso chikhulupiriro zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale pa abalenu. 24 Kukoma mtima kwakukulu+ kukhale pa onse amene ali ndi chikondi chenicheni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 9.
“Alaliki” palembali akutanthauza “amishonale.”
Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “muzigula nthawi yoikidwa.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Zakumapeto 2.