Chivumbulutso
9 Kenako mngelo wachisanu analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinaona nyenyezi+ imene inagwera kudziko lapansi kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi+ wa dzenje+ lolowera kuphompho. 2 Pamene inatsegula dzenje lolowera kuphompholo, utsi+ ngati wa m’ng’anjo yaikulu+ unatuluka m’dzenjemo, ndipo dzuwa ndi mpweya zinada+ ndi utsi wa m’dzenjewo. 3 Mu utsiwo, munatuluka dzombe+ n’kubwera padziko lapansi. Dzombelo linapatsidwa ulamuliro wofanana ndi umene zinkhanira+ za padziko lapansi zili nawo. 4 Ndipo linauzidwa kuti lisawononge zomera za padziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma livulaze anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.+
5 Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze+ miyezi isanu. Ndipo kuzunzika kwawo kunali kofanana ndi mmene munthu amazunzikira akalumidwa ndi chinkhanira.+ 6 M’masiku amenewo, anthuwo adzafunafuna imfa,+ koma sadzaipeza. Adzalakalaka kufa, koma imfa izidzawathawa.
7 Dzombelo linali kuoneka ngati mahatchi+ okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali zinthu zooneka ngati zisoti zachifumu zokhala ngati zagolide. Nkhope zawo zinali ngati nkhope za amuna,+ 8 koma tsitsi lawo linali ngati la akazi.+ Mano awo anali ngati a mikango.+ 9 Pachifuwa pawo panali zotetezera+ zokhala ngati zachitsulo. Ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta+ okokedwa ndi mahatchi ambiri omwe akuthamangira kunkhondo.+ 10 Dzombelo linali ndi michira ndi mbola ngati zinkhanira.+ M’michira yawoyo ndi mmene munali ulamuliro wawo wovulaza anthuwo kwa miyezi isanu. 11 Dzombelo lili ndi mfumu. Mfumuyo ndiye mngelo wa phompho.+ M’Chiheberi, dzina lake ndi Abadoni, koma m’Chigiriki ali ndi dzina lakuti Apoliyoni.+
12 Tsoka limodzilo linapita. Koma masoka ena awiri+ anali kubwera pambuyo pa zimenezi.
13 Kenako mngelo wa 6+ analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinamva mawu amodzi+ kuchokera panyanga za paguwa lansembe lagolide+ lokhala pamaso pa Mulungu. 14 Mawuwo anauza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: “Masula angelo anayi+ omangidwa+ amene ali kumtsinje waukulu wa Firate.”+ 15 Angelo anayiwo anamasulidwa. Iwo anali okonzekera kuti pa ola, tsiku, mwezi, ndi chaka chimenecho, aphe gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.
16 Ndipo chiwerengero cha makamu a asilikali okwera pamahatchi, chinali miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda.* Chimenechi ndicho chiwerengero chawo chimene ndinamva. 17 Mahatchi ndi okwerapowo ndinawaona motere m’masomphenyawo: Anavala zoteteza pachifuwa zofiira ngati moto, zobiriwira ngati mwala wa huwakinto, ndi zachikasu ngati sulufule. Mitu ya mahatchiwo inali ngati mitu ya mikango,+ ndipo m’kamwa mwawo munali kutuluka moto, utsi, ndi sulufule.+ 18 M’kamwa mwawomo munalinso kutuluka miliri itatu iyi: Moto, utsi, ndi sulufule, ndipo inapha gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu. 19 Ulamuliro wa mahatchiwo unali m’kamwa mwawo ndi m’michira yawo, pakuti michira yawo inali ngati njoka,+ ndipo inali ndi mitu. Zinthu zimenezi anali kuwononga nazo anthu.
20 Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo.+ Sanalape kulambira ziwanda+ ndi mafano agolide, asiliva,+ amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+ 21 Iwo sanalape ntchito zawo zopha anthu,+ zamizimu,+ dama lawo, ngakhalenso umbava wawo.